Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 5/1 tsamba 4-7
  • Kodi Nchiyani Chimene Chiri Chifuno Chaulosi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nchiyani Chimene Chiri Chifuno Chaulosi?
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chipembedzo Choyamba
  • Chipembedzo Chonyenga Chiwonekera
  • Chifuno cha Ulosi
  • Chifukwa Ninji kwa a Israyeli?
  • Bukhu la Ulosi Wowona
  • Kumasuka ku Chipembedzo Chonyenga
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kodi Mulungu Wakhala Akuchitanji?
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
  • Kulambira Kumene Mulungu Amavomereza
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Khalani ndi Chikhulupiriro M’mawu Aulosi a Mulungu!
    Nsanja ya Olonda—2000
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 5/1 tsamba 4-7

Kodi Nchiyani Chimene Chiri Chifuno Chaulosi?

AWO amene amadzigangira kuti kulambira kwawo kosiyanasiyana kuli zivumbulutso zochokera ku magwero a mphamvu yoposa ya munthu amavomerezanso kuti pali mphamvu yoposa ya chibadwa imene iri yabwino ndi yoipa. Kuvomereza kumeneku kumadzutsa mafunso awa: Kodi mtundu uliwonse wa kulambira unavumbulutsidwa kuchokera kumagwero abwino? Kapena kodi kuli ndi magwero oipa? Ndi kuti kumene kuli kouziridwa ndi Mulungu wowona?

Chipembedzo Choyamba

Mtundu wa anthu umazindikiridwa kukhala banja limodzi, ichi chimagwirizana ndi mbiri ya Baibulo ya anthu awiri oyambirira, Adamu ndi Hava. Yehova, Mlengi, anadzidziwikitsa iyemwini kwa iwo. Iye anavumbula kwa Adamu ndi Hava ntchito yawo mu chifuno chake ndi unansi wawo weniweni kwa iye. Mulungu anapanga Adamu kukhala mneneri wake woyamba, ndi thayo la kupereka zivumbulutso za umulungu kwa mkazi wake ndipo mkupita kwanthawi kwa ana awo, ndiko kuti, mtundu wonse wa anthu.​—Genesis 1: 27-30; 2:15-17.

Ichi chinali chipembedzo chokha, mtundu umodzi wakulambira wovumbulutsidwa ndi Yehova Mulungu. Kunawonetsedwa ndi chimvero ku chifuno cha Mulungu. Kunalibe malamulo achipembedzo, nsembe, malo oyera, kapena kuombeza kumene kunafunikira.

Chipembedzo Chonyenga Chiwonekera

“Vumbulutso” lotsutsa loyamba linachokera kwa mngelo amene anafuna kulambiridwa. Iye anapereka lingaliro losemphana ndi chipembedzo chowona ndipo ananyenga Adamu ndi Hava kugwirizana naye mkupandukira Mlengi wawo. Ichi chinamupanga iye kukhala Satana mtsutsi wa Yehova. “Ulosi” wake unawoneka monga unapereka kudzipangira chosankha ndi chimasuko kuchoka kwa Mulungu. Mmalo mwake, unadzetsa ukapolo kwa Satana ndi ku uchimo, kubweretsa imfa.​—Genesis 3:1-19; Mateyu 4:8-10; Aroma 5:12.

Mu kupita kwanthawi angelo ena opanduka, kapena ziwanda zinagwirizana ndi Satana. Mosakaikira izi zinabweretsa ganizo la chipembedzo lonyenga limene linapangitsa chivundi cha mtundu wa anthu. Masiku a mdzukulu wa Adamu, Enosi, “[chiyambi chinapangidwa, NW] cha kuitana pa dzina la Yehova.” Malinga ndi Tar gum ya Palestine, ichi chinachitidwa monyansa monga mbali ya kulambira mafano kwa panthawi imeneyo.​—Genesis 4:26; 6:1-8; 1 Petro 3:19, 20; 2 Petro 2:1-4.

Chipembedzo chonyenga chinafafanizidwa pa Chigumula cha mtsiku la Nowa, kusiyapo kokha mtundu wa kulambira kowona kochitidwa ndi mneneri wa Yehova, Nowa. (Genesis 6:5-9, 13; 7:23; 2 Petro 2:5) Ziwandazo zinatsala, ngakhale kuli tero, ndipo zinabweretsanso maulosi onyenga ndi maganizo a chipembedzo. Zinapangitsa mbadwa za Nowa kukwiyitsa Yehova mwa kumanga mzinda wa Babele monga malo apakati a kulambira konyenga. Koma Mulungu anasokoneza chinenero chawo ndi “kuwabalalitsa iwo kuchokera ku dziko lonse lapansi.”​—Genesis 11:1-9.

Kodi nchiyani chimene zonsezi zikutiuza? Tonsefe tiri mbadwa za Nowa ndi Adamu. Chotero miyambo yonse iri ndi chiyambi chofanana ndipo inasunga ganizo la Mulungu monga. chiyambi cha chidzŵitso chimene chapulumuka kuchokera mtsiku la Nowa. Koma ganizo loyamba limeneli linavunditsidwa ndi malingaliro a chipembedzo chonyenga acholowa kuchokera kwa makolo oyamba amene anabalalitsidwa kuchokera ku Babele pambuyo pake wobwezeretsedwa monga Babulo kupita ku mbali zonse za dziko lapansi. Ichi chimawonedwa mu miyambo yofala ponena za mizimuya anthu akufa, mu kulambira makolo, ndi kachitidwe ka kupenda nyenyezi, ulauli, ndi ufiti.​—Danieli 2:1, 2.

Chifuno cha Ulosi

Kodi ichi chikutanthauza kuti zipembedzo za masiku ano ziri zozikidwa kokha pa ganizo lacholowa kuchokera kale? Ayi. Satana ndi ziwanda amauzirabe ulosi wonyenga kunyenga ndi kugawanitsa mtundu wa anthu kusokoneza zivumbulutso zowona zonena za Mulungu, ndi kukhazikitsa maganizo onyenga ndi zipembedzo. (1 Timoteo 4:1; 1 Yohane 4:1-3; Chivumbulutso 16:13-16) Baibulo limati: “Padakhalanso pakati pa anthuwo aneneri onama, monganso padzakhala aphunzitsi onama pakati pa inu, amene adzalowa nayo m’tseri mipatuko yotayikitsa.”​—2 Petro 2:1.

Kumbali ina, Yehova wasunga chipembedzo chowona chimene chinaperekedwa mu Edene. Iye wawonjezera chidziŵitso ku chidziŵitso chathu cha iye ndi thayo lathu mkukwaniritsa chifuno chake. Chotero maulosi owona amadziŵikitsa chowonadi chonena za Mulungu, chifuno chake, ndi mkhalidwe wake wabwino wa makhalidwe. Amamvetsetsa bwino unansi wa munthu ndi iye kotero kuti abwezere mtundu wa anthu mchigwirizano ndi chifuno chake, kutsogolera ku kukwaniritsa kwake kotheratu.​—Yesaya 1:1820; 2:1-5; 55:8-11.

Pa chiyambi cha chipanduko cha munthu, Yehova analankhula ulosi umene unapereka chiyembekezo kwa mbadwa za Adamu ndi Hava. Iye anavumbulutsa kuti kudzakhala mpulumutsi, “mbewu,” amene akawononga Satana ndi mbadwa zake. (Genesis 3:15) Maulosi atsopano anathandizira kuzindikiritsa“mbewu,” yolonjezedwayi “wodzozedwa” wa Mulungu, ndi kuvumbula kuti akachita mbali yaikulu m’kukwaniritsa zifuno za Mulungu.​—Masalmo 2:2; 45:7; Yesaya 61:1.

