-
Aroma 2:28, 29Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
28 Amene ali Myuda kunja kokha si Myuda,+ ndiponso mdulidwe wakunja kokha wochitidwa pathupi, si mdulidwe.+ 29 Kukhala Myuda weniweni kuli mumtima+ ndipo mdulidwe wake umakhalanso wamumtima+ wochitidwa ndi mzimu, osati ndi malamulo olembedwa.+ Munthu woteroyo amatamandidwa ndi Mulungu, osati anthu.+
-
-
1 Akorinto 7:18-20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Kodi pali mwamuna amene anaitanidwa ali wodulidwa?+ Akhalebe wodulidwa. Nanga alipo amene anaitanidwa ali wosadulidwa? Asadulidwe.+ 19 Mdulidwe sutanthauza chilichonse ndipo kusadulidwa sikutanthauzanso chilichonse,+ koma chofunika nʼkusunga malamulo a Mulungu.+ 20 Aliyense akhalebe mmene analili pamene ankaitanidwa.+
-