-
“Liwu Lawo Linatulukira ku Dziko Lonse Lapansi”Nsanja ya Olonda—1989 | January 1
-
-
MU SALMO 19, Davide akulemekeza ulemerero wa chilengedwe cha kuthupi cha Mulungu ndi kupitiriza kulongosola chiyamikiro chotentha cha lamulo la Yehova, zokumbutsa, malangizo, malamulo, ndi maŵeruzo. Mtumwi Paulo nayenso anasonyeza chiyamikiro kaamba ka zinthu zimenezi. Iye anagwira mawu kuchokera ku salmo limeneli ndi kufutukula kugwiritsira ntchito kwake ku ntchito yofunika koposa ya Akristu owona. Za izi iye ananena kuti: “Liwu lawo linatulukira ku dziko lonse lapansi, ndi maneno awo ku malekezero okhalamo anthu.”—Aroma 10:18.
“Maneno” amenewa ali chodetsa nkhaŵa cha moyo ndi imfa kwa mtundu wonse wa anthu lerolino, popeza kuti ziŵeruzo za Yehova ziri pafupi kuperekedwa pa dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu loipa pa dziko lapansi. (Zefaniya 2:2, 3; 3:8) Mtundu wa anthu ndithudi ufunikira kudziŵa ponena za mbiri yabwino ya Ufumu wa Yehova. Kulikonse kumene mungayang’ane lerolino, pali kusagwirizana, kusayeruzika, upandu, chisembwere, nyumba zosweka. Oh, inde, pali kulankhula kwa mtendere, koma mphamvu zazikuluzo zikupitiriza kumangirira zida zomwe ziri zapamwamba koposa, pamene ziwalo za ‘gulu la nyukliya’ zikupitirizabe kufutukukira ku mitundu yochulukira koposa. Mikhalidwe pa dziko lapansi imayenerera mowonekera bwino “masiku otsiriza” olongosoledwa ndi Paulo pa 2 Timoteo 3:1-5.
-
-
“Liwu Lawo Linatulukira ku Dziko Lonse Lapansi”Nsanja ya Olonda—1989 | January 1
-
-
Mwachimwemwe, Yehova watumiza Mboni zake kudziŵitsa anthu kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi ndipo kuti udzatanthauza chipulumutso ku moyo wosatha kaamba ka awo omafika ku kudziŵa Mulungu ndi Mwana wake, Yesu Kristu. (Yesaya 43:10, 12; Luka 21:25, 26, 31; Yohane 17:3) Mbiri yabwino imeneyi ikumveketsedwa “ku dziko lonse lapansi.”
-