Chothetsa Nzeru cha Maphunziro a Zaumulungu
“LINGALIRO la kusafa kwa mzimu ndi kukhulupirira m’kuuka kwa akufa . . . zili zikhulupiriro ziŵiri zosiyana kwambiri, pa zimenezo chimodzi chiyenera kusankhidwa.” Mawu ameneŵa a Philippe Menoud amafotokoza mwachidule chothetsa nzeru choyang’anizana ndi akatswiri a zaumulungu Achiprotestanti ndi Achikatolika cha mkhalidwe wa akufa. Baibulo limanena za chiyembekezo cha chiukiriro pa “tsiku lomaliza.” (Yohane 6:39, 40, 44, 54) Koma chiyembekezo cha okhulupirira ambiri, akutero katswiri wina wa zaumulungu Gisbert Greshake, “chazikidwa pa kusafa kwa mzimu, umene umasiyana ndi thupi pa imfa ndi kubwerera kwa Mulungu, pamene kuli kwakuti chiyembekezo cha chiukiriro chazimiririka kwakukulukulu, ngati kusali kotheratu.”
Chifukwa cha zimenezo, pakubuka vuto lalikulu kwambiri, akufotokoza motero Bernard Sesboüé: “Kodi mkhalidwe wa akufa ngwotani mkati mwa ‘nyengo’ ya pakati pa imfa yawo ya thupi ndi chiukiriro chotsiriza?” Funso limenelo likuonekera kukhala lalikulu pa mkangano wa zaumulungu m’zaka zingapo zapitazo. Kodi nchiyani chimene chinachititsa kuti lifunsidwe? Ndipo chofunika kwambiri nchakuti, kodi chiyembekezo chenicheni cha akufa nchotani?
Magwero ndi Kukula kwa Chothetsa Nzerucho
Akristu oyamba anazindikira bwino lomwe nkhaniyo. Anadziŵa kuchokera m’Malemba kuti akufa sadziŵa kanthu kalikonse, pakuti Malemba Achihebri amati: “Amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi, . . . mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziŵa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.” (Mlaliki 9:5, 10) Akristu amenewo anayembekezera chiukiriro kuchitika mkati mwa “kukhalapo kwa Ambuye” kwamtsogolo. (1 Atesalonika 4:13-17, NW) Sanayembekezere kuti akakhala amoyo kumalo ena pamene akayembekezera nthaŵi imeneyo. Joseph Ratzinger, yemwe pakali pano ali woyang’anira wa Vatican Congregation for the Doctrine of the Faith, akunena kuti: “Panalibe umboni umene unalipo wa chiphunzitso m’Tchalitchi chakale pankhani ya kusafa kwa mzimu.”
Komabe, Nuovo dizionario di teologia, imafotokoza kuti poŵerenga zolemba za Abambo Atchalitchi, zonga za Augustine kapena Ambrose, “timazindikira za kanthu kena katsopano ponena za mwambo wa Baibulo—kubuka kwa chiphunzitso cha Chigiriki chonena za kutha kwa dziko, chosiyana kwambiri ndi cha Ayuda ndi Akristu.” Chiphunzitso chatsopano chimenechi chinazikidwa pa “kusafa kwa mzimu, pakupatsidwa chiweruzo kwa aliyense payekha ndi mphotho kapena chilango imfa itangochitika.” Motero, funso lonena za “mkhalidwe wa pakati” linadzutsidwa: Ngati mzimu umapulumuka imfa ya thupi, kodi nchiyani chimene chimauchitikira pamene ukuyembekezera chiukiriro pa “tsiku lomaliza”? Chimenechi chili chothetsa nzeru chimene akatswiri a zaumulungu alimbana nacho kuti achidziŵe.
M’zaka za zana lachisanu ndi chimodzi C.E., Papa Gregory I anatsutsa kuti pa imfa mizimu imapita kumalo awo olinganizidwiratu nthaŵi yomweyo. Papa John XXII wa m’zaka za zana la 14 anali wotsimikiza kuti akufa akalandira mphotho yawo pa Tsiku Lachiweruzo. Komabe, Papa Benedict XII anatsutsa womuyambirira wake. M’kalata yaupapa yotchedwa Benedictus Deus (1336), iye anagamula kuti “mizimu ya akufa imaloŵa mumkhalidwe wachimwemwe [kumwamba], kuyeretsedwa [purigatoriyo], kapena chilango [helo] imfa itangochitika, ndi kudzakumananso ndi matupiwo pakutha kwa dziko.”
Mosasamala kanthu za kutsutsana ndi kukanganako, umu ndimo mmene matchalitchi a Dziko Lachikristu akhalira kwa zaka mazana ambiri, ngakhale kuti matchalitchi ambiri a Aprotesitanti ndi a Orthodox kwenikweni sakhulupirira za purigatoriyo. Komabe, kuyambira kumapeto kwa zaka za zana lapitalo, chiŵerengero chowonjezereka cha akatswiri asonyeza kuti chiphunzitso cha kusafa kwa mzimu sichili chochokera m’Baibulo, ndipo monga chotulukapo chake, “maphunziro a zaumulungu amakono tsopano amayesayesa kulingalira munthu monga chinthu chimene chimatheratu pa imfa.” (The Encyclopedia of Religion) Motero, othirira ndemanga pa Baibulo amapeza kukhala kovuta kuvomereza kukhalapo kwa “mkhalidwe wa pakati.” Kodi Baibulo limanena kanthu za uwo, kapena kodi limapereka chiyembekezo cha mtundu wina?
Kodi Paulo Anakhulupirira “Mkhalidwe wa Pakati”?
Catechism of the Catholic Church imati: “Kuti tiuke ndi Kristu, tiyenera kufa ndi Kristu: tiyenera ‘kusiyana ndi thupi ndi kugwirizana ndi Ambuye.’ [2 Akorinto 5:8] ‘Pakusiyana’ kumeneko kumene kuli imfa mzimu umalekana ndi thupi. [Afilipi 1:23] Udzagwirizana ndi thupi patsiku la kuuka kwa akufa.” Koma kodi m’mavesi ogwidwa mawu panopo, Paulo akunena kuti mzimu umapulumuka pa imfa ya thupi ndiyeno kuyembekezera “Chiweruzo Chomaliza” kuti udzagwirizane ndi thupi?
Pa 2 Akorinto 5:1, Paulo akunena za imfa yake ndipo akulankhula za “nyumba ya pansi pano” imene “ipasuka.” Kodi iye anali kulingalira za thupi limene mzimu wake wosafa unachokamo? Ayi. Paulo anakhulupirira kuti munthu ndiye moyo, osati kuti ali ndi mzimu wosafa. (Genesis 2:7; 1 Akorinto 15:45) Paulo anali Mkristu wodzozedwa ndi mzimu amene chiyembekezo chake, mofanana ndi chija cha abale ake a m’zaka za zana loyamba, ‘chinasungikira m’mwamba.’ (Akolose 1:5; Aroma 8:14-18) Motero, “kukhumbitsa” kwake kunali kwakuti adzaukitsidwire kumwamba monga cholengedwa chauzimu chosafa panthaŵi yoikika ya Mulungu. (2 Akorinto 5:2-4) Polankhula za chiyembekezo chimenechi, iye analemba kuti: “Tonse tidzasandulika, . . . pa lipenga lotsiriza; pakuti lipenga lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa osavunda, ndipo ife tidzasandulika.”—1 Akorinto 15:51, 52.
Pa 2 Akorinto 5:8, Paulo akunena kuti: “Tilimbika mtima, ndipo tikondwera makamaka kusakhala m’thupi, ndi kukhala kwathu kwa Ambuye.” Ena amakhulupirira kuti mawu ameneŵa amanena za mkhalidwe woyembekezera umene umakhala pakati. Oterowo amasonyezanso za lonjezo la Yesu kwa otsatira ake okhulupirika lakuti anali kupita kukawakonzera malo amene ‘akawalandiriramo kwa iye yekha.’ Koma kodi ziyembekezo zotero zidzakwaniritsidwa liti? Kristu ananena kuti kudzakhala pamene ‘abweranso’ m’kukhalapo kwake kwamtsogolo. (Yohane 14:1-3) Mofananamo, pa 2 Akorinto 5:1-10, Paulo ananena kuti chiyembekezo cha Akristu odzozedwa onse chinali cha kukakhala kumwamba. Zimenezi zikachitika, osati mwa kusafa kwa mzimu kongolingaliridwa, koma kupyolera m’chiukiriro mkati mwa kukhalapo kwa Kristu. (1 Akorinto 15:23, 42-44) Wotanthauzira malemba Charles Masson akunena kuti 2 Akorinto 5:1-10 “angamvedwe bwino popanda kutembenukira ku lingaliro la ‘mkhalidwe wa pakati.’”
Pa Afilipi 1:21, 23, Paulo akunena kuti: “Kwa ine kukhala ndi moyo ndiko Kristu, ndi kufa kuli kupindula. Koma ndipanikizidwa nazo ziŵirizi, pokhala nacho cholakalaka cha kuchoka kukhala ndi Kristu, ndiko kwabwino koposaposatu.” Kodi Paulo pano akunena za “mkhalidwe wa pakati”? Ena amaganiza choncho. Komabe, Paulo akunena kuti anapanikizidwa ndi zinthu ziŵiri zothekera—moyo kapena imfa. “Pokhala nacho cholakalaka,” iye anawonjezera motero, akumatchula kuthekera kwina kwachitatu, “kuchoka kukhala ndi Kristu.” “Kuchoka” kukakhala ndi Kristu nthaŵi yomweyo imfa itachitika? Chabwino, monga momwe taonera kale, Paulo anakhulupirira kuti Akristu odzozedwa okhulupirika akaukitsidwa mkati mwa kukhalapo kwa Kristu. Chifukwa chake, iye ayenera kukhala anali akulingalira za zochitika za nyengo imeneyo.
Zimenezi zingaonedwe m’mawu ake opezeka pa Afilipi 3:20, 21 ndi 1 Atesalonika 4:16. “Kuchoka” kumeneko mkati mwa kukhalapo kwa Kristu Yesu kukakhozetsa Paulo kulandira mphotho imene Mulungu anamkonzera. Kunena kuti chimenechi chinali chiyembekezo chake kukuchitiridwa umboni m’mawu ake kwa Timoteo wachichepere: “Chotsalira wandiikira ine korona wa chilungamo, amene Ambuye, woweruza wolungama, adzandipatsa ine tsiku lijalo: ndipo si kwa ine ndekha, komatunso kwa onse amene anakonda maonekedwe ake.”—2 Timoteo 4:8.
Chiukiriro—Choonadi Chabwino Koposa cha Baibulo
Akristu oyambirira analingalira chiukiriro kukhala chochitika chimene chikayamba mkati mwa kukhalapo kwa Kristu, ndipo analimbitsidwa ndi kutonthozedwa ndi choonadi chabwino koposa chimenechi cha Baibulo. (Mateyu 24:3; Yohane 5:28, 29; 11:24, 25; 1 Akorinto 15:19, 20; 1 Atesalonika 4:13) Anayembekezera mokhulupirika mtsogolo mwachisangalalo mmenemo, akumakana ziphunzitso zampatuko za kusafa kwa mzimu.—Machitidwe 20:28-30; 2 Timoteo 4:3, 4; 2 Petro 2:1-3.
Ndithudi, chiukiriro sichili chabe cha Akristu okhala ndi chiyembekezo chakumwamba. (1 Petro 1:3-5) Makolo ndi atumiki ena akale a Mulungu anasonyeza chikhulupiriro m’kukhoza kwa Yehova kuukitsira akufa kumoyo pa dziko lapansi. (Yobu 14:14, 15; Danieli 12:2; Luka 20:37, 38; Ahebri 11:19, 35) Ngakhale kwa miyandamiyanda ya awo amene m’zaka mazana ambiri apita sanadziŵe Mulungu ali ndi mwaŵi wa kukhalanso ndi moyo padziko lapansi la paradaiso, popeza kuti “kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Machitidwe 24:15; Luka 23:42, 43) Kodi chimenechi sichiyembekezo chokondweretsa?
M’malo mwa kutichititsa kukhulupirira kuti kuvutika ndi imfa zidzakhalako nthaŵi zonse, Yehova amatisonyeza za nthaŵiyo pamene “mdani wotsiriza . . . imfa,” adzachotsedwa kosatha ndipo mtundu wa anthu wokhulupirika udzakhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso wobwezeretsedwanso pa dziko lapansi. (1 Akorinto 15:26; Yohane 3:16; 2 Petro 3:13) Kudzakhala kwabwino chotani nanga kuona okondedwa athu akukhalanso ndi moyo! Chiyembekezo chimenechi nchabwino kwambiri chotani nanga kuposa lingaliro lopanda maziko la kusafa kwa mzimu—chiphunzitso chozikidwa, osati pa Mawu a Mulungu, koma pa nthanthi Yachigiriki! Ngati muika chiyembekezo chanu pa lonjezo lotsimikizirika la Mulungu, nanunso mungatsimikizire kuti posachedwa “sipadzakhalanso imfa”!—Chivumbulutso 21:3-5.
[Chithunzi patsamba 31]
Chiukiriro ndicho choonadi chabwino koposa cha Baibulo