-
Rute 1:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
1 Tsopano, pa nthawi imene oweruza+ ankatsogolera* ku Isiraeli, mʼdzikomo munagwa njala. Ndiyeno munthu wina anasamuka ku Betelehemu+ wa ku Yuda nʼkukakhala ngati mlendo ku Mowabu.+ Anasamuka ndi mkazi wake ndi ana ake awiri aamuna. 2 Munthuyu dzina lake anali Elimeleki,* ndipo mkazi wake anali Naomi.* Mayina a ana akewo anali Maloni* ndi Kiliyoni.* Anthuwa anali a ku Betelehemu Efurata wa ku Yuda. Ndipo anafika ku Mowabu nʼkumakhala kumeneko.
-