Chotero cholinga choyambirira cha ulosi chinali kudziwikitsa zifuno za Mulungu ndi “wodzozedwa,” kapena “Kristu,” kupyolera mwa amene zikakwaniritsidwa. Popeza wosankhidwa ameneyu anatsimikizira kukhala Yesu, mngelo wa Yehova anati: “Lambira Mulungu; pakuti umboni wa Yesu ndiwo unauzira [kapena ndiwo mzimu wal kunenera.” (Chivumbulutso 19:10, NW) Nsonga ziŵiri zamveketsedwa ndi chilengezo ichi. Choyamba, palibe mthenga wa ulosi wowona amene angalamule kuti alambiridwe chifukwa kulambira kowona kuli kwa Yehova Mulungu yekha. (Mateyu 4:4; Yohane 4:23, 24) Chachiŵiri, chifuno chachikulu cha ulosi wonse wowona chiyenera kukhala kuvumbula zochitika ndi zenizeni zokhudza Yesu. Ichi chimazindikiritsa ntchito yeniyeni imene Yehova anampatsa iye mu kuchita chifuno chake cha kuyeretsa dzina Lake ndi kubwezeretsa dziko lapansi ku malo Ake enieni’ mkakhazikitsidwe Kake ka zinthu.​—Yohane 14:6; Akolose 1:19, 20.

Kaamba ka chifukwa ichi, mauthenga ouziridwa kuchokera kwa Mulungu analoza choyambirira kwa Yesu. Mzimu wonse, kapena cholinga ndi chifuno, cha ulosi wowona woterowo chinali kuchitira umboni iye. Kuwonjezerapo, kuzindikiridwa kwa maulosi mwa Yesu kumazindikiritsa iwo onse kukhala owona. Ichi ndicho chifukwa chake Baibulo likunena likuti “chowonadi chakhala chokwaniritsidwa mwa Yesu Kristu.” “Pakuti ngakhale ali ambiri malonjezo a Mulungu akhala okwaniritsidwa kupyolera mwa Yesu.”​—Yohane 1:17; 2 Akorinto 1:20; Machitidwe 10: 43; 28:23.

Chifukwa Ninji kwa a Israyeli?

Yehova anayamba “umboni wake kwa Yesu” mwa ulosi wake kuloza ku “mbewu” yolonjezedwa. Mulungu pambuyo pake anavumbulutsa mzera wa padziko lapansi wa “mbewu” monga kupyolera mwa Nowa. , Shemu, Abrahamu, Isake (osati Ismayeli), ndi Yakobo. Amuna amene anatsala omvera ku chipembedzo chowona, kudzitsimikizira kukhala aneneri okhulupirika a Yehova pamene mitundu yonse inali yovunditsidwa ndi kulambira muungu yonyenga. (Genesis 6:9; 22: 15-18; Ahebri 11:8-10, 16) Mzerawo unapitiriza kupyolera mu mbadwa za amuna amenewa​—mtundu wa Israyeli ndipo makamaka banja la Davide, mfumu yodziwika kwambiri ya mrayeli.​—2 Samueli 7:12-16.

Kuwonetsa chifukwa chimene anasankhira Israyeli, Yehova anati: “Sikuchuluka kwanu koposa mitundu ina yonse ya anthu. . . [koma] chifukwa cha kusunga lumbiro . . . makolo anu,” Abrahamu, Isake, ndi Yakobo. (Deutronomo 7:6-8; 29:13) Mwachidziwikire, mtundu umodzi ndiwo ukanapereka mzera wa “mbewu” yolonjezedwa. Komabe chipembedzo chowona sichinali ndi malire kwa Aisrayeli okha. Pamene zivumbulutso za chowonadi sizinaperekedwe kwa mitundu ina, aliyense payekha kuchokera mwa iyo akanagwirizana ndi Israyeli m’kulambira, ndipo ena a iwo anaphatikizidwa mu mzera wa “mbewu.” (Numeri 9:14; Rute 4:10-22; Mateyu 1:5, 6) Zivumbulutso zapadera zopatsidwa kupyolera mu mtundu kapena mafuko zikanapangitsa mipatuko ya chipembedzo yokulira, pamene chiri chifuno cha Yehova kugwirizanitsanso mtundu wa anthu ku kulambira kumodzi.​—Genesis 22:18; Aefeso 1:8-10; 2:11-16.

Zifuno za Mulungu ziri zofanana kwa mafuko onse. Popeza ali wosasinthika mu mikhalidwe yake yokoma ndi zifuno, kachitidwe kake ndi Aisrayeli kanasonyeza mmene akachitira zinthu pa mikhalidwe imodzimodziyo panthawi ina iriyonse yopatsidwa, (Malaki3:6) Chotero Israyeli anatumikira monga chitsazo kwa mitundu yonse. Kupyolera mwa iye Mulungu anasonyeza mapindu amene ali mu kulambira kowona ndi kuipa kwa kachitidwe konyenga. Pamene Aisrayeli anapitiriza kukhala okhulupirika kwa iye, anawachinjiriza ndi kuwadaHtsa iwo. Pamene iwo anatembenukira kwa milungu yonama ya mitundu ina, anatsenderezedwa ndi mitunduyo, monga momwe Yehova anawachenjezera.​—Deuteronomo 30:15-20; Danieli 9:2-14.

Israyeli anatumikiranso monga chitsanzo cha ulosi, ndipo Davide anakhala woimira wa Yesu mwa ulosi, amene analowa mu pangano la Ufumu la Mulungu ndi Davide. (1 Mbiri 17:11, 14; Luka 1:32) Lamulo lopatsidwa kwa Israyeli, limodzi ndi nsembe zake ndi unsembe, zinaimira nsembe ya Yesu ndi kuloza ku Ufumu wake wakumwamba ndi unsembe. Chotero Lamulo linakhala “nkhoswe kuloza kwa Kristu.”​—Agalatiya 3:19, 24; Machitidwe 2:25-36; Ahebri 10:1-10; Chivumbulutso 20:4-6.

Bukhu la Ulosi Wowona

Mawu ofunika awa sakanasungidwa mosamalitsa ndi miyambo ya pakamwa kapena zivumbulutso zosiyana ku mitundu yosiyanasiyana. Njira yabwino koposa ya kusungira ndi kuipereka kwa mitundu yonse iri mbiri yolembedwa. Ndipo Baibulo limakwaniritsa mbali imeneyi. Ho lokha liri ndi zivumbulutso zouziridwa ndipo limasunga mbiri ndi mawu aulosi mu zochita zake ndi anthu. ilo lokha limaloza kwa Yesu Kristu monga Nthumwi ya Mulungu kaamba ka chipulumutso ndipo liri ndi ulosi womaliza ponena za kukwaniritsa kwake ntchito ya Umesiya ya mtsogolo. Chotero iri liri Mawu ouziridwa athunthu olembedwa a Mulungu.​—Aroma 15:4; 1 Akorinto 10:11; 2 Petro 1:20, 21.

Kuyambira pamene Baibulo linamalizidwa, awo amene anabweretsa “maulosi” atsopano, zipembedzo, ndi mipatuko sangakhale ouziridwa ndi Mulungu. Maulosi owona sanaperekedwe kuti avumbulutse zipembedzo zatsopano. Anachipanga chipembedzo chowona chimodzi kukhala chatsopano ndi kudziwikitsa kugwira ntchito kwa mtsogolo kwa chifuno cha Yehova. Kukwaniritsidwa kwawo kumapereka chitsimikiziro cha Umulungu wake wapadera ndi mphamvu, kusonyeza kuti iye yekha anganeneretu zaka mazana pasadakhale za zochitika ndipo mosalakwa kuzikwaniritsa izo.​—Yesaya 41:21-26; 46:9-11.

Chotero onse amene amakhumba kuzolowerana ndi ulosi wowona ndi kuchita chipembedzo chowona ayenera kutembenukira ku Baibulo. Liri bukhu la Mulungu la ulosi​—uthenga wake wokwanira ku mtundu wa anthu.​—2 Timoteo 3:16, 17.

[Chithunzi patsamba 7]

Mzera wa ”mbewu” yolonjezedwa

Nowa

Semu

Abrahamu

Isake

Yakobo

Davide

Yesu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena