Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 5/1 tsamba 10-14
  • Njala Yopatsa Imfa mu Nthawi ya Mwana Alilenji

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Njala Yopatsa Imfa mu Nthawi ya Mwana Alilenji
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Njala Yopatsa Imfa
  • Ndimotani Mmene Iriri Nthawi ya Mwana Alilenji?
  • Yosefe, Msungi wa Moyo
  • Chitsanzo Chifutukuka
  • Yosefe mu Igupto
  • ‘Kodi Mulungu Sindiye Amamasulira Maloto?’
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Yehova Sanamuiwale Yosefe
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Kupulumutsa Moyo mu Nthawi ya Njala
    Nsanja ya Olonda—1987
  • “Sadzamvanso Njala”
    Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 5/1 tsamba 10-14

Njala Yopatsa Imfa mu Nthawi ya Mwana Alilenji

“Atumiki anga adzadya, koma inu mudzakhala ndi njala.”​—YESAYA 65:13.

1, 2. (a) Kodi ndi vuto lotani limene mitundu imalimbana nalo kopanda phindu? (b) Ndi ku chiyembekezo chenicheni chiti kumene Baibulo limaloza?

MZIMU wanjala uli padziko lonse lapansi! Kuchitira ndemanga pa kuipitsitsa, bungwe lolemba mu The Boston Globe linanena kuti: “Dziko lokhala ndi chifupifupi anthu biliyoni omwe ali pafupi kufa ndi njala liyenera kupeza njira zothandizira mitundu yosauka kwambiri kusangalala ndi chuma chake kufikira zokolola zochuluka zopezedwa ndi mitundu yolemera koposa.” Komabe, ngakhale mitundu yopita patsogolo mu zochitachita, monga mmene kunganenedwere, singadzinenere kukhala yopatulidwa kotheratu ku kuperewera kwa chakudya. Iyinso yalephera kupanga programu yotsimikizirikakuti nzika zawo zonse zidzadyetsedwa. Yokhudzidwa ndikulimbanirana kwa umunthu ndi mavuto omakulakula. Kodi pali yankho?

2 Bungwe lolemba logwidwa mawu pamwambapo linavomereza: “Mbali yomvetsa chisoni koposa ya kudya mosakwanira . . . iri yakuti dziko liri ndi kuthekera kwakudyetsa aliyense.” Komabe muliri wa njala ndi kusowa kwa chakudya ukupitirizabe kupita patsogolo. Kodi nchifukwa ninji ichi chiyenera kukhala tero? Mlengi wathu wachikondi wapereka zokwanira kaamba ka mabiliyoni onse omakula a padziko lapansi. Mkukonzekera dziko lapansi monga nyumba ya munthu, iye analipanga iro kukhala lothekera kutulutsa mochuluka, zochuluka zoposa zimene ziri zoyenerera kaamba ka onse. (Masalmo 72: 16-19; 104:15, 16, 24) Ngakhale mu nthawi izi zovuta, tiri otsimikiziridwa kuti Mgawiri wathu Wamkulu adzapereka chakudya chokwanira kaamba ka awo amene akuyang’ana kumagwero abwino. Kupyolera mwa mmodzi amene iye anamukhazikitsa monga Woyang’anira Chakudya, wamkulu iye akutiuza ife: “Koma muthange mwafuna Ufumu wake [wa Mulungu] ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo [zosowa za kuthupi zoyenerera] zidzawonjezedwa kwa inu.”—Mateyu 6: 33; 1 Yohane 4:14.

Njala Yopatsa Imfa

3. Kodi ndi iti imene iri njala yowonekera kwambiri

3 Chowonekera kwambiri padziko lapansi lerolino iri njala yauzimu. Iyo iri mwachindunji yogwirizana ndi kusoweka kwa mtendere. Mtundu wa anthu ukudzandama mozungulira, kufufuzafufuza mopanda phindu kaamba ka njira yotulukira. Mulungu wamphamvuyonse anapangitsa mneneri wake kulemba ponena za mkhalidwe umenewu zaka mazana ambiri pasadakhale, akumati: “ ‘Tawonani! akudza masiku,’ ati Ambuye Yehova, ‘ndidzatumiza njala m’dzikomo, si njala ya mkate kapena ludzu la madzi, koma njala ya kumva mawu a Yehova. Ndipo adzayendayenda peyupeyu kuyambira kunyanja kufikira kunyanja ndi kuyambira kumpoto kufikira kum’mawa; adzathamangathamanga kufunafuna mawu a Yehova, koma osawapeza.’”​—Amosi 8:11, 12.

4, 5. (a) Kodi nchifukwa ninji ena samupeza Mulungu ngakhale kuti amafunafuna iye? (b) Kodi ndimotani mmene Yesu anasiyanirana ndi atsogoleri achipembedzo a mtsiku lake? (Mateyu 15:1-14)

4 Komabe, kodi pali njira yotulukira ku zinthu zosatheka kuzipyola zimenezi? Mtumwi Paulo akuyankha inde, kutilimbikitsa ife ndi mawu awa: “Mulungu amene analenga dziko lapansi . . . atapangiratu nyengo zawo, ndi malekezero a pokhala pawo; kuti afunefune Mulungu, kapena akamfufuze ndi kumpeza, ngakhale sakhala patali ndi yense wa ife.”​—Machitidwe 17:24-27.

5 Ngati Mulungu asali patali ndi aliyense wa ife,” nchifukwa ninji kuti ambiri amafufuzafufuza iye, koma sampeza? Chiri chifukwa chakuti iwo akufunafuna kaamba ka iye m’malo olakwika. Ndi angati a awo amene amadzitcha iwo eni kukhala Akristu mwaumwini amafikira bukhu lenileni lophunzitsira la Chikristu, Baibulo Loyera? Ndi angati otchedwa “abusa” amagwiritsira ntchito Mawu a Mulungu kuphunzitsa “nkhosa”? (Yerekezani Ezekieli 34: 10. ) Yesu anauuza atsogoleri achipembedzo onyada a mtsiku lake kuti iwo “sadziwa Malemba ngakhale mphamvu ya Mulungu.” (Mateyu 22:29; Yohane 5:44) Komabe, Yesu ponse pawiri anadziwa Malemba ndi kuphunzitsa iwo kwa anthu, kaambaa amene iye anamverera chisoni “popeza anali okambululudwa ndi omwazikana akunga nkhosa zopanda mbusa.”​—Mateyu9:36.

Ndimotani Mmene Iriri Nthawi ya Mwana Alilenji?

6. Ponena za mwana alilenji wauzimu, kodi ndimotani mmene Yehova amatsimikizira atumiki ake?

6 Yehova amatsimikizira ndi kulimbikitsa amene mofunitsitsa amafuna kumudziwa iye. Mkudzudzula abusa achipembedzo chonyenga, iye ananena kupyolera mwa mneneri wake Yesaya: “Taonani! atumiki anga adzadya, koma inu mudzakhala ndi njala. Taonani! atumiki anga adzamwa, koma inu mudzakhala ndi ludzu. Taonani! atumiki anga adzasangalala, koma inu mudzakhala ndi manyazi.” (Yesaya 65:13, 14) Kodi ndimotani mmene Mulungu amaperekera zochuluka kaamba ka atumiki ake okha? Kodi nchiyani chimene tiyenera kuchita kuti tigawane ndi chimwemwe mu zopereka zake. kaamba ka kusunga moyo, mosasamala kanthu za njala yauzimU ya lerolino?

7. Kodi ndi chitsanzo chamake dzana chachikondi chiti chimene chinaperekedwa kaamba ka chilimbikitso chathu lerolino?

7 Popeza chipulumuko chimadalira pa kudziwa kwathu kotheratu zifuno za Mulungu ndi kugwirira ntchito mu chikhulupiriro pa izo, ife mwachimwemwe tiyenera kupita ku Mawu a Mulungu, kufuna kudziwa chifuno chake kaamba ka ife ndi kumvetsetsa njira yake yakuchitira ndi ife. (Yohane 17:3) Kufika ku mlingo umenewo, tsopano tidzalingalira chitsanzo cha Baibulo chomwe .chimafanana ndi zimene zikuchitika lerolino. Munthu wowonekera kwambiri mu chitsanzo chimenechi liri kholo Yosefe. Pamene Yehova anapanga choperekedwa chanzeru kaamba ka anthu ake kudzera mwa Yosefe, chotero iye mwachikondi amatsogoza awo amene akumfunafuna iye lerolino.​—Yerekezani ndi Aroma 15:4; 1 Akorinto 10: 11, Reference Bible futunoti (*); Agalatiya 4:24.

