33 Adzangodzivulaza yekha ndipo anthu adzamunyoza,+
Moti kunyozeka kwake sikudzafufutika.+
34 Chifukwa nsanje imachititsa kuti mwamuna wake akwiye kwambiri.
Pomubwezera sadzamva chisoni.+
35 Iye sadzavomera chipukuta misozi chilichonse,
Ndipo sadzapepeseka ngakhale utapereka mphatso yaikulu bwanji.