-
Mateyu 2:4-6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Choncho Herode anasonkhanitsa ansembe aakulu ndi alembi onse a anthu, ndipo anawafunsa za kumene Khristu* adzabadwire. 5 Iwo anamuyankha kuti: “Adzabadwira ku Betelehemu+ wa ku Yudeya, chifukwa mneneri analemba zimenezi kuti: 6 ‘Iwe Betelehemu wamʼdziko la Yuda, si iwe mzinda waungʼono kwambiri kwa olamulira a Yuda, chifukwa mwa iwe mudzatuluka wolamulira amene azidzaweta anthu anga, Aisiraeli.’”+
-