Zimene Tiyenera Kuchita Kuti Tipulumuke
KODI nchifukwa ninji tifunikira kupulumuka? Chifukwa chakuti tonsefe timavutika ndi zotulukapo zomvetsa chisoni za kupanda uchimo: ungwiro, kuwawa, matenda, chisoni, ndipo pomalizira pake imfa. Mtumwi Paulo analongosola kuti izi ziri choncho chifukwa chakuti kholo lathu loyambirira Adamu anapandukira lamulo la Mulungu. Paulo analemba kuti: “Monga uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.” (Aroma 5:12) Kodi nchifukwa ninji chimo la Adamu limapangitsa imfa kufalikira kwa anthu onse? Ndithudi, izi zinali choncho chifukwa cha kuchitidwa kwa zinthu mwachibadwa.
Pamene Adamu anachimwa, iye anaweruzidwira ku imfa mogwirizana ndi lamulo laumulungu. Zimenezi zinali ponse paŵiri zolungama ndi zoyenerera. Zinali zolungama, popeza kuti moyo suli choyenera koma mphatso yochokera kwa Mulungu. Mwa kuchimwa dala, Adamu anataya mwaŵi wonse wa mphatso imeneyo. (Aroma 6:23) Kuweruzidwira kwa Adamu ku imfa kunali koyenerera chifukwa chakuti palibe chirichonse chopanda ungwiro chomwe chingaloledwe kupulumuka ndi kuipitsa chilengedwe chonse ku nthaŵi yosadziŵika. Chotero, pamene Adamu anachimwa, anayamba kufa ndipo analibenso moyo wangwiro, wopanda uchimo wakuupereka kwa ana ake monga cholowa. Iye akanawapatsa kokha moyo woipitsidwa ndi kupanda ungwiro ndi chimo.—Aroma 8:18-21.
Komabe, sitiyenera kuiwala kuti kuli kokha chifukwa cha kukoma mtima kwapadera kwa Mulungu kuti tiridi ndi moyo kukhalapo waufupi umene tiri nawo lerolino. (Yobu 14:1) Mulungu sanali wokakamizika kulola Adamu ndi Hava kukhala ndi ana iwo asanafe. Iye anawalola iwo kutero kotero kuti atsimikizire kuti anthu ena opanda ungwiro akakhoza kuchirikiza ulamuliro wa Mulungu mwa kusunga umphumphu wawo kwa iye. Ndiponso, Mulungu analola izi, chifukwa chakuti anadziŵa kuti m’kupita kwa nthaŵi iye akawombola, kapena kupulumutsa, mbadwa zolabadira za opanduka oyambirirawo, Adamu ndi Hava. Koma motani?
Makonzedwe a Chipulumutso
Yehova Mulungu sakanangokhazika pambali chiweruzo chake cholungama. Iye sangaiwale dala chimo loyambirira la Adamu ndi zonse zimene anthu awonjezerapo kuyambira nthaŵi imeneyo. Ngati Mulungu akananyalanyaza malamulo ake olungama, zimenezi zikanachepetsa ulemu kaamba ka dongosolo lake lonse lachiweruzo cholungama ndi chidaliro mu ilo. Tangoyerekezerani mfuu zimene zikanamvedwa ngati, chifukwa cha lingaliro la iye mwini, woweruza wina waumunthu analola dala mpandu kumasulidwa popanda chilango. Komabe, moyenerera woweruza wachifundo angakhoze kulinganiza kulipiridwa kwa faindi mogwirizana ndi lamulo m’malo mwa munthu waliwongoyo ndi munthu wina amene ali wofunitsitsa kutero. Mwapang’ono, zimenezi ndizo zimene Mulungu anatichitira.
Yehova analinganiza kuti Mwana wa iye yekha, Yesu Kristu, apereke moyo wake wangwiro waumunthu kuloŵa m’malo mwa moyo wangwiro umene Adamu anautaya. Mofunitsitsa Yesu anasenza chilango cha machimo athu—imfa. (Yesaya 53:4, 5; Yohane 10:17, 18) Baibulo likunena kuti: “Mwana wa munthu anadza . . . kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.” (Mateyu 20:28; 1 Timoteo 2:6) Palibe wina aliyense akanachita chimenechi. Yesu anali wapadera m’chakuti anabadwa wopanda chimo nakhalabe wangwiro, munthu wopanda chimo kufikira pa imfa yake yeniyeniyo. (Ahebri 7:26; 1 Petro 2:22) Kukhulupirika kwake kufikira imfa kunamtheketsa kulipira chilango chokhazikitsidwa mwa malamulo kaamba ka machimo athu.
Kumbukirani, kuti Mulungu, Woweruza Wamkulu, sali wokakamizika konse kumasula aliyense. Amawona moyo wangwiro waumunthu woperekedwa nsembe wa Yesu monga malipiro a ngongole imene tiri nayo kaamba ka uchimo. Komatu Yehova Mulungu sadzagwiritsira ntchito zimenezi kwa ochimwa osalapa, osayamikira, ndi ochimwira dala. M’malo mwa kulonjeza makonzedwe a kukhululukira anthu onse kapena chipulumutso cha munthu aliyense, Baibulo limakhazikitsa ziyeneretso zimene ziyenera kufikiridwa kuti tipulumutsidwe kuchokera ku ziyambukiro za chimo lacholoŵa.
Ziyeneretso za Chipulumutso
Chotero, pamenepa, kodi nchiyani chimene chiri chofunika kaamba ka chipulumutso? Chofunika chachikulu ndicho chija chimene mtumwi Paulo analongosola kwa wosunga ndende wa ku Filipi: “Ukhulupirire Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka.” (Machitidwe 16:31) Kulandiridwa kowona mtima kwa mwazi wokhetsedwa wa Yesu kuli kofunika ngati titi tipulumutsidwe. Ndipo kodi chipulumutso chidzatanthauzanji kwa ife? Yesu anasonyeza yankho pamene anati: “Ndipo ine ndizipatsa moyo wosatha; ndipo sizidzawonongeka ku nthaŵi yonse.” (Yohane 10:28) Kwa ambiri, chipulumutso chidzatanthauza moyo wosatha pa dziko lapansi lobwezeretsedwa ku paradaiso wangwiro. (Salmo 37:10, 11; Chibvumbulutso 21:3, 4) Komabe, ponena za “kagulu ka nkhosa,” chidzatanthauza kulamulira ndi Yesu mu Ufumu wake wakumwamba.—Luka 12:32; Chibvumbulutso 5:9, 10; 20:4.
Ena amalingalira kuti kukhulupirira Yesu ndiko mapeto a nkhaniyo. “Pali chinthu chimodzi chokha chimene aliyense afunikira kuchita kuti apite kumwamba,” ikutero trakiti ina ya chipembedzo. “Icho chiri, kulandira Yesu Kristu monga Mpulumutsi wake, gonjerani kwa Iye monga Mbuye ndi Ambuye, ndi kuvomereza Iye poyera monga wotero pamaso pa dziko lonse.” Chotero, ambiri amakhulupirira kuti chokumana nacho cha kutembenuka kwadzidzidzi kwa maganizo, ndicho chokha chimene timafunikira kuti titsimikizire za moyo wosatha. Komabe, kusumika maganizo pa chiyeneretso chimodzi chokha kaamba ka chipulumutso mosaphatikizapo zofunika zina kuli kofanana ndi kuŵerenga chiyeneretso chofunika chimodzi m’pangano ndi kunyalanyaza zina zonse.
Zimenezi zinawonekera kwambiri pamene timvetsera ku ndemanga za ena amene pa nthaŵi ina analingalira kuti kusonyeza chikhulupiriro mwa Yesu ndizo zokha zimene anafunikira kuti apulumutsidwe. Bernice akuti: “Ndinaleredwera m’Tchalitchi cha Brethren, koma ndinayamba kudabwa, kuti ngati moyo wosatha unali wodalira pa Yesu yekha, nchifukwa ninji iye mwini adanena kuti: ‘Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe inu Mulungu wowona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.’”—Yohane 17:3.
Kwa zaka zisanu ndi zinayi Norman anali wokhutiritsidwa kuti anali wopulumutsidwa. Koma kenaka iye anawona kuti zambiri zinali zofunikira kuposa kutengeka maganizo kwakuti Yesu Kristu anali Mpulumutsi wake. “Ndinawona kuchokera m’Baibulo kuti sikunali kokwanira kungovomereza kwa Mulungu kuti ndife ochimwa ndi ofunikira chipulumutso,” iye amatero. “Tifunikiranso kuchita ntchito zoyenera kulapa.”—Mateyu 3:8; Machitidwe 3:19.
Nzowona kuti, kukhulupirira Yesu kuli kofunika koposa kuti tipeze chipulumutso, komatu zambiri zikufunikira. Yesu analankhula za ena amene ananena kuti anamkhulupirira ndi kuchitadi “ntchito zamphamvu” m’dzina lake. Koma iye sanawazindikire iwo. Nchifukwa ninji? Chifukwa chakuti iwo anali “akuchita kusayeruzika” ndipo sanachite chifuniro cha Atate wake. (Mateyu 7:15-23) Wophunzira Yakobo amatikumbutsa za kufunika kwa “kukhala akuchita mawu, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha.” Iye anatinso: “Ukhulupirira iwe kuti Mulungu ali mmodzi; uchita bwino; ziwanda zikhulupiriranso, ndipo zinthunthumira. . . . Chikhulupiriro chopanda ntchito chiri chakufa.”—Yakobo 1:22; 2:19, 26.
Komabe, ena, amanena kuti ndiiko komwe awo amene ali opulumutsidwa mowonadi amachita zinthu zonsezi. Koma kodi chizoloŵezi chimenecho chikugwiradi ntchito? Denis, amene ‘analandira Yesu’ pamene anali kamnyamata, akuti: “Anthu ‘opulumutsidwa’ amene ndawadziŵa samawona kufunika kokulira kwa kusanthula Malemba chifukwa chakuti amaganiza kuti iwo ali nazo kale zonse zimene afunikira kaamba ka chipulumutso.” Ndithudi, chinyengo ndi machitachita osakhala Achikristu za ambiriwo odzinenera kukhala opulumutsidwa apangitsa nkhani yonse ya ku chipulumutso kukhala yochititsa manyazi.
Komabe, ena amawumirira kuti Malemba amati: “Wakukhulupirira Mwanayo ali nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:36, King James Version) Chotero, iwo amamaliza mwakunena kuti pamene inu mulandira Ambuye Yesu Kristu monga Mpulumutsi wanu, simungatayikenso konse. “Wopulumutsidwa kamodzi, wapulumutsidwa nthaŵi zonse” ndiyo silogani yawo. Koma kodi zimenezo ndizo zimene Malemba amanenadi? Kuti tiyankhe izi, tifunikira kupenda zonse zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi. Sitikafuna ‘kudzinyenga tokha’ mwa kuŵerenga mbali zoyanjidwa zokha za Mawu a Mulungu.
“Wopulumutsidwa Kamodzi, Wapulumutsidwa Nthaŵi Zonse”?
Tawonani chenjezo lowuziridwa la wophunzira Yuda. Iye analemba kuti: “Okondedwa, pakuchita changu chonse chakukulemberani za chipulumutso cha ife tonse, ndafulumidwa mtima ine kukulemberani ndi kudandaulira kuti mulimbanetu chifukwa cha chikhulupiriro chapatsidwa kamodzi kwa oyera mtima.” (Yuda 3) Kodi nchifukwa ninji Yuda analemba izi? Chifukwa chakuti anadziŵa kuti Akristu alionse pa okha akakhozabe kutaya ‘chipulumutso chimene ali nacho chopatsidwa kwa onse.’ Iye anapitiriza kunena kuti: “Ndifuna kukukumbutsani . . . kuti [Yehova, NW], atapulumutsa mtundu wa anthu [Aisrayeli] ndi kuwatulutsa m’dziko la Igupto, anawononganso iwo osakhulupirira.”—Yuda 5.
Chenjezo la Yuda likakhala lopanda tanthauzo ngati Akristu sanayang’anizane ndi ngozi yofanana ndi ya Aisrayeli amenewo. Yuda sanali kukaikira phindu la nsembe ya Yesu. Nsembe imeneyo yatipulumutsa kuchokera ku uchimo wa Adamu, ndipo Yesu adzatetezera awo osonyeza chikhulupiriro mwa iye. Palibe munthu amene angawatsomphole m’dzanja lake. Komatu tingataye chitetezo chimenecho. Motani? Mwa kuchita zimene zinachitidwa ndi Aisrayeli ambiri amene anapulumutsidwa mu Igupto. Ife tingasankhe dala kusamvera Mulungu.—Deuteronomo 30:19, 20.
Tayerekezerani kukhala mukupulumutsidwa kuchokera pa nsanja yoyaka moto. Talingalirani mpumulo umene mukanakhala nawo pamene munatengedwa wosavulazika kuchokera panyumbapo ndipo wokupulumutsaniyo nanena kuti: “Tsopano muli wosungika.” Inde, mungakhale mutapulumutsidwa kuchokera ku imfa yotsimikizirika. Koma kodi nchiyani chikanachitika ngati munasankha kubwerera ndi kukalowa mnyumbayo kaamba ka chifukwa china chopanda pake? Moyo wanu ukanakhalanso pa ngozi.
Akristu ali mu mkhalidwe wopulumutsidwa. Ali ndi chiyembekezo cha moyo wosatha chifukwa chakuti ali mumkhalidwe wachiyanjo pamaso pa Mulungu. Monga kagulu, chipulumutso chawo kuchokera ku uchimo wa Adamu ndi zotulukapo zake zonse chiri chotsimikizirika. Koma aliyense payekha iwo adzapulumutsidwira ku moyo wosatha kokha ngati apitirizabe kumamatira ku zofunika zonse za Mulungu. Yesu anagogomezera zimenezi pamene anadziyerekezera ndi mtengo wa mphesa ndipo ophunzira ake monga nthambi za mphesawo. Iye anati: “Nthambi iriyonse ya mwa ine yosabala chipatso, [Mulungu] aichotsa . . . Ngati wina sakhala mwa ine, watayika kunja monga nthambi, nafota; ndipo azisonkhanitsa nazitaya ku moto nazitentha.” (Yohane 15:2, 6; Ahebri 6:4-6) Awo otaya chikhulupiriro mwa Yesu amatayanso moyo wosatha.
“Iye Wakulimbika Chilimbikire . . . Adzapulumuka”
Inde, pali unyinji wa zinthu zosiyanasiyana zophatikizidwa m’kupulumutsidwa. Tiyenera kuloŵetsa chidziŵitso cholongosoka cha zifuno za Mulungu ndi njira yake ya chipulumutso. Ndiyeno tiyenera kusonyeza chikhulupiriro mwa Mkulu wa chipulumutso, Yesu Kristu, ndi kuchita chifuniro cha Mulungu mbali yonse yotsala ya moyo wathu. (Yohane 3:16; Tito 2:14) Chipulumutso chiri chotsimikizirika kwa amene atsatira njira imeneyi. Koma kumaphatikizapo kupirira kufikira kumapeto a moyo wathu kapena a dongosolo iri la zinthu. Kokha “iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.”—Mateyu 24:13.
Limodzi ndi ena m’banja lake, wosunga ndende wa ku Filipi analabadira mwachiyanjo uthenga wa chipulumutso umene Paulo ndi Sila analalikira. “Nabatizidwa pomwepo, iye ndi a pabanja pake.” (Machitidwe 16:33) Tingatenge kachitidwe kotsimikizirika kofananako. Mwakutero, tidzaloŵa mu unansi wa ponda apo mpondepo ndi wodalitsika ndi Yehova Mulungu ndi Mwana wake, Yesu Kristu, ndipo tingakhale ndi chidaliro chotheratu mu makonzedwe aumulungu a chipulumutso. Wosunga ndendeyo wa ku Filipi “[a]nasangalala kwambiri, pamodzi ndi a pabanja pake, atakhulupirira Mulungu.” (Machitidwe 16:34) Njira yoteroyo idzatipangitsanso ife ‘kusangalala kwambiri.’
[Chithunzi patsamba 7]
Kodi nchiyani chimene chingachitike ngati mubwerera kukaloŵa m’nyumba yoyaka moto pambuyo pa kupulumutsidwa?