-
Deuteronomo 9:5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Sikuti mukulowa mʼdzikoli kukalitenga kukhala lanu chifukwa choti ndinu olungama kapena chifukwa choti ndinu owongoka mtima. Koma Yehova Mulungu wanu akuthamangitsira mitundu imeneyi kutali ndi inu,+ chifukwa choti ndi yoipa, ndiponso kuti Yehova akwaniritse mawu onse amene analumbirira makolo anu Abulahamu,+ Isaki+ ndi Yakobo.+
-
-
Agalatiya 3:21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Ndiye kodi Chilamulo chimatsutsa malonjezo a Mulungu? Ayi ndithu. Chifukwa pakanaperekedwa lamulo lopatsa moyo, bwenzi tikuonedwa kuti ndife olungama chifukwa chotsatira chilamulo.
-