Yosefe, Msungi wa Moyo

8, 9. (a) Kodi ndi kufanana kotani kumene timapeza mnthawi zino kaamba ka Yosefe ndi kaamba ka Yakobo ndi Farao? (b) Kodi ndimotani mmene ife eni tingaphatikizidwire mkukwaniritsidwa kwake?

8 Monga msungi wa moyo, Yosefe mwana wa Yakobo anachita mbali yowonekera kwambiri. Kodi chimenechi chimaimira chinthu china chake chodzachitika mnthawi yamtsogolo? Chabwino, talingalirani kupirira kwa Yosefe kukachitidwe kosayenera ka abale ake, kuchita nawo mayeso ndi mavuto mu dziko lachilendo, chikhulupiriro chake chosagwedezeka, kusunga umphUmphu kwake, ndi kukwezedwa ku malo a woyang’anira wanzeru mnthawi yangozi ya njala. (Genesis 39:1-3, 7-9; 41:38-41) Kodi sitikuwona kufanana mu njira ya moyo ya Yesu?

9 Kunali kupyolera mu nsautso kuti Yesu anakhala mkate wa moyo pakati pa dziko lomwe linali ndi njala “kaamba ka kumva mawu a Yehova.” (Amosi 8:11; Ahebri 5:8, 9; Yohane 6:35) Mu unansi wawo ndi Yosefe, onse awiri Yakobo ndi Farao amatikumbutsa ife za Yehova ndi zimene iye anakwaniritsa kupyolera mwa Mwana wake. (Yohane 3:17, 34; 20:17; Aroma 8:15, 16; Luka 4:18) Panali enanso omwe anagawana m’kuchita chitsanzo chamoyo weniweni chimenechi, ndipo tidzalingalira mbali zawo ndi chikondwerero. Ife mosakaikira tidzakumbutsidwa za kudalira kwathU pa Yosefe Wokulirapo, Kristu Yesu. Tiri oyamikira chotani nanga kuti iye amatipulumutsa ife kuchokera ku njala yopatsa imfa mkati mwanthawi zomaipaipazi “za masiku otsirizaP—2 Timoteo 3:1, 13.

Chitsanzo Chifutukuka

10. (a) Kodi ndimotani mmene Yosefe anakonzekeretsedwera kaamba ka thayo lomwe iye anayenera kulichita? (b) Kodi ndi mikhalidwe yotani imene iye anasonyeza m’moyo wake woyambirira?

10 M’tsiku la Yosefe, panalibe munthu wina aliyense akanadziwa pasanakhale zimene Yehova anasunga kaamba ka anthu ake. Koma pofika nthawi imene Yosefe anaitanidwa kukakwaniritsa mbali yake yofunika, Yehova anali atamphunzitsa kale ndi kumufikitsa iye ku ungwiro ponena za kuyenerera kwake. Mchigwirizano ndi moyo wake woyambirira, mbiriyo ikunena kuti: “Yosefe anali wa zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri anali nkudyetsa zoweta pamodzi ndi abale ake; ndipo anali anyamata pamodzi ndi ana a Biliha ndi ana amuna a Zilipa, akazi a atate, wake; ndipo Yosefe anafotokozera atate wake mbiri yawo yoipa.” (Genesis 37:2) Iye anasonyeza kumvera ku chikondwerero cha atate wake monga mmene Yesu anali mosagwedezeka womvera mkusamalira zoweta za atate wake pakati pa “mbadwo wosakhulupirika ndi wokhotakhota.”​—Mateyu 17:17, 22, 23.

11. (a) Kodi nchifukwa ninji abale opeza a Yosefe anayamba kumuda iye? (b) Kodi ndi mkhalidwe wofananawo wotani umene unakhudza Yesu?

11 Atate a Yosefe, Israyeli, anamukonda iye koposa abale ake ndi kumuyanja iye mwakukhala ndi chovala chachitali, cha mizere mizere chitapangidwa kaamba ka iye. Chifukwa cha ichi, abale opeza a Yosefe “anamuda iye, ndipo sanathe kulankhula ndi iye mwa mtendere.” Iwo anapeza chifukwa chowonjezereka cha kumudera iye pamene iye anali ndi maloto awiri omwe iwo anatanthauzira kutanthauza kuti iye adzawalamulira’ iwo. Mofananamo, atsogoleri pakati pa Ayuda anafikira kumuda Yesu chifukwa chakumvera kwake, kuphUnzitsa kwake kokakamiza, ndi dalitso lowonekera la Yehova pa iye.​—Genesis 37:3-11; Yohane 7:46; 8:40.

12. (a) Ndi chifukwa ninji Yakobo anali wodera nkhawa ponena za ana ake? (b) Kodi ndi kufanana kotani kumene timapeza pakati pa njira ya Yosefe ndi ija ya Yesu?

12 Mkupita kwanthawi, abale ake a Yosefe anali kusamalira nkhosa kufupi ndi Sekemu. Atate wa Yosefe moyenerera anali wodera nkhawa chifukwa chakuti kunali kumeneko kumene Sekemu anadetsa Dina, kotero kuti Simeoni ndi Levi, limodzi ndi abale awo ena, anapha amuna a mzinda umenewo. Yakobo anafunsa Yosefe kupita ndi kukawona mmene abale ake anali kukhalira ndi kubweretsa ripoti kwa iye. Mosasamala kanthu za udani wa abale ake kulinga kwa iye, Yosefe mwamsanga ananyamuka kukawapeza iwo. Mu njira yofananayo, Yesu mwachimwemwe anavomereza thayo la Yehova pano padziko lapansi, ngakhale kuti kunatanthauza kuvutika kwambiri mkati mwa kupangitsidwa kwake kukhala wangwiro monga Mtsogoleri Woyamba wachipulumutso. M’kupirira kwake, Yesu anakhala chitsanzo chabwino chotani nanga kaamba ka ife tonse!​—Genesis 34:25-27; 37:12-17; Ahebri 2:10; 12:1, 2.

13. (a) Kodi ndimotani mmene abale opeza a Yosefe anabwezerera chidani chawo? (b) Kodi chisoni cha Yakobo chingayerekezedwe ndi chiyani?

13 Abale opeza khumi a Yosefe anamuwona iye akubwera patali. Mwamsanga mkwiyo wawo unayaka pa iye, ndipo iwo anapangana kumuchotsa iye. Poyambirira iwo anakonzekera kumupha iye. Koma Rubeni, chifukwa chathayo monga woyamba kubadwa, anapambana mkuwakakamiza iwo kumuponya Yosefe mu chitsime chamadzi chouma, akumalingalira kubwerera pambuyo pake ndi kumumasula iye. Panthawiyo, ngakhale kuli tero, Yuda anakakamiza abale ake kumugulitsa iye monga kapolo kwa Aismayeli omwe anali kudutsa. Abalewo kenaka anatenga mwinjiro wautali wa Yosefe ndi kuuviika iwo mu mwazi wa mbuzi yamphongo ndi kuutumiza iwo kwa atate awo. Pamene Yakobo anauwona iwo, iye anapfuula: “Ndiwo malaya a mwana wdnga! wajiwa ndi chirombo! Yosefe wakadzulidwa ndithu!” Yehova angakhale anamva chisoni chofananacho pa kuvutika kwa Yesu pamene iye anakwaniritSa thayo lake padziko lapansi.​—Genesis 37:18-35; 1 Yohane 4:9, 10;

Yosefe mu Igupto

14. Kodi ndimotani mmene chitsanzo chamake dzana chimenechi chingatipindulire ife lerolino?

14 Sitiyenera kumaliza kuti kukwamritsidwa kwa zochitika za chitsanzo zokhudza Yosefe kunachitika mundandanda yolongosoka yeniyeniyo. M’malo mwake, timapeza m’mbuyomo ndandanda ya Zochitika zomwe ziri kaamba ka malangizo athu ndi chilimbikitso lerolino. Monga mmene mtumwi Paulo ananenera:“Pakuti zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiriro ndi chitorithozo cha Malembo, tikhale ndi chiyembekezo. Ndipo Mulungu wa chipiriro ndi wa chitonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake, monga mwa Kristu Yesu; kuti nonse pamodzi, m’kamwa mmodzi, mukalemekeze Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu ​-Aroma 15:4-6.

15. Kodi nchifukwa ninji Yosefe ndi nyumba ya Potifara inapita patsogolo?

15 Yosefe anatengedwa kupita ku Igupto, ndipo kumeneko iye anagulitsidwa ku Muaigupto wotchedwa Potifara, mkulu wa asirikari a Farao. Yehova anatsimikizira kukhala ndi Yosefe, yemwe anapitirizabe kukhala ndi maprinsipulo abwino amene atate wake anali ataika mwa iye, ngakhale kuti iye anali kutali kwambiri kuchokera kunyumba ya atate wake. Yosefe sanasiye kulambira Yehova. Mbuye wake, Potifara, anayamikira mikhalidwe yowonekera ya Yosefe ndipo anamuika iye woyang’anira nyumba yake. Yehova anapitiriza kudalitsa nyumba ya Potifara chifukwa cha Yosefe.​—Genesis 37:36; 39:1-6.

16, 17. (a) Kodi ndimotani mmene Yosefe anakumanizirana mowonjezereka ndi chiyeso chaumphumphu? (b) Chokumana nacho cha Yosefe mu naende chinasonyeza kuchitsogozo chiti chazinthu?

16 Kunali kumeneko kumene mkazi wa Potifara anayesa kumunyenga Yosefe. Iye anapitiriza kumukana iye. Tsiku lina iye anamugwira chovala chake, koma iye anathawa, akumachisiya icho m’dzanja lake. Pamaso pa Potifara, iye anamuimba mlandu Yosefe wakufuna kugona naye, ndipo Potifara anamuika Yosefe mu ndende. Kwakanthawi iye anamangidwa ndi zingwe za chitsulo. Koma kupyolera m’nsautso ya chokumana nacho chake cha m’ndende Yosefe anapitirizabe kutsimikizira kuti iye anali munthu waumphumphu. Chotero, wosunga wandende anamuika iye woyang’anira wa akaidi onse.​—Genesis 39:7-23; Masalmo 105:17, 18.

17 Mu kupita kwanthawi, wamkulu wa woperekera chikho wa Farao ndi wamkulu wa ophika mkate anamukwiitsa iye ndipo anawaika mu ndende. Yosefe anapatsidwa thayo la kuwatumikira iwo. Kachwirinso, Yehova anayendetsa zinthu. Nduna ziwirizo zinali ndi maloto omwe anasautsa izo. Pambuyo pa kugogomezera kuti “kumasulira ndi kwa Mulungu,” Yosefe anauza iwo chimene maloto awo anatanthauza. Ndipo monga momwe Yosefe anasonyezera, masiku atatu pambuyo pake (pa tsiku la kubadwa kwa Farao) woperekera chikho anabwezeretsedwa kumalo ake, koma wamkulu wa ophika mkate anapachikidwa.​—Genesis 40:1-22.

18. (a) Kodi ndimotani mmene Yosefe anakumbukiridwira? (b) Kodi nchiyani chimene chinali mbali yeniyeni ya maloto a Farao?

18 Ngakhale kuti Yosefe anadandaulira woperekera chikho kukalankhula kwa Farao m’malo mwake, zaka ziŵiri zinapita munthuyo asanakumbukire Yosefe. Ngakhale pamenepo, ichi chinali kokha chifukwa cha kulota kwa Farao maloto aŵiri ovuta kumasulira mtsiku limodzi. Pamene panalibe aliyense wa ansembe amatsenga a mfumu yemwe akanamasulira tanthauzo lake, woperekera chikho anauza Farao kuti Yosefe angatanthauzire maloto. Chotero Farao anamuitana Yosefe, amene modzichepetsa analoza ku Magwero a kumasulira kowona akumati: “Mulungu adzayankha Farao mwamtendere.” Wolamulira wa Igupto kenaka analongosola malotowo kwa Yosefe, chotere:

“Ndinaima m’mphepete mwa nyanja; ndipo tawona, zinatuluka m nyanjamo ng’ombe zazikazi zisanu ndi ziŵiri, zonenepa ndi za mawonekedwe abwino; ndipo zinadya m’mabango;ndipo, tawona, ng’ombe zazikazi zisanu ndi ziŵiri zina zinatuluka pambuyo pawo zosauka ndiza mawonekedwe oipa ndi zowonda, zoipa zotere sindinaziwone m’dziko la Aigupto; ndipo ng’ombe zazikazi zowonda ndi za mawonekedwe oipa zinadya ng’ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zonenepa. Ndipo pamene zinadya sizinadziwika kuti zinadya; koma zinaipabe m’mawonekedwe awo monga poyamba. . . .

“Ndipo ndinawona m’kulota kwanga, tawona, ngala zisanu ndi ziwiri zinamera pa mbuwa imodzi zodzala ndi zabwino; ndipo, tawona, ngala zisanu ndi ziwiri zina zofota, zowonda, zopsyerera ndi mphepo ya kum’mawa, zinamera pambuyo pawo; ndipo ngala zowonda zinameza ngala zisanu ndi ziŵiri zabwino; ndipo ndinafotokozera amatsenga; koma panalibe wondimasulira ine.”​—Genesis 40:23-41:24.

19. a) Kodi ndimotani mmene Yosefe anasonyezera kudzichepetsa? (b) Kodi ndi uthenga wotani umene unaperekedwa ndi tanthauzo lamalotowo?

19 Anali maloto achilendo chotani nanga! Kodi ndimotani mmene aliyense akanalongosolera iwo? Yosefe anatero, koma osati kaamba ka ulemerero wa iye mwini. Iye anati: Loto la Farao ndi limodzi. Chimene Mulungu ati achite . . . wasonyeza kwa Farao.” Kenaka Yosefe anapitiriza kuvumbulutsa uthenga wamphamvu wa ulosi wa maloto amenewo, akumati:

“Zidzafika zaka zisanu ndi ziŵiri zakuchuluka kwa chakudya mdziko lonse la Aigupto. Koma pambuyo pawo zidzauka zaka zisanu ndi ziwiri za njala, ndipo anthu adzaiwala zochuluka zonsezo mdziko la Aigupto ndipo njala idzapululutsa dziko . . . ndipo lotolo linabwezedwa kawiri kwa Farao, chifukwa chinthu chiri chokhazikika ndi Mulungu wowona, ndipo Mulungu wowona afulumira kuchichita.”​—Genesis 41:25-32.

20, 21. (a) Kodi ndimotani mmene Farao anachitira kuchenjezolo? (b) Pa nsonga iyi, kodi ndimotani mmene Yosefe angayerekezedwere ndi Yesu?

20 Kodi ndi chiyani chimene Farao akanachita ponena zanjala yomayandikirayo? Yosefe anavomereza kuti Farao apange makonzedwe mwakukhazikitsa woyang’anira wochenjera ndi wanzeru padziko kuti asunge chakudya chotsala cha zokolola za zaka zabwino. Kufika nthawi imene ino Farao anali atazindikira mikhalidwe yowonekera ya Yosefe. Akumachotsa mphete yake kuchoka m’dzanja lake ndi kuika iyo padzanja la Yosefe, Farao chotero anamusankha iye kukhala woyang’anira dziko la Igupto.​—Genesis 41:33-46.

21 Yosefe anali wa zaka 30 pamene iye anaima pamaso pa Farao, msinkhu wofanana ndi wa Yesu Kristu pamene iye anabatizidwa ndi kuyamba uminisitala wake wopatsa moyo. Nkhani yotsatira idzasonyeza ndimotani mmene Yosefe anagwiritsidwira ntchito ndi Yehova kuunikira “Mtsogoleri Wamkulu ndi Mpulumutsi” wa Yehova mnthawi ya njala yauzimu ndi kulozera kwapadera ku tsiku lathu.​—Machitidwe 3:15; 5:31.

Kodi Mumayankha Motani?

◻ Kodi ndi munjira ziwiri ziti mmene njala iliri chaupandu lerolino?

◻ Kodi ndi mikhalidwe yabwino yotani imene Yosefe anali nayo pamene iye anali ndi abale ake opeza?

◻ Kodi nchiyani chimene tingaphunzire kuchokera ku zokumana nazo zoyambirira za Yosefe mu Igupto?

◻ Kudera nkhawa kwa Yehova kaamba ka Yosefe ndi anthu anjala kumatitsimikizira ife za chiyani?

ndipo ndimotani mmene iyo inanenedweratu

[Bokisi pa tsamba 13]

Wolemba nkhani mudanga la The Sunday Star (Toronto, March 30, 1986) ananena ponena za matchalltcfri odzlnenera kukhala otsogolera: “Kumene iwo akulephera kwambiri ndi; kupanga chigwirizano ndi njala yozama kwambiri yauzimu ya amuna, akazi, ndi anthu achichepere lerolino”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena