2 Samueli 7:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Tsopano mtumiki wanga Davide ukamuuze kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Ine ndinakutenga kubusa kumene unkaweta nkhosa+ kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga.+ 2 Samueli 7:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Ukadzamwalira+ nʼkugona mʼmanda ndi makolo ako, ndidzachititsa kuti mbadwa* yako, mwana wako weniweni, akhale mfumu ndipo ndidzachititsa kuti ufumu wake ukhazikike.+ 1 Mafumu 2:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Komanso Yehova adzakwaniritsa zimene analonjeza zokhudza ineyo zakuti: ‘Ana ako akamadzachita zinthu mosamala komanso kuyenda mokhulupirika* pamaso panga ndi mtima wawo wonse ndi moyo wawo wonse,+ anthu a mʼbanja lako adzapitiriza kukhala pampando wachifumu wa Isiraeli.’+ 1 Mafumu 9:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 ndidzakhazikitsa mpando wako wachifumu mu Isiraeli mpaka kalekale, ngati mmene ndinalonjezera bambo ako Davide kuti, ‘Munthu wa mʼbanja lako sadzachoka pampando wachifumu wa Isiraeli.’+ Salimo 89:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Ndapeza Davide mtumiki wanga,+Ndipo ndamudzoza ndi mafuta anga opatulika.+ Salimo 89:29 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 29 Ndidzachititsa kuti mbadwa* zake zidzakhalepo kwamuyaya,Ndipo ndidzachititsa kuti mpando wake wachifumu udzakhalepo mpaka kalekale ngati kumwamba.+
8 Tsopano mtumiki wanga Davide ukamuuze kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Ine ndinakutenga kubusa kumene unkaweta nkhosa+ kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga.+
12 Ukadzamwalira+ nʼkugona mʼmanda ndi makolo ako, ndidzachititsa kuti mbadwa* yako, mwana wako weniweni, akhale mfumu ndipo ndidzachititsa kuti ufumu wake ukhazikike.+
4 Komanso Yehova adzakwaniritsa zimene analonjeza zokhudza ineyo zakuti: ‘Ana ako akamadzachita zinthu mosamala komanso kuyenda mokhulupirika* pamaso panga ndi mtima wawo wonse ndi moyo wawo wonse,+ anthu a mʼbanja lako adzapitiriza kukhala pampando wachifumu wa Isiraeli.’+
5 ndidzakhazikitsa mpando wako wachifumu mu Isiraeli mpaka kalekale, ngati mmene ndinalonjezera bambo ako Davide kuti, ‘Munthu wa mʼbanja lako sadzachoka pampando wachifumu wa Isiraeli.’+
29 Ndidzachititsa kuti mbadwa* zake zidzakhalepo kwamuyaya,Ndipo ndidzachititsa kuti mpando wake wachifumu udzakhalepo mpaka kalekale ngati kumwamba.+