Zipwirikiti Zandale Zimene Zikukwaniritsa Ulosi wa M’Baibulo
Masiku ano anthu ndi ogawikana kwambiri pankhani zandale. Sagwirizana pa nkhani zokhudza malamulo ofunika kwambiri pa moyo wawo ndipo amatsutsana mwamphamvu pa nkhani zimenezi. Kawirikawiri pamakhala kusagwirizana pakati pa anthu amene amapanga malamulo m’boma ndi akuluakulu ena aboma moti palibe amene amafuna kugonjera zonena za mnzake. Kusamvana kotereku n’kumene kumayambitsa zipwirikiti pa ndale zomwe zingapangitse kuti ntchito za boma zisamayende bwino.
Koma zipwirikiti zimene zikuchitika ku United States komanso ku Britain (dziko limene limadziwikanso kuti United Kingdom), n’zochititsa chidwi kwambiri. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti Baibulo linaneneratu kuti zipwirikiti zoterezi zidzachitika m’mayiko awiriwa ndipo pa nthawi imeneyi, boma la Mulungu lidzalowererapo n’kusintha chilichonse padzikoli.
Zipwirikiti zimene zikuchitika “mʼmasiku otsiriza” ano
M’Baibulo muli ulosi wochititsa chidwi womwe ukupezeka m’buku la Danieli. Mu ulosi umenewu, Mulungu ananeneratu “zimene zidzachitike mʼmasiku otsiriza.” Pamene Danieli ankalemba ulosiwu, ankalemba zimene zidzachitike m’tsogolo zomwe zidzakhudze kwambiri zochitika pa moyo wa anthu.—Danieli 2:28.
Mulungu anapereka ulosi umenewu kudzera m’maloto amene anaonetsa mfumu ya Babulo. M’malotowo mfumuyo inaona chifaniziro chachikulu chimene chinapangidwa ndi zitsulo zosiyanasiyana. Ndiyeno mneneri Danieli anafotokoza kuti kuchokera kumutu kukafika kumapazi, chifanizirocho chikuimira maulamuliro amphamvu padziko lonse omwe adzalamulire pa nthawi zosiyanasiyana kenako n’kutha.a Pamapeto pake chifanizirocho chidzawonongedwa ndi mwala umene ukuimira Ufumu kapena kuti boma lokhazikitsidwa ndi Mulungu.—Danieli 2:36-45.
Mogwirizana ndi zimene ulosiwu ukunena, Ufumu wa Mulungu udzalowa m’malo mwa maboma onse a anthu. Ndi Ufumu womwewu umene Yesu anauza ophunzira ake kuti aziupempherera. Iye anawaphunzitsa kuti azipemphera kuti: “Ufumu wanu ubwere.”—Mateyu 6:10.
Koma kodi ndi pati pamene ulosi wa m’Baibulowu umanena kuti m’dzikoli mudzakhala zipwirikiti pa ndale? Onani kuti mapazi a chifanizirochi “anali achitsulo chosakanikirana ndi dongo.” (Danieli 2:33) Mbali zina za chifanizirochi zinali zosiyana ndi mapazi a chitsulo chosakanikirana ndi dongowa chifukwa chakuti mbali zinazo zinali ndi chitsulo cha mtundu umodzi okha. Zimenezi zinasonyeza kuti padzakhala ulamuliro wina wamphamvu padziko lonse, umene udzakhale wosiyana ndi maulamuliro ena onsewo. Udzasiyana bwanji? Ulosi wa Danieli ukufotokoza kuti:
Mogwirizana ndi zimene ulosiwu ukunena, mu ulamuliro wamphamvu padziko lonse, umene ukuimiriridwa ndi mapazi a chifanizirochi, mudzakhala zipwirikiti pa ndale. Mphamvu zake zidzachepa ndipo anthu am’dziko momwemo ndi amene adzachititse zimenezi.
Ulosi wa Danieliwu ukukwaniritsidwa panopa
Mapazi a chifanizirochi akuimira ulamuliro wamphamvu padziko lonse umene ukulamulira panopa, womwe ndi mgwirizano wa United States ndi Britain. Kodi zimene zikuchitika m’dzikoli masiku ano zikutsimikizira bwanji mfundo imeneyi?
Mapazi a chifaniziro chija ndi ‘achitsulo chosakanikirana ndi dongo,’ zimene zikupangitsa kuti mapaziwo akhale osalimba. (Danieli 2:42) Masiku ano mphamvu za dziko la United States komanso la Britain zachepa chifukwa cha kugawikana kwa anthu m’mayikowa. Mwachitsanzo, magulu a anthu m’mayiko onsewa akungokhalira kukangana. Komanso anthu akuchita ziwonetsero ndiponso ziwawa pomenyera ufulu wawo. Kawirikawiri atsogoleri amene anawasankha m’maudindo osiyanasiyana sagwirizana pa zinthu zambiri. Popeza kuti anthu awo ndi ogawanika choncho, nthawi zina maboma onsewa amalephera kuchita zinthu zimene amafunika kuchita.
Chaputala 2 cha buku la Danieli chinaneneratu za maulamuliro amenewa
Tiyeni tikambiranenso matanthauzo a mfundo zina za mu ulosi wa Danieli komanso mmene zikukwaniritsidwira masiku ano:
Ulosi: “Ufumuwo udzakhala wogawanika. Koma udzakhala wolimba pa zinthu zina ngati chitsulo.”—Danieli 2:41.
Tanthauzo Lake: Ngakhale kuti anthu m’mayiko a United States komanso Britain ndi ogawikana pa nkhani zandale, mayikowa ali ndi magulu ankhondo amphamvu kwambiri. Chifukwa cha zimenezi ali ndi mphamvu pa zochitika zapadziko lonse, ndipo mphamvu zawo ndi zofanana ndi za chitsulo.
Kukwaniritsidwa Kwake
M’chaka cha 2023, mayiko a United States ndi United Kingdom kuwaphatikiza pamodzi, anagwiritsa ntchito ndalama zambiri pa zinthu zokhudzana ndi nkhondo tikayerekezera ndi zimene mayiko ena 12 kuwaphatikiza pamodzi anagwiritsa ntchito.—Stockholm International Peace Research Institute.
“Mgwirizano wa dziko la United Kingdom ndi la United States womwe cholinga chake ndi kuteteza mayiko athu . . . ndi wamphamvu kwambiri kuposa mgwirizano wa mayiko awiri aliwonse. Tikugwiritsa ntchito luso komanso mfundo zamakono . . . Timagwira ntchito limodzi, timathandizana komanso timamenya nkhondo limodzi.”—Strategic Command, U.K. Ministry of Defence, April 2024.
Ulosi: “Popeza zala zakumiyendo zinali zachitsulo chosakanikirana ndi dongo, pa zinthu zina ufumuwo udzakhala wolimba koma pa zinthu zina udzakhala wosalimba.”—Danieli 2:42.
Tanthauzo Lake: Ngakhale kuti mayiko a United States ndi United Kingdom ali ndi magulu ankhondo amphamvu kwambiri, amalephera kuchita zinthu zina zimene akanafuna chifukwa cha mmene maboma awo, omwe ndi ademokalase, amachitira zinthu. Ngati anthu ambiri sanavomereze zimene mabomawa akufuna kuchita, nthawi zina zimavuta kuti akwaniritse zolinga zawo.
Kukwaniritsidwa Kwake
“Akatswiri ena ounika mmene ndale zikuyendera akunena kuti kugawikana pa ndale kumene kukuchitika ku America, kukulepheretsa dziko la United States kuchita zimene limauza dziko lonse kuti lingathe kuchita pa nkhani ya chitetezo kapena malonda.”—“The Wall Street Journal.”
“Panopa ku Britain kuli mavuto ambiri okhudzana ndi ndale amene sanakhalepo chiyambire, ndipo asokoneza kwambiri atsogoleri andale. Zimenezi zikulepheretsa ogwira ntchito m’boma kusintha zinthu n’cholinga chothandiza nzika zawo.”—Institute for Government.
Ulosi: “Mbali zake zina [za ufumuwo] zidzasakanikirana ndi anthu koma sadzagwirizana.”—Danieli 2:43.
Tanthauzo Lake: M’maboma a demokalase, anthu wamba amatha kuuza maboma awo zoti achite. Koma zotsatira zake sizisangalatsa akuluakulu aboma kapena anthu amene anawavotera.
Kukwaniritsidwa Kwake
“Masiku ano, anthu ambiri a ku America sakusangalala ndi andale komanso mmene zinthu zikuyendera pa ndale.”—Pew Research Center.
“Masiku ano, anthu a ku Britain sakukhulupiriranso kwenikweni boma lawo komanso andale ngati mmene ankachitira zaka 50 zapitazo.”—“National Centre for Social Research.”
Mmene ulosi wa Danieli udzakwaniritsidwire m’tsogolo
Mogwirizana ndi ulosi wa Danieli, mgwirizano wa dziko la United States ndi la Britain udzakhala ulamuliro wamphamvu padziko lonse pamene Ufumu wa Mulungu uzidzalowa m’malo maboma onse a anthu.—Danieli 2:44.
Mu ulosi wina wofanana ndi umenewu, womwe ukupezeka m’buku la Chivumbulutso, Baibulo limasonyeza kuti “mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu” adzasonkhanitsidwa pamodzi kuti alimbane ndi Yehovab Mulungu pa nkhondo ya Aramagedo, yomwe ndi ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.’ (Chivumbulutso 16:14, 16; 19:19-21) Pa nkhondo imeneyi, Yehova adzawononga maboma onse a anthu. Zimenezi zikadzachitika, ndiye kuti maulamuliro onse amphamvu padziko lonse, amene akuimiridwa ndi fano la mu ulosi wa Danieli lija, adzathera pomwepo.
Kuti mumve zambiri, onani nkhani yakuti “Kodi Nkhondo ya Aramagedo Idzakhala Yotani?”
Phunzirani ulosi wa Danieli wonena za zipwirikiti pa ndale kuti mupeze mfundo zothandiza
Baibulo linaneneratu molondola zokhudza zipwirikiti pa ndale zimene zikuchitika ku United States ndi ku Britain. Choncho kuphunzira zimene linanenazo kukuthandizani kuti muziona zimene zikuchitika masiku ano mosiyana ndi mmene mumazionera poyamba.
Mumvetsa chifukwa chake Yesu anauza otsatira ake kuti asamalowerere ndale zam’dzikoli. (Yohane 17:16) Mumvetsanso chifukwa chake Yesu, amene Mulungu anamusankha kuti akhale wolamulira mu Ufumu wake, ananena kuti: “Ufumu wanga si wochokera mʼdzikoli.”—Yohane 18:36.
Mulimbikitsidwa ndi mfundo yakuti posachedwapa Ufumu wa Mulungu usintha zinthu padzikoli ndipo ubweretsa madalitso mogwirizana ndi zimene Mulungu analonjeza.—Chivumbulutso 21:3, 4.
Mukhala ndi chiyembekezo kuti zinthu zikhala bwino m’tsogolomu ndipo simuzidanso nkhawa kuti mayiko amene akukanganawa awononga dzikoli.—Salimo 37:11, 29.
Ulosi wa Danieli ukusonyeza kuti mgwirizano wa United States ndi Britain, womwe ukuimiridwa ndi mapazi a chifaniziro, ndi ulamuliro womaliza wa anthu kulamulira dziko lonse. Ulamuliro umenewu ukachoka, pabwera ulamuliro wabwino kwambiri. Ulamuliro wake ndi Ufumu wa Mulungu womwe ukulamulira uli kumwamba.
Kuti mumve zambiri zimene Ufumu wa Mulungu udzachitire anthu, onerani vidiyo yakuti Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
a Onani bokosi lakuti “Kodi Ulosi wa Danieli Ukunena za Maulamuliro Ati Amphamvu Padziko Lonse?”
b Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu. (Salimo 83:18) Onani nkhani yakuti “Kodi Yehova Ndi Ndani?”