Landirani Baibulo Monga Momwe Lililidi
“Tiyamika Mulungu kosalekeza, kuti, pakulandira mawu a uthenga wa Mulungu [amene munamva kwa ife, NW] simunawalandira monga mawu a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mawu a Mulungu, amenenso achita mwa inu okhulupirira.”—1 ATESALONIKA 2:13.
1. Kodi ndi chidziŵitso chotani cha m’Baibulo chimene chimalipanga bukulo kukhala lapadera kwambiri?
BAIBULO LOPATULIKA ndilo buku lotembenuzidwa m’zinenero zambiri koposa ndi lofalitsidwa kwambiri padziko lonse. Ambiri amalizindikira kukhala limodzi la mabuku aukatswiri. Komabe, chofunika koposa nchakuti, Baibulo limapereka chitsogozo chimene anthu a fuko ndi dziko lililonse akufunikira kwambiri, mosasamala kanthu za ntchito kapena malo awo m’moyo. (Chivumbulutso 14:6, 7) Mwa njira imene imakhutiritsa maganizo ndi mtima womwe, Baibulo limayankha mafunso onga: Kodi chifuno cha moyo wa munthu nchiyani? (Genesis 1:28; Chivumbulutso 4:11) Kodi nchifukwa ninji maboma a anthu alephera kudzetsa mtendere wachikhalire ndi chisungiko? (Yeremiya 10:23; Chivumbulutso 13:1, 2) Chifukwa ninji anthu amafa? (Genesis 2:15-17; 3:1-6; Aroma 5:12) M’dziko lamavutoli, kodi tingakhoze bwanji kuchita mwachipambano ndi mavuto a moyo? (Salmo 119:105; Miyambo 3:5, 6) Kodi mtsogolo mwatisungiranji?—Danieli 2:44; Chivumbulutso 21:3-5.
2. Kodi nchifukwa ninji Baibulo limapereka mayankho odalirika kotheratu pa mafunso athu?
2 Kodi nchifukwa ninji Baibulo limayankha mafunso otero motsimikiza? Chifukwa chakuti lili Mawu a Mulungu. Iye anagwiritsira ntchito anthu kulilemba, koma monga momwe pa 2 Timoteo 3:16 pamanenera bwino lomwe, “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu.” Silinakhalepo mwa kumasulira kwa munthu zochitika zaumunthu. “Chinenero [mawu a zilinkudza, malamulo a Mulungu, miyezo ya makhalidwe ya Baibulo] sichinadza ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi mzimu woyera, analankhula.”—2 Petro 1:21.
3. (a) Tchulani zitsanzo zosonyeza mmene anthu m’maiko osiyanasiyana aliyamikirira Baibulo koposa. (b) Kodi nchifukwa ninji anthu anafuna kuika miyoyo yawo pangozi kuti aŵerenge Malemba?
3 Pozindikira kufunika kwa Baibulo, anthu ambiri aika moyo wawo pangozi ya kuponyedwa m’ndende, ngakhale imfa, kuti akhale nalo ndi kuliŵerenga. Zimenezo zinalidi choncho zaka zakumbuyozo m’Spain Wachikatolika, kumene atsogoleri achipembedzo anachita mantha kuti mphamvu yawo ikafooketsedwa ngati anthu akaŵerenga Baibulo m’chinenero chawo; zinalinso choncho ku Albania, kumene malamulo olimba anaperekedwa mu ulamuliro wokana Mulungu kotero kuti athetse chisonkhezero chonse cha chipembedzo. Komabe, anthu owopa Mulungu anasunga mosamalitsa makope a Malemba, kuwaŵerenga, ndi kukambitsirana za iwo. M’Nkhondo Yadziko II, mumsasa wachibalo wa Sachsenhausen, anthu ankapatsirana Baibulo mochenjera m’malumande (ngakhale kuti zimenezi zinali zosaloledwa), ndipo aja amene anali ndi mwaŵi wa kuliŵerenga analoŵeza pamtima mbali zake kuti akauze ena. M’ma 1950, m’dziko limene panthaŵiyo linali East Germany Wachikomyunizimu, Mboni za Yehova zimene zinali m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro chawo zinadziika pangozi ya kukhala akaidi obindikiritsidwa payekhapayekha kwanthaŵi yaitali pamene zinapatsirana zigawo zazing’ono za Baibulo zoŵerenga usiku. Nchifukwa ninji zinachita zimenezo? Chifukwa chakuti zinazindikira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu, ndipo zinadziŵa kuti “munthu sakhala wamoyo ndi mkate wokha,” koma “ndi zonse zakutuluka m’kamwa mwa Yehova.” (Deuteronomo 8:3) Mawu ameneŵa, olembedwa m’Baibulo, anakhozetsa Mbonizo kukhalabe zamoyo mwauzimu ngakhale kuti zinachitiridwa nkhanza yosaneneka.
4. Kodi Baibulo liyenera kukhala ndi malo otani m’miyoyo yathu?
4 Baibulo si buku longoika pa shelufu ndi kuliŵerenga kamodzikamodzi, ndipo silinalinganizidwire kugwiritsiridwa ntchito chabe pamene okhulupirira asonkhana pakulambira. Liyenera kugwiritsiridwa ntchito tsiku lililonse kuunikira mikhalidwe imene timayang’anizana nayo ndi kutisonyeza njira yoyenera ife kuyendamo.—Salmo 25:4, 5.
Linalembedwa Kuti Liŵerengedwe ndi Kumvedwa
5. (a) Ngati kuli kotheka, kodi ife tonse tiyenera kukhala ndi chiyani? (b) Mu Israyeli wakale, kodi anthu anali kudziŵa bwanji zimene zinali m’Malemba? (c) Kodi Salmo 19:7-11 limakhudza bwanji maganizo anu kulinga ku kuŵerenga Baibulo?
5 M’tsiku lathu lino, ma Baibulo amapezeka mosavuta m’maiko ambiri, ndipo tikulimbikitsa aliyense amene amaŵerenga Nsanja ya Olonda kugula kope lake. Panthaŵi imene Baibulo linali kulembedwa, kunalibe makina osindikiza. Anthu ambiri analibe makope awoawo. Koma Yehova anachititsa kuti atumiki ake amve zimene zinalembedwa. Chifukwa chake, Eksodo 24:7 amasimba kuti Mose atalemba zimene Yehova anamuuza, iye “anatenga buku la chipangano naŵerenga m’makutu a anthu.” Pokhala mboni za zochitika zachilendo paphiri la Sinai, iwo anazindikira kuti zimene Mose anawaŵerengera zinachokera kwa Mulungu ndi kuti iwo anafunikira kudziŵa mawuwo. (Eksodo 19:9, 16-19; 20:22) Nafenso tifunikira kudziŵa zimene zalembedwa m’Mawu a Mulungu.—Salmo 19:7-11.
6. (a) Kodi Mose anachitanji mtundu wa Israyeli usanaloŵe m’Dziko Lolonjezedwa? (b) Kodi tingachitsanzire bwanji chitsanzo cha Mose?
6 Pamene mtundu wa Israyeli unakonzekera kuwoloka Mtsinje wa Yordano kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, motero akumasiya moyo wawo wopupulika m’chipululu, kunali koyenera kwa iwo kupendanso Chilamulo cha Yehova ndi zochita zake pa iwo. Posonkhezeredwa ndi mzimu wa Mulungu, Mose anapenda nawo Chilamulo. Anawakumbutsa mfundo zonse za Chilamulo, ndipo anasonyezanso mikhalidwe yake yaikulu ndi mzimu umene unayenera kusonkhezera unansi wawo ndi Yehova. (Deuteronomo 4:9, 35; 7:7, 8; 8:10-14; 10:12, 13) Pamene ife lerolino tilandira ntchito yatsopano kapena kuyang’anizana ndi mikhalidwe yatsopano m’moyo, nafenso tingachite bwino kuona mmene uphungu wa Malemba uyenera kulamulira zimene timachita.
7. Aisrayeli atangowoloka Yordano, kodi anachita chiyani kuti akhomereze Chilamulo cha Yehova m’maganizo ndi mitima yawo?
7 Israyeli atangowoloka Mtsinje wa Yordano, anthu anasonkhananso kuti apendenso zimene Yehova anawauza mwa Mose. Mtunduwo unasonkhana pafupifupi makilomita 50 kumpoto kwa Yerusalemu. Theka la mafukowo anaima pandunji pa phiri la Ebala, ndipo ena theka pandunji pa phiri la Gerizimu. Pamenepo Yoswa “anaŵerenga mawu onse a chilamulo, dalitso ndi temberero.” Motero, amuna, akazi, ndi ana, limodzinso ndi alendo akuyenda pakati pawo, anamva kubwerezedwa kwa panthaŵi yake kwa malamulo onena za khalidwe limene likachititsa Yehova kusawayanja ndi madalitso amene iwo akapeza ngati akamvera Yehova. (Yoswa 8:34, 35) Anafunikira kukhala ndi chithunzi chabwino m’maganizo ponena za chabwino ndi choipa mogwirizana ndi lingaliro la Yehova. Ndiponso, anafunikira kukhomereza m’mitima yawo kukonda chabwino ndi kudana nacho choipa, monga momwe aliyense wa ife amachitira lerolino.—Salmo 97:10; 119:103, 104; Amosi 5:15.
8. Kodi kuŵerenga Mawu a Mulungu panthaŵi ndi nthaŵi pamisonkhano ina mu Israyeli kunali ndi phindu lotani?
8 Kuwonjezera pa kuŵerenga Chilamulo panthaŵi zapadera zimenezo za m’mbiri, makonzedwe a kuŵerenga Mawu a Mulungu nthaŵi zonse analongosoledwa pa Deuteronomo 31:10-12. Chaka chachisanu ndi chiŵiri chilichonse, mtundu wonse unafunikira kusonkhana kuti umvetsere kuŵerengedwa kwa Mawu a Mulungu. Zimenezi zinawapatsa chakudya chauzimu. Zinachititsa maganizo ndi mitima yawo kusungabe malonjezo a Mbewu, ndipo zinathandiza okhulupirika kuzindikira Mesiya. Makonzedwe a kudya kwauzimu amene anayamba pamene Israyeli anali m’chipululu sanathe pamene iwo analoŵa m’Dziko Lolonjezedwa. (1 Akorinto 10:3, 4) M’malo mwake, Mawu a Mulungu anawonjezedwa mwa kuphatikizapo mavumbulutso ena a aneneri.
9. (a) Kodi Aisrayeli anali kungoŵerenga chabe Malemba atasonkhana pamodzi m’magulu? Fotokozani. (b) Kodi malangizo a m’Malemba anali kuperekedwa motani m’banja lililonse, ndipo ndi cholinga chotani?
9 Kupenda uphungu wa Mawu a Mulungu sikunayenera kuchitidwa chabe panthaŵi imene anthuwo ankasonkhana m’gulu lalikulu. Anayenera kukambitsirana masiku onse zigawo za Mawu a Mulungu ndi malamulo amene alimo. (Deuteronomo 6:4-9) M’madera ambiri lerolino, achichepere akhoza kukhala ndi Baibulo lawolawo, ndipo angapindule kwambiri mwa kukhala nalo. Koma m’Israyeli wakale, zinthu sizinali choncho. Panthaŵiyo, pamene makolo anali kupereka malangizo kuchokera m’Mawu a Mulungu, anali kudalira pa zimene anali ataloŵeza pamtima ndi choonadi chimene mitima yawo inayamikira, limodzinso ndi mipukutu yaing’ono iliyonse imene angakhale anali atalemba. Mwa kuwabwereza kaŵirikaŵiri, iwo ankayesayesa kukulitsa mwa ana awo kukonda Yehova ndi njira zake. Cholinga chawo sichinali chabe cha kudzaza chidziŵitso m’mutu koma kuthandiza wa m’banja aliyense kukhala ndi moyo mwa njira imene ikasonyeza chikondi pa Yehova ndi Mawu ake.—Deuteronomo 11:18, 19, 22, 23.
Kuŵerenga Malemba m’Masunagoge
10, 11. Kodi ndi programu iti ya kuŵerenga Malemba imene inatsatiridwa m’masunagoge, ndipo kodi Yesu anaziona bwanji nthaŵi zimenezi?
10 Panthaŵi ina Ayuda atatengedwa ukapolo ku Babulo, masunagoge anakhazikitsidwa kukhala malo olambirira. Kuti Mawu a Mulungu aziŵerengedwa ndi kukambitsiridwa pamalo osonkhanira ameneŵa, makope owonjezereka a Malemba anapangidwa. Zimenezi zinachititsa kukhalako kwa malembo apamanja akale pafupifupi 6,000 okhala ndi zigawo za Malemba Achihebri.
11 Mbali yofunika pa kulambira kwa m’sunagoge inali kuŵerenga Torah, imene imapanga mabuku asanu oyambirira a ma Baibulo amakono. Machitidwe 15:21 amasimba kuti m’zaka za zana loyamba C.E., kuŵerengako kunali kuchitika pa Sabata lililonse, ndipo Mishnah imasonyeza kuti pofika m’zaka za zana lachiŵiri, kuŵerenga Torah kunalinso kuchitika patsiku lachiŵiri ndi lachisanu la mlungu. Anthu angapo anali kuŵerenga zigawo zosankhidwa, motsatizana wina ndi mnzake. Mwambo wa Ayuda amene anali kukhala ku Babulo unali wa kuŵerenga Torah yonse pachaka; ku Palestina mwambowo unali wa kuchita kuŵerengako m’nyengo yoposa zaka zitatu. Chigawo cha Aneneri chinalinso kuŵerengedwa ndi kufotokozedwa. Unali mwambo wa Yesu kupezeka pa programu ya kuŵerenga Baibulo pa Sabata kumalo kumene anali kukhala.—Luka 4:16-21.
Kuwalabadira Kwaumwini ndi Kuwagwiritsira Ntchito
12. (a) Pamene Mose anaŵerengera anthu Chilamulo, kodi anthuwo anapindula motani? (b) Kodi anthuwo anayankha bwanji?
12 Kuŵerenga Malemba ouziridwa sikunayenera kungokhala mwambo chabe. Cholinga chake sichinali kungokondweretsa chabe anthu. Pamene Mose anaŵerengera Israyeli “buku la chipangano” pa chigwa choyang’anizana ndi phiri la Sinai, iye anatero kuti iwo adziŵe mathayo awo kwa Mulungu ndi kuwakwaniritsa. Kodi iwo akatero? Kuŵerengako kunafuna kuti iwo ayankhe. Anthu anazindikira zimenezo, ndipo analankhula, nati: “Zonse zimene Yehova walankhula tidzachita, ndi kumvera.”—Eksodo 24:7; yerekezerani ndi Eksodo 19:8; 24:3.
13. Pamene Yoswa anaŵerenga matemberero a kusamvera, kodi anthuwo anayenera kuchitanji, ndipo ndi cholinga chotani?
13 Pambuyo pake, pamene Yoswa anaŵerengera mtunduwo madalitso olonjezedwa ndi matemberero, kapena masoka, iwo anafunikira kuyankha. Malangizo anali akuti, pambuyo pa kutchulidwa kwa temberero lililonse: “Ndipo anthu onse ayankhe ndi kuti, Amen.” (Deuteronomo 27:4-26) Motero, pamfundo iliyonse iwo anavomereza poyera ziweruzo za Yehova pa zolakwa zotchulidwazo. Chochitikacho chiyenera kukhala chinali chochititsa chidwi chotani nanga pamene mtundu wonsewo unayankha mogwirizana ndi liwu lalikulu koposa!
14. M’nthaŵi ya Nehemiya, kodi nchifukwa ninji kuŵerenga Chilamulo poyera kunakhala kopindulitsa koposa?
14 M’nthaŵi ya Nehemiya, pamene anthu onse anasonkhana m’Yerusalemu kudzamva Chilamulo, iwo anaona kuti sanali kutsatira malangizo onse olembedwamo. Panthaŵiyo iwo sanazengereze kugwiritsira ntchito zimene anaphunzira. Kodi zotulukapo zake zinali zotani? “Chimwemwe chachikulu.” (Nehemiya 8:13-17) Atamaliza mlungu umodzi akuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku paphwandolo, iwo anazindikira kuti panafunikirabe zina. Mwapemphero iwo anapenda mbiri ya zochita za Yehova ndi anthu ake kuyambira masiku a Abrahamu mpaka masikuwo. Zonsezi zinawasonkhezera kuchita lumbiro la kukwaniritsa zofunika za Chilamulo, kuleka kukwatira akunja, ndi kulandira mathayo a kusamalira kachisi ndi utumiki wake.—Nehemiya, machaputala 8-10.
15. Kodi malangizo a pa Deuteronomo 6:6-9 amasonyeza motani kuti kuphunzira Mawu a Mulungu m’banja sikunayenera kukhala mwambo chabe?
15 Momwemonso, m’banja, kuphunzitsa Malemba sikunayenera kukhala mwambo chabe. Monga momwe taonera kale m’mawu ophiphiritsira pa Deuteronomo 6:6-9, anthu anauzidwa ‘kumanga mawu a Mulungu padzanja ngati chizindikiro’—motero akumasonyeza mwa chitsanzo ndi ntchito kukonda kwawo njira za Yehova. Ndipo anayenera kuika mawu a Mulungu ngati ‘chapamphumi pakati pa maso awo’—motero akumakumbukira nthaŵi zonse malamulo amene ali m’Malemba ndi kuwagwiritsira ntchito monga maziko a zosankha zawo. (Yerekezerani ndi mawu ogwiritsiridwa ntchito pa Eksodo 13:9, 14-16.) Anayenera ‘kuwalemba pamphuthu za nyumba zawo ndi pazipata zawo’—motero akumasiyanitsa nyumba zawo ndi malo awo monga malo kumene mawu a Mulungu analemekezedwa ndi kugwiritsiridwa ntchito. Mwa mawu ena, miyoyo yawo inayenera kupereka umboni wochuluka wakuti iwo anali kukonda malamulo olungama a Yehova ndi kuwagwiritsira ntchito. Zimenezo zinayenera kukhala zopindulitsa chotani nanga! Kodi Mawu a Mulungu ali ndi malo oyamba otero m’moyo wa tsiku ndi tsiku wa mabanja athu? Nzomvetsa chisoni kuti Ayuda anasintha zonsezi kukhala mwambo chabe, akumavala timaphukusi tokhala ndi malemba monga ngati kuti tinali zithumwa. Kulambira kwawo kunaleka kuchokera mumtima ndipo Yehova anakukana.—Yesaya 29:13, 14; Mateyu 15:7-9.
Thayo la Aja Amene Ali ndi Malo a Uyang’aniro
16. Kodi nchifukwa ninji kuŵerenga Malemba nthaŵi zonse kunali kofunika kwa Yoswa?
16 Nkhani ya kuŵerenga Malemba inalunjikitsidwa makamaka pa aja amene anali oyang’anira mtunduwo. Yehova anati kwa Yoswa: “Usamalire kuchita monga mwa chilamulo chonse.” Ndi cholinga cha kukwaniritsa thayo limenelo, iye anauzidwa kuti: “Ulingiriremo usana ndi usiku, . . . popeza ukatero udzakometsa njira yako, nudzachita mwanzeru.” (Yoswa 1:7, 8) Mofanana ndi woyang’anira Wachikristu aliyense lerolino, kuŵerenga Malemba nthaŵi zonse kwa Yoswa kukamthandiza kukumbukira bwino lomwe malamulo akutiakuti amene Yehova adapatsa anthu Ake. Yoswa anafunikiranso kumvetsetsa mmene Yehova adachitira ndi atumiki Ake m’mikhalidwe yosiyanasiyana. Pamene anali kuŵerenga za chifuno cha Mulungu, kunali kofunika kwa iye kusinkhasinkha thayo lake mogwirizana ndi chifuno chimenecho.
17. (a) Kuti mafumu apindule ndi kuŵerenga Malemba mwa njira imene Yehova ananena, kodi iwo anafunikira kuchitanji pamene anali kuŵerenga? (b) Kodi nchifukwa ninji kuŵerenga Baibulo nthaŵi zonse ndi kusinkhasinkha kuli kofunika kwambiri kwa akulu Achikristu?
17 Yehova analangiza kuti aliyense amene anatumikira monga mfumu pa anthu Ake anayenera kulemba buku la Chilamulo cha Mulungu poyamba ufumu wake, akumajambula m’buku limene linali kusungidwa ndi ansembe. Ndiyeno anafunikira ‘kuŵerengamo masiku onse a moyo wake.’ Cholinga chake sichinali kungoloŵeza pamtima mawu ake. M’malo mwake, chinali chakuti “aphunzire kuwopa Yehova Mulungu wake,” ndi kuti “mtima wake usadzikuze pa abale ake.” (Deuteronomo 17:18-20) Zimenezi zinafuna kuti iye asinkhesinkhe zimene anali kuŵerenga. Malinga ndi maumboni, mafumu ena anaganiza kuti anali otanganitsidwa kwambiri ndi ntchito yolamulira kwakuti sakanakhoza kuchita zimenezo, ndipo mtundu wonse unavutika chifukwa cha kunyalanyaza kwawo zimenezo. Ntchito ya akulu mumpingo Wachikristu sindiyo ija ya mafumu. Chikhalirechobe, mofanana ndi mafumuwo, kuli kofunika kwambiri kuti akulu aŵerenge Mawu a Mulungu ndi kuwasinkhasinkha. Kuchita kwawo motero kudzawathandiza kukhala ndi lingaliro loyenera ponena za aja omwe iwo akuwasamalira. Kudzawatheketsanso kukwaniritsa thayo lawo la uphunzitsi mwa njira imene imalemekezadi Mulungu ndi kulimbikitsa Akristu anzawo.—Tito 1:9; yerekezerani ndi Yohane 7:16-18; siyanitsani ndi 1 Timoteo 1:6, 7.
18. Kodi ndi chitsanzo chotani choperekedwa ndi mtumwi Paulo chimene kuŵerenga Baibulo ndi kuliphunzira kudzatithandiza kutsanzira?
18 Mtumwi Paulo, woyang’anira Wachikristu wa m’zaka za zana loyamba, anali munthu wodziŵa bwino Malemba. Polalikira anthu m’Tesalonika wakale, iye anakhoza kukambitsirana nawo Malemba mogwira mtima ndi kuwathandiza kumvetsetsa tanthauzo lake. (Machitidwe 17:1-4) Anafika mtima wa omvetsera enieni. Chifukwa chake, ambiri amene anamumvetsera anakhulupirira. (1 Atesalonika 2:13) Chifukwa cha programu yanu ya kuŵerenga Baibulo ndi kuliphunzira, kodi mukhoza kupereka zigomeko za m’Malemba mogwira mtima? Kodi malo amene kuŵerenga Baibulo kuli nawo m’moyo wanu ndi mmene mumakuchitira zimapereka umboni wakuti mumayamikiradi cholinga chake cha kukhala kwanu ndi Mawu a Mulungu? M’nkhani yotsatira, tidzapenda mmene inu, ngakhale aja amene ndandanda yawo ilibe mpata, mungaperekere yankho lovomereza pa mafunso ameneŵa.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi nchifukwa ninji anthu akhala akufuna kuika moyo ndi ufulu wawo pangozi kuti aŵerenge Baibulo?
◻ Kodi timapindula motani mwa kupenda makonzedwe amene anapangidwira Israyeli wakale a kumva Mawu a Mulungu?
◻ Kodi tiyenera kuchita nazo chiyani zimene timaŵerenga m’Baibulo?
◻ Kodi nchifukwa ninji kuŵerenga Baibulo ndi kusinkhasinkha kuli kofunika kwambiri kwa akulu Achikristu?
[Chithunzi patsamba 9]
Yehova anauza Yoswa kuti: “Ulingiriremo usana ndi usiku”