Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • pe mutu 5 tsamba 47-56
  • Kodi Baibulo Nlochokeradi kwa Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Baibulo Nlochokeradi kwa Mulungu?
  • Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • PALIBE BUKHU LINA LONGA BAIBULO
  • MMENE BAIBULO LINALEMBEDWERA
  • KUPANGITSA BAIBULO KUKHALA LOPEZEKA KWA ONSE
  • KODI BAIBULO LASINTHIDWA?
  • KODI BAINULO NLOWONADI?
  • Kodi Baibulo N’chiyani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Ziphunzitso Zoona Zimene Zimakondweretsa Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2005
  • N’chifukwa Chiyani Pali Mabaibulo Osiyanasiyana?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
  • Baibulo Ndi Buku Lochokera kwa Mulungu
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
Onani Zambiri
Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
pe mutu 5 tsamba 47-56

Mutu 5

Kodi Baibulo Nlochokeradi kwa Mulungu?

1. Kodi nchifukwa ninji kuli koyenera kukhulupirira kuti Mulungu akatipatsa chidziwitso chonena za iye mwini?

KODI YEHOVA MULUNGU watipatsa chidzitso chonena za iye mwini? Kodi watiuza zimene wachita ndi zimene akulinganizabe kuchita? Atate amene amakonda aa ake amawauza zinthu zambiri. Ndipo mwa zimene tawona, Yehova alidi ataye wachikondi.

2. (a) Kodi njira yabwino kwambiri yakuti Yehova atiuze ponena za iye mwini njotani? (b) Kodi imeneyi imadzutsa mafunso otani?

2 Kodi Yehova akapereka bwanji chidziwitso kwa anthu okhala m’mbali zambiri za dziko lapansi ndi m’nyengo za nthawi zosiyanasiyana? Njira yabwino kwambiri ikakhala yakuti iye achititse bukhu kulembedwa ndiyeno kuwona kuti linapangitsidwa kukhala lopezeka kwa onse. Kodi Baibulo ndiBukhu loterolo lochokera kwa Mulungu? Kodi tingadziwe bwanji ngati ndilo?

PALIBE BUKHU LINA LONGA BAIBULO

3. Kodi njira imodzi yotani mu imene Baibulo liri bukhu lapadera?

3 Ngati Baibulo liri lochokeradi kwa Mulungu, tiyenera kuliyembekezera kukhala bukhu lapadera koposa lolembedwa chiyambire. Kodi ndilo? Inde, ndipo kaamba ka zifukwa zambiri. Choyamba, nlakale kwambiri; simukanayembekezera Mawu a Mulungu kwa anthu onse kukhala atalembedwa nthawi yaifupi yapitayo, kodi sichoncho? Kulembedwa kwake kunayamba zaka zokwanira 3,500 zapitazo m’chinenero Chachihebri. Ndiyeno, zaka zoposa 2,200 zapitazo, linayamba kutembenuziridwa m’zinenero zina. Lerolino pafupifupi aliyense padziko lapansi angawerenge Baibulo m’chinenero chakechake.

4. Kodi ndimotani mmene chiwerengero cha Mabaibulo otulutsidwa chimasiyanira ndi chija cha mabukhu ena?

4 Ndiponso, palibe bukhu lina limayandikira Baibulo m’chiwerengero cha makope amene apangidwa. Bukhu lingatchedwe “logudwa kwambiri” pamene kokha makope zikwi zambiri atulutsidwa. Komabe chaka chirichonse mamiliyoni ambiri a Mabaibulo amasindikizidwa. Ndipo mkati mwa zaka mazana ambiri mamiliyoni zikwi zambiri apangidwa! Palibe malo alionse padziko lapansi, mosasamala kanthu mmene iwo angakhalire akutali, kumene simungapeze Baibulo. Kodi zimenezi sindizo zimene mukanayembekezera bukhu limene liri lochokeradi kwa Mulungu?

5. Kodi ndizoyesayesa zotani zimene zapangidwa kuwononga Baibulo?

5 Chimene chikupangitsa kufalitsidwa kwakukulu kwa Baibulo kumeneku kukhaladi kwapadera ndicho chenicheni chakuti adani ayesayesa kuliwononga. Koma kodi sitiyenera kuyembekezera kuti bukhu lochokera kwa Mulungu likaukiridwa ndi oimira a Mdyerekezi? Zimenezi zachitika. Kutentha Mabaibulo pa nthawi ina kunali kofala, ndipo awo amene anagwidwa akuwerenga Baibulo kawirikawiri analangidwa ndi imfa.

6. (a) Kodi ndimafunso ofunika otani amene Baibulo limayankha? (b) Kodi olemba Baibulo amanena kuti analandira mawu awo kuchokera kwa yani?

6 Mukayembekezera bukhu lochokera kwa Mulungu kofotokoza zinthu zofunika zimene tonsefe tiyenera kufuna kudziwa. ‘Kodi moyo unachokera kuti?’ ‘Kodi nchifukwa ninji tiri pano?’ ‘Kodi mtsogolo mudzabweretsanji?’ ndiwo ena a mafunso amene limayankha. Ndipo limanena mwachimvekere kuti chidziwitso chimene chiri nacho nchochokera kwa Yehova Mulungu. Wolemba Baibulo wina anati: “Mzimu wa Yehova unalankhula mwa ine, ndi mawu ake anali pa lilime langa. (2 Samueli 23:2) Wina analemba kuti: “Lemba lirolonse adaliuzira Mulungu.” (2 Timoteo 3:16) Popeza kuti Baibulo limafotokoza motsimikiza kwambiri kuti ndilo Mawu a Mulungu, kodi sikukakhala kwanzeru kulipenda kuti muwone ngati liridi?

MMENE BAIBULO LINALEMBEDWERA

7. (a) Kodi ndani analemba Baibulo? (b) Pamenepa, kodi ndimotani mmene kunganenedwere kuti ndilo Mawu a Mulungu?

7 ‘Komabe kodi ndimotani mmene Baibulo lingakhalire lochokera kwa Mulungu pamene linalembedwa ndi anthu?’ mungafunse. Zowona, anthu okwanira 40 anakhala ndi phande m’kulemba Baibulo. Anthu amenewa analembadi Baibulo kupatulapo Malamulo Khumi, amene analemedwa ndi Mulungu mwini pamagome amiyala mwa kachitidwe kachindunji ka mzimu wake woyera. (Eksodo 31:18) Komabe, zimenezi sizipangitsa zimene iwo analemba kusakhalanso Mawu a Mulungu. Baibulo limafotokoza kuti: ‘Anthu analankhula zochokera kwa Mulungu pamene anagwidwa ndi mzimu woyera.”(2 Petro 1:21 NW) Inde monga momwedi Mulungu anagwiritsira ntchito mzimu wake woyera wamphamvu kulenga kumwamba, dziko lapansi ndi zinthu zonse zamoyo, iye anaugwiritsiranso ntchito kutsogoza kulembedwa kwa Baibulo.

8, 9. Kodi ndizitsanzo zotani lerolino zimene zingatithandize kuzindikira mmene Mulungu anachititsira Baibulo kulembedwa?

8 Zimenezi zikutanthauza kuti Baibulo liri ndi mlembi mmodzi yekha, Yehova Mulungu. Iye anagwiritsira ntchito anthu kulemba chidziwitsocho, mofanana ndi mmene bizinesimani amagwiritsira ntchito mlembi kulemba kalata. Mlembiyo amalemba kalata, koma kalatayo imakhala ndi maganizo ndi malingaliro a bizinesimaniyo. Motero imakhala kalata yake, osati ya mlembi, monga momwedi Baibulo liriri Bukhu la Mulungu, osati bukhu la anthu amene amagwiritsiridwa ntchito kulilemba.

9 Popeza kuti Mulungu analenga maganizo, iye ndithudi sanawone kukhala kovuta kugwirizana ndi maganizo a atumiki ake kuwapatsa chidziwitsocho kuti alembe. Ngakhale lerolino munthu angakhale pansi m’nyumba mwake ndi kulandira mauthenga ochokera kutali mwa njira ya rediyo kapena televizheni. Mawu kapena zithunzithuzi zimayenda maulendo atali mwa kugwiritsiridwa ntchito kwa malamulo achilengedwe amene Mulungu anayambitsa. Chifukwa cha chimenecho, nkwapafupi kuzindikira kuti Yehova, ali kumalo ake kutali kumwamba, akatha kutsogoza anthu kulemba chidziwitso chimene iye anafuna kuti banja la anthu lidziwe.

10. (a) Kodi ndimabukhu angati amene akupanga Baibulo, ndipo kodi iwo analembedwa mkati mwa nyengo ya nthawi yotani? (b) Kodi ndinkhani yaikulu yotani imene imapezeka m’Baibulo lonse?

10 Chotulukapocho chakhala Bukhu lodabwitsa. Kwenikweni, Baibulo lapangika ndi mabukhu ang’ono 66. Liwu Lachigirikilo biblia, m’limene liwulo “Baibulo” limachokera, limatanthauza “timabukhu.” Mabukhu, kapena makalata amenewa, amalembedwa mkati mwa nyengo ya zaka 1,600, kuyambira 1513 B.C.E. kufikira 98 C.E. Komabe, chifukwa cha kukhala Mlembi mmodzi yekha, mabukhu onsewa ngogwirizana lina ndi linzake. Nkhani imodzimodzi imapezeka my lonse, yakuti Yehova Mulungu adzabweretsa mikhalidwe yolungama mwa ufumu wake. Bukhu loyambalo, Genesis, limasimba mmene malo okhala aparadaiso anatayikira chifukwa cha kupandukira Mulungu, ndipo bukhu lotsirizalo, Chivumbulutso, limafotokoza mmene dziko lapansi lidzapangidwiranso kukhala paradaiso mwa ulamuliro wa Mulungu.—Genesis 3:19, 23; Chivumbulutso 12:10; 21:3, 4.

11. (a) Kodi zinenero zogwiritsiridwa nchito kulemba Baibulo zinali zotani? (b) Kodi Baibulo lagawidwa kukhala mbali ziwiri zazikulu zotani, koma kodi nchiyani chimene chimasonyeza chigwirizano chawo?

11 Mabukhu a Baibulo 39 oyambirirawo analembedwa kwakukulukulu m’chinenero Chachihebri, limodzi ndi mbali zochepa kwambiri m’Chiaramu. Mabukhu 27 otsirizirawo analembedwa m’Chigiriki, chinenero chofala cha anthu pamene Yesu ndi atsatiri ake Achikristu anali padziko lapansi. Mbali ziwiri zazikulu za Baibulo zimenezi zimatchedwa moyenerera “Malemba Achihebri” ndi “Malemba Achigiriki.” Posonyeza kugwirizana kwawo ina ndi inzake, Malemba Achigiriki amagwira mawu m’Malemba Achihebri koposa nthawi 365, ndi kupanga marefurensi ena 375 kwa iwo.

KUPANGITSA BAIBULO KUKHALA LOPEZEKA KWA ONSE

12. Kodi nchifukwa ninji Yehova anachititsa makope a Baibulo kupangidwa?

12 Ngati malemba oyambirira okha akanakhala opezeka, kodi munthu aliyense akanawerenga motani Mawu a Mulungu? Iwo sakadatha. Motero Yehova analinganiza kuti makope a malemba oyambirira Achihebri apangidwe. (Deuteronomo 17:18) Mwa chitsanzo, mwamunayo Ezara, akutchedwa “mlembi waluntha m’chilamulo cha Mose, chimene Yehova Mulungu wa Israyeli anachipereka.” (Ezara 7:6) Ndiponso, makope zikwi zambiri za Malemba Achigiriki anapangidwa.

13. (a) Kodi nchiyani chimene chinafunika kotero kuti anthu ochuluka akathe kuwerenga Baibulo? (b) Kodi ndiliti pamene kutembenuzidwa koyamba kwa Baibulo kunapangidwa?

13 Kodi mumawerenga Chihebri kapena Chigiriki? Ngati ayi, simungawerenge makope a Baibulo oyambirira olembedwa pamanja, ena ake amene alipobe. Chifukwa cha chimenecho, kuti muwerenge Baibulo, winawake