Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 6/1 tsamba 5-7
  • Zaka Chikwi Zopambana Zikuyandikira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zaka Chikwi Zopambana Zikuyandikira
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Choloŵa Chotaika
  • Olandira Choloŵa​—“Ana” a Kristu
  • Kupambana Ulamuliro wa Solomo
  • Kufikira Pamodzi Ndi Zaka Chikwi Zachitatu?
  • Kodi Zaka za Chikwi Chachitatu Zidzayamba Liti?
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Zaka 1000 Zatsopano—Kodi Tsogolo Lanu Ndi Lotani?
    Zaka 1000 Zatsopano—Kodi Tsogolo Lanu Ndi Lotani?
  • Kukhala Olinganizidwa Kaamba ka Kupulumuka Kuloŵa m’Zaka Chikwi
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Zaka Chikwi Zachitatu—Kodi Zidzakwaniritsa Ziyembekezo Zanu?
    Nsanja ya Olonda​—1990
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 6/1 tsamba 5-7

Zaka Chikwi Zopambana Zikuyandikira

“Ndipo ndinawona mipando yachifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa chiweruziro; ndipo ndinawona mizimu ya iwo amene adawadula khosi chifukwa cha umboni wa Yesu, ndi chifukwa cha mawu a Mulungu, ndi iwo amene sanalambira chirombo, kapena fano lake, nisanalandira lembalo pamphumi ndi pa dzanja lawo; ndipo anakhala ndi moyo, nachita ufumu pamodzi ndi Kristu zaka chikwi.” “Ndipo [Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso [pa anthu]; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.”​—Chibvumbulutso 20:4; 21:4.

BAIBULO limaneneratu motero za zaka chikwi zopambana zoyandikirazo​—Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Yesu Kristu ndi bungwe logwirizana naye la mafumu akumwamba. Mwinamwake ndinu wokhoterera kutsutsa ulosi umenenewu kukhala chinyengo, nthano. Komabe, pali chifukwa chokwanira kuti inu mulingalire Zaka Chikwi zimenezi kukhala zikubweradi!

Pakuti, phunziro la Baibulo lidzakuvumbulirani kuti ilo lachita ndi zaka zikwi zisanu ndi chimodzi za mbiri ya anthu mwanjira yokhulupirika kwenikweni. Kuwonjezera apa, Baibulo liri bukhu laulosi, ndipo chiŵerengero chachikulu cha zoneneratu zake, kapena maulosi, zakwaniritsidwa kale m’tsatanetsatane wake yense.a Izi pokhala tero, kodi nchifukwa ninji Baibulo silikudaliridwa poneneratu za kuyandikira kwa kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Kristu? Chotero, mungazizwe zimene Baibulo limatiuza ponena za nyengo imeneyo yanthaŵi. Kodi iyo idzatumikira chifuno chotani? Ndipo chokondweretsa kwenikweni kwa inu nchakuti, kodi zidzauyambukira motani moyo wanu?

Choloŵa Chotaika

Baibulo limasonyeza kuti Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Kristu ndiko njira yake yopatsirira choloŵa chamtengo wapatali koposa kwa “ana” ake. Koma kodi ncholoŵa chotani? Ndipo kwa “ana” ati? Choloŵa chingafotokozedwe kukhala chinthu chosiidwira ana a munthu pa imfa yake. Pamene kholo lathu Adamu anatsimikizira kukhala wosamvera Mulungu, anadzitaira yekha ndi ana ake onse​—mtundu wonse wa anthu​—kuyenerera kwa moyo wosatha m’dziko lapansi la paradaiso. Chotero Adamu anasiira mbadwa zake choloŵa cha uchimo, imfa, ndi mavuto.​—Genesis 3:1-19; Aroma 5:12.

Yesu anadza padziko lapansi m’thupi lanyama kudzawombolera anthu choloŵa chimene Adamu anachitaya. Iye anachita chimenechi mwakutsimikizira kukhala wokhulupirika kwa Yehova Mulungu, napereka moyo wake modzifunira kaamba ka mtundu wa anthu. (Yohane 3:16) Pokhala ndi moyo wangwiro, wopanda uchimo, Yesu anapeza kuyenerera kwa moyo wosatha wangwiro m’Paradaiso wa padziko lapansi​—chinthu chenichenicho chimene Adamu anachitaya. Komabe, Yesu sanapindule ndi kuyenerera kumeneko; ndipo sanakutaye pamene anafa naukitsidwira ku moyo wakumwamba. Motero iye akachigwiritsira ntchito monga choloŵa cha mtengo wapatali chosiira “ana” ake.​—Aroma 5:18, 19.

Olandira Choloŵa​—“Ana” a Kristu

Pa Yesaya 9:6 Yesu mwaulosi akutchedwa “Atate Wosatha.” Iye amakhala Atate Wosatha kwa anthu owomboledwa m’dziko, woyenera kupatsa choloŵa owomboledwa ameneŵa, kapena ana olera. (Mateyu 20:28; onaninso Salmo 37:18, 29.) Ichi chasonyezedwa bwino lomwe m’lonjezo lake iri: “Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, lowani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi.” Iye anawonjezeranso kuti: “Odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi.”​—Mateyu 5:5; 25:34.

Komabe, kuti dziko lapansi likhale choloŵa chaphindu, zinthu ziyenera kusinthidwa kotheratu​—kukhalitsidwa zangwiro! Liyenera kukhala dziko limene mtendere wangwiro ndi chigwirizano zikalamulira zolengedwa zonse za Mulungu. (Yesaya 11:6-9) Chizindikiro chirichonse cha kupanda ungwiro kwa munthu chiyenera kufafanizidwa, kuphatikizapo imfa. (1 Akorinto 15:25, 26) Ichi chikutanthauza kuti akufa, omwe ali mbali ya anthu owomboledwa, akayenera kuwukitsidwa. Ndi mwanjira iyi yokha mmene akakhalira ndi mwaŵi wokhala oloŵa nyumba a Kristu!​—Yohane 5:28, 29.

Motero, Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Kristu kudzakhala nyengo yachimwemwe mmene anthu mwapang’onopang’ono ‘adzamasulidwa ku ukapolo wa chibvundi’ ndi kufikira ungwiro. (Aroma 8:21) Mokondweretsa, ngakhale magwero akudziko amazindikira ichi kukhala chifuno cha zaka chikwi. Webster’s Ninth New Collegiate Dictionary (kufalitsa kwa 1985) imamasulira “millennium” (zaka chikwi) kukhala “nyengo ya chimwemwe chachikulu kapena ungwiro wa anthu.”

Kupambana Ulamuliro wa Solomo

Zaka Chikwi zaulemerero zimenezi zingafanizidwe ndi ulamuliro wa Mfumu Solomo wamtendere ndi wokhupuka wa zaka 40 pa Israyeli wakale. (1 Mafumu 4:24, 25, 29) Pamene mfumu yaikazi ya ku Seba inachezera Mfumu Solomo, iyo inati: “Idali yowonadi mbiri ija ndinaimva ine ku dziko langa ya machitidwe anu ndi nzeru zanu. Koma sindinakhulupira mawu amenewo mpaka ndafika ine kuno, ndawona ndi maso anga; ndipo tawonani, anangondiwuza dera lina lokha; nzeru zanu ndi zokoma zanu zakula pa mbiri ndinaimvayo. Odala anthu anu, odala anyamata anu akukhala nthaŵi zonse pamaso panu, akumvaimva nzeru yanu.”​—1 Mafumu 10:6-8.

Ngati mtendere, kukhupuka, ndi nzeru za ulamuliro wa zaka 40 wa Mfumu Solomo yapadziko lapansi zinapambana, inde, kuposa ndi kuŵirikiza kaŵiri, pa ziyembekezo zazikulu za mfumu yaikazi ya ku Seba, pamenepo ndiko kuti Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Mfumu Solomo yaikulu yakumwamba, Yesu Kristu, kudzapambanadi kulingalira kwamunthu! Mogwirizana ndi mawu a Yesu iyemwini, iye alidi “wakuposa Solomo.” (Mateyu 12:42) Tangoyesani kupenya ndi diso lamaganizo mikhalidwe yaumoyo wabwino koposa, yokhupuka, yamtendere, yolungama, ndi yachimwemwe padziko lapansi imene mungalingalire, ndipo simudzakhoza kufika ngakhale pa nusu ya zimene Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Kristu kuli nazo.

Kufikira Pamodzi Ndi Zaka Chikwi Zachitatu?

Zochitika zadziko chiyambire 1914 zikusonyeza kuti tikukhala mu ‘mathedwe a dongosolo iri lazinthu.’ Yesu ananenanso kuti mbadwo umene unagwirizanitsidwa ndi zochitika zonenedweratu izi “sudzatha kuchoka, kufikira zinthu zonsezi zidzachitidwa.” Nangano, kodi ichi chikutanthauza kuti Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Kristu kudzafikira pamodzi ndi zaka chikwi zachitatu?​—Mateyu 24:3-21, 34.

Yesu anachenjeza ophunzira ake kusapambanitsa. Iye anati: “Sikuli kwa inu kudziŵa nthaŵi kapena nyengo, zimene Atate anaziika m’ulamuliro wake wa Iye yekha.” (Machitidwe 1:7) Ndipo ponena za “tsiku [lenilenilo] ndi nthaŵi yake” pamene zinthuzi zikachitika, Yesu anati Atate wake yekha, Yehova Mulungu, ndiye anadziŵa. (Mateyu 24:36) Motero, Baibulo nlosachirikiza aliyense wa aneneri achiwonongeko omwe tsopano akuwonjezeka ndi mabungwe amene amaloza ku kufika kwa pakati pausiku wa Tsiku Lotsatira Chaka Chatsopano, 1999, kukhala mapeto adziko.

Komabe, zochitika zamakono zadziko zimasonyeza poyera kuti nthaŵi ya mapeto a dongosolo lazinthu loipa lamdima iri, ‘lapita’ ndikuti Zaka Chikwi za Kristu ‘zayandikira.’ (Aroma 13:12) M’malo mosumika maganizo patsiku ndi ola lenileni pamene adzabwera, tsopano ndiyo nthaŵi yophunzira ziyeneretso za Mulungu kaamba ka chipulumutso. (Yohane 17:3) Mwanjirayi mungaphunzire mmene mungakhalire pakati pa anthu amene Yesu anawauza kuti: “Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, lowani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi.” (Mateyu 25:34) Mboni za Yehova nzofunitsitsa ndipo nzokhoza kukuthandizani kukhala pakati pa awo amene adzasangalala ndi madalitso a Zaka Chikwi zopambana zikudzazo.b

[Mawu a M’munsi]

a Onani bukhu lakuti The Bible​—God’s Word or Man’s?, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

b Phunziro Labaibulo lapanyumba laulere lingakonzedwe mwakulembera ofalitsa a magazine ano.

[Mawu Otsindika patsamba 6]

“Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, lowani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena