Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Yesu Apitanso ku Yerusalemu
MWAMSANGA Yesu alinso pa msewu, kuphunzitsa kuchokera ku mzinda ndi mzinda ndi kuchokera ku mudzi ndi mudzi. Mwachiwonekere iye ali mu boma la Pereya, ku tsidya la Mtsinje wa Yordano kuchokera ku Yudeya. Koma kumene akupita ndi ku Yerusalemu.
Nthanthi ya Chiyuda yakuti kokha chiŵerengero chokhala ndi malire chiri choyenerera chipulumutso iri imene mwinamwake yasonkhezera munthu kufunsa kuti: “Ambuye, akupulumutsidwa ndi oŵerengeka kodi?” Ndi yakho lake, Yesu akukakamiza anthu kulingalira za chomwe chiri chofunikira kaamba ka chipulumutso: “Yesetsani [kumeneko ndiko kuti, kulimbanira, kapena kulimbikira] kulowa pa khomo lopapatiza.”
Kuyesetsa kolimbikira kumeneko kuli kofulumira “chifukwa anthu ambiri,” Yesu akupitiriza, “adzafunafuna kulowamo koma sadzakhoza.” Nchifukwa ninji iwo sadzakhoza? Iye akulongosola kuti pamene atauka mwininyumba natseka pa khomo ndipo anthu adzayamba kuima pa bwalo ndi kugogoda pa chitseko, ndi kunena, “Ambuye, titsegulireni ife,” iye adzanena kuti: “Sindidziŵa inu kumene muchokera. Chokani pa ine, nonsenu akuchita chosalungama!”
Awo otsekeredwa kunja mwachidziŵikire anabwera pa nthaŵi yoyenerera kokha kwa iwo eni. Koma pa nthaŵiyo chitseko cha mwaŵi chatsekedwa ndi kukhomedwa. Kuti alowe mkati iwo akanayenera kubwera mofulumira, ngakhale kuti panali pa nthaŵi imene siikanakhala yoyenerera kuchita tero. Ndithudi, chotulukapo chomvetsa chisoni chikuyembekezera awo omwe amaika pambali kupanga kulambira Yehova kukhala chifuno chawo chokulira m’moyo!
Ayuda kwa amene Yesu watumizidwa kukatumikira, kwa mbali yaikulu, anali atalephera kutenga mwaŵi wawo wozizŵitsa koposa wa kulandira makonzedwe a Mulungu kaamba ka chipulumutso. Chotero Yesu akunena kuti iwo adzalira ndi kukukuta mano pamene adzataidwa kunja. Ku mbali ina, anthu ochokera “ku m’mawa ndi kumadzulo, ndi ochokera kumpoto ndi kum’mwera,” inde, ochokera ku mitundu yonse, “adzakhala pansi mu ufumu wa Mulungu.”
Chotero, pamene Yesu akupitiriza: “Alipo akuthungo [osakhala ayuda onyozedwa, limodzinso ndi Ayuda oponderezedwa] amene adzakhala oyamba, ndipo alipo oyamba [Ayuda oyanjidwa m’zakuthupi ndi m’chipembedzo] adzakhala akuthungo.” Kukhala wakuthungo kumatanthauza kuti aulesi, osayamikira oterowo sadzakhala mu Ufumu wa Mulungu nkomwe.
Afarisi tsopano akubwera kwa Yesu ndi kunena kuti: “Tulukani chokani kuno, chifukwa Herode [Antipas] afuna kupha inu.” Chingakhale chakuti Herode iyemwiniyo anayambitsa mphekeserayi kumpangitsa Yesu kuthaŵa kuchoka m’gawolo. Herode angakhale akuwopa kuphatikizidwa mu imfa ya mneneri wina wa Mulungu monga mmene iye analiri m’kuphedwa kwa Yohane Mbatizi. Koma Yesu akuuza Afarisiwo kuti: “Pitani kauzeni nkhandweyo, ‘Tawonani! Nditulutsa ziwanda nditsiriza machiritso lero ndi m’mawa, ndipo mkucha nditsirizidwa.’”
Pambuyo pa kumaliza ntchito yake kumeneko, Yesu akupitiriza ulendo wake kulinga ku Yerusalemu chifukwa, monga mmene iye akulongosolera, “sikuloledwa kuti mneneri awonongeke kunja kwake kwa Yerusalemu.” Nchifukwa ninji chiyenera kuyembekezeredwa kuti Yesu akaphedwa m’Yerusalemu? Chifukwa chakuti Yerusalemu uli mzinda waukulu, kumene Bwalo Lamilandu Lapamwamba la Chiyuda la ziwalo 71 liri ndi kumene nsembe za nyama zimaperekedwa. Chotero, sichikakhala chovomerezedwa kwa “Mwanawankhosa wa Mulungu” kuphedwera kwina kuli konse koma m’Yerusalemu.
“Yerusalemu, Yerusalemu, iwe wakupha aneneri ndi wakuponya miyala iwo atumidwa kwa iwe,” Yesu akuchitira chisoni tero, “kaŵirikaŵiri ndinafuna kusonkhanitsa ana ako monga ngati thadzi ndi anapiye ake m’mapiko ake, ndipo simunafunai! Onani! Nyumba yanu isiyidwa kwa inu yabwinja.” Chifukwa cha kukana Mwana wa Mulungu, mtunduwo waŵeruzidwa!
Pamene Yesu akupitiriza kulinga ku Yerusalemu, iye akuitanidwa kunyumba ya wolamulira wa Afarisi. Pali pa Sabata, ndipo anthu akumupenyerera iye mosamalitsa, popeza kuti pali munthu yemwe akuvutika mbulu, kuwunjikana kwa madzi mwinamwake m’mikono ndi miyendo yake. Yesu akulankhula ndi afarisiwo ndi akatswiri pa Chilamulo omwe alipo, akumafunsa kuti: “Kodi kuloledwa tsiku la sabata kuchiritsa kapena ayi?”
Palibe aliyense amene akuyankha. Chotero Yesu akuchiritsa munthuyo ndi kumuuza iye apite. Kenaka iye akufunsa: “Ndani wa inu, [mwana] wake kapena ng’ombe yake itagwa m’chitsime, ndipo sadzaitulutsa pomwepo pa tsiku la sabata kodi?” Kachiŵirinso, palibe amene akuyankha. Luka 13:22–14:6; Yohane 1:29.
◆ Nchiyani chimene Yesu akusonyeza kuti chiri chofunikira kaamba ka chipulumutso, ndipo nchifukwa ninji ambiri atsekeredwa kunja?
◆ Ndani omwe ali “akuthungo” omwe amakhala oyamba, ndi “oyamba” omwe amakhala akuthungo?
◆ Nchifukwa ninji mothekera chinanenedwa kuti Herode anafuna kupha Yesu?
◆ Nchifukwa ninji sichiri chololedwa kwa mneneri kuphedwa kunja kwa Yerusalemu?