Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 4/15 tsamba 4-6
  • Kodi Mulungu Amamvetsera Pamene Mupemphera?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mulungu Amamvetsera Pamene Mupemphera?
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mapemphero Amene Anamvedwa
  • Mayankho a Mapemphero
  • Khalani ndi Chidaliro Chakuti Mulungu Amamvetsera
  • Kodi Ndimapemphero Ayani Omwe Amayankhidwa?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Mapemphero Amene Amayankhidwa
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Pemphero Lingakuthandizeni Kukhala pa Ubwenzi ndi Mulungu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Kodi ndi Mapemphero Andani Amene Amayankhidwa?
    Nsanja ya Olonda​—1990
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 4/15 tsamba 4-6

Kodi Mulungu Amamvetsera Pamene Mupemphera?

MKULU wantchito amasankha ngati angapatse wina ntchito kapena kuichita yekha. Mofananamo, Mfumu Yolamulira ya chilengedwe chonse imadzisankhira kuti ndi kumlingo wotani umene ingadziloŵetsemo m’nkhani iliyonse. Malemba amaphunzitsa kuti Mulungu anasankha kudziloŵetsamo yekha m’mapemphero athu ndipo chotero akutilamula kuwalunjikitsa kwa iye.​—Salmo 66:19; 69:13.

Chosankha cha Mulungu pankhaniyi chimasonyeza chikondwerero chake chaumwini m’mapemphero a atumiki ake aumunthu. Mmalo molefula anthu ake kuti asamfikire ndi nkhaŵa zawo zonse, amawalimbikitsa kuti: “Pempherani kosaleka,” ‘limbikani chilimbikire m’kupemphera,’ ‘umsenze Yehova nkhaŵa zako,’ ‘tayani pa [Mulungu] nkhaŵa yanu yonse.’​—1 Atesalonika 5:17; Aroma 12:12; Salmo 55:22; 1 Petro 5:7.

Ngati Mulungu sanafune kupereka chisamaliro ku mapemphero a atumiki ake, iye sakadakonza njira imeneyo yomfikira ndi kulimbikitsa kuigwiritsira ntchito mwaufulu. Pamenepo, kusankha kwa Mulungu kukhala wofikirika kwa anthu ake, kuli chifukwa chimodzi chokhalira ndi chidaliro kuti amamvetseradi. Inde, amalingalira pemphero lirilonse la atumiki ake.

Sitiyenera kunyalanyaza mfundo yakuti Baibulo limanena mosabisa kuti Mulungu amamvetsera pemphero. Mwachitsanzo, mtumwi Yohane analemba kuti: ‘Uku ndi kulimbika mtima kumene tiri nako kwa iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera.’ (1 Yohane 5:14) Mfumu Davide anatcha Yehova Mulungu “Wakumva pemphero” ndipo mwachidaliro anati: ‘Amamva mawu anga.’​—Salmo 55:17; 65:2.

Chotero ngakhale kuti kupemphera kwenikweniko kuli ndi mapindu, Malemba amasonyeza kuti zambiri zimaloŵetsedwamo pamene munthu wolungama apemphera. Wina amakhala akumvetsera. Ndipo Mulungu ndiye womvetserayo.​—Yakobo 5:16-18.

Mapemphero Amene Anamvedwa

M’Baibulo muli nkhani zambiri za anthu amene mapemphero awo anamvedwa ndi kuyankhidwa ndi Mulungu. Zokumana nazo zawo zimatsimikizira bwino lomwe kuti mapindu a pemphero amaloŵetsamo zoposa chithandizo chaumwini chopezedwa mwakuzindikira ndi kufotokoza malingaliro a munthuwe. Amapyola zoyesayesa zaumwini za munthuyo zogwirizana ndi mapemphero ake.

Mwachitsanzo, pamene anayang’anizana ndi chiŵembu cha Abisalomu chofuna kulanda ufumu wa Israyeli, Mfumu Davide anapemphera kuti: “Yehova, musandulize uphungu wa Ahitofeli [mlangizi wa Abisalomu] ukhale wopusa.” Silinalitu pempho laling’ono, popeza kuti ‘uphungu wa Ahitofeli . . . unali monga ngati munthu anafunsira mawu kwa Mulungu; uphungu wonse wa Ahitofeli unali wotere.’ Pambuyo pake Abisalomu anakana uphungu woperekedwa ndi Ahitofeli wogwetsera Mfumu Davide. Chifukwa? ‘Kunaikidwa ndi Yehova kutsutsa uphungu wabwino wa Ahitofeli kuti Yehova akamtengere Abisalomu choipa.’ Mowonekeratu, pemphero la Davide limamvedwa.​—2 Samueli 15:31; 16:23; 17:14.

Mofananamo, atatha kupembedzera Mulungu kaamba ka chilanditso ku matenda ake aakulu, Hezekiya anachira. Kodi zidangochitika chifukwa cha kutonthozedwa maganizo kwa Hezekiya monga chotulukapo chakupemphera? Ndithudi ayi! Uthenga womwe Yehova anatumiza kwa Hezekiya kudzera mwa mneneri Yesaya unali wakuti: ‘Ndamva pemphero lako, ndapenya misozi yako; tawona, ndidzakuchiritsa.’​—2 Mafumu 20:1-6.

Danieli, amene pemphero lake linayankhidwa mochedwerako kuposa mmene anayembekezera, anatsimikiziridwa ndi mngelo wa Yehova kuti: ‘Mawu ako anamveka.’ Mapemphero a anthu ena, monga ngati aja a Hana, ophunzira a Yesu, ndi kazembe wankhondo Korneliyo, anayankhidwa m’njira zimene sizingagwirizanitsidwe ndi luso la anthu lokha. Pamenepo, Baibulo limaphunzitsa momvekera kuti mapemphero ogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu amalandiridwa, kumvedwa, ndi kuyankhidwa ndi Mulungu.​—Danieli 10:2-14; 1 Samueli 1:1-20; Machitidwe 4:24-31; 10:1-7.

Koma kodi Mulungu amayankha motani mapemphero a atumiki ake okhulupirika lerolino?

Mayankho a Mapemphero

Mapemphero otchulidwa pamwambapawa anayankhidwa mwanjira zodabwitsa, ngakhale zozizwitsa. Komabe, kumbukirani kuti ngakhale m’nthaŵi za Baibulo, mayankho ambiri a mapemphero kaŵirikaŵiri sanazindikiridwe. Izi zinachitika chifukwa chakuti anatumikira kupereka nyonga yamakhalidwe ndi chiunikiro, kutheketsa atumiki a Mulungu kumamatira ku njira yolungama. Makamaka kwa Akristu, mayankho a mapemphero analoŵetsamo nkhani zimene kwakukulukulu zinali zauzimu, osati machitidwe owonekera kapena amphamvu.​—Akolose 1:9.

Choncho musakhumudwe ngati nthaŵi zina mapemphero anu samayankhidwa m’njira imene mumayembekezera kapena kufuna. Mwachitsanzo, mmalo mochotsa chiyeso, Mulungu angasankhe kukupatsani “ukulu woposa wamphamvu” kuti muchipirire. (2 Akorinto 4:7; 2 Timoteo 4:17) Sitiyenera konse kuchepsa phindu la mphamvu yoteroyo, ndiponso sitiyenera kugamula kuti Yehova sanayankhe konse pemphero lathu.

Talingalirani nkhani ya Mwana wa Mulungu weniweniyo, Yesu Kristu. Podera nkhaŵa kuti asamwalire monga wochita mwano, Yesu anapemphera kuti: ‘Atate, mukafuna inu, chotsani chikho ichi pa ine.’ Kodi pempheroli linamvedwa moyanja ndi Mulungu? Inde, monga momwe kwatsimikiziridwa pa Ahebri 5:7. Yehova sanachotsere Mwana wake kufunika kwa kufa pamtengo wozunzirapo. Mmalomwake, ‘anamuwonekera iye mngelo wa kumwamba namlimbitsa iye.’​—Luka 22:42, 43.

Kodi linali yankho lodabwitsa, lozizwitsa? Lingakhaledi tero kwa aliyense wa ife! Koma kwa Yehova Mulungu, magwero a mphamvu zoterozo, ichi sichinali chozizwitsa. Ndipo kuyambira moyo wake wakale kumwamba, Yesu anadziŵa za zochitika zakale kumene angelo anawonekera kwa anthu. Choncho kuwonekera kwa mngelo sikukadakhala ndi chiyambukiro chodabwitsa pa iye monga momwe chingachitire kwa ife. Komabe, mngelo ameneyu, yemwe mwachidziŵikire Yesu anamdziŵa kuyambira kukhalapo Kwake asanakhale munthu, anamthandiza kumlimbikitsa Iye kaamba ka chiyeso chomwe chinali kutsogolo.

Poyankha mapemphero a atumiki ake okhulupirika lerolino, kaŵirikaŵiri Yehova amapereka nyonga yofunikira kuti tipirire. Chichilikizo chimenechi chingadzere m’chilimbikitso chochokera kwa alambiri anzathu amene timadziŵana nawo. Kodi aliyense wa ife akafuna kukana chilimbikitso choterocho, mwinamwake kugamulapo kuti popeza kuti atumiki anzathu sanakumanepo ndi ziyeso zofanana ndi zathu, iwo sangathe kutilimbikitsa? Yesu akadakhoza kulingalira motero za mngelo amene anamuwonekera. Mmalomwake, analandira chilimbikitsocho kukhala yankho la Yehova la pemphero lake ndipo anakhoza kukwaniritsa mokhulupirika chifuniro cha Atate wake. Nafenso tikafuna kulandira mwachisomo nyonga imene Mulungu amapereka poyankha mapemphero athu. Kumbukiraninso kuti nyengo zoterozo za kupirira moleza mtima kaŵirikaŵiri zimatsatiridwa ndi madalitso osasimbika.​—Mlaliki 11:6; Yakobo 5:11.

Khalani ndi Chidaliro Chakuti Mulungu Amamvetsera

Komabe musataye chidaliro m’kugwira ntchito kwa pemphero ngati simuyankhidwa m’njira yoyenera. Mayankho a mapemphero ena, monga ngati aja opempha mpumulo ku chisautso kapena mathayo owonjezereka muutumiki wa Mulungu, angafunikire kudikirira nthaŵi imene Mulungu akudziŵa kuti njoyenera ndiponso yabwino koposa. (Luka 18:7, 8; 1 Petro 5:6) Ngati mukupempherera nkhani yodetsa nkhaŵa kwambiri kwa inuyo, msonyezeni Mulungu mwakuumirira kuti chikhumbo chanu nchachikulu, cholinga chanu nchoyera ndi chowona. Yakobo anasonyeza mzimu umenewu pamene, pambuyo polimbana mwamphamvu kwa nthaŵi yaitali ndi mngelo, anati: “Sindidzakuleka iwe kuti umuke, ukapanda kundidalitsa ine.” (Genesis 32:24-32) Tiyenera kukhala ndi chidaliro chofananacho kuti ngati tipitiriza kupempha, tidzalandira dalitso panthaŵi yake.​—Luka 11:9.

Lingaliro lomalizira. Kumvedwa ndi Mfumu ya chilengedwe chonse kuli mwaŵi wapadera. Chifukwa chake, kodi timamvetsera mosamalitsa pamene Yehova Mulungu, kudzera m’Mawu ake, alankhula nafe za zofuna zake? Pamene mapemphero athu akutifikitsa kufupi kwenikweni ndi Mlengi wathu, tidzafuna kumvetsera mosamalitsa zonse zimene amatiuza.

[Chithunzi patsamba 6]

Mulungu amamvetsera mapemphero. Kodi timamvetsera kwa iye kudzera m’Mawu ake?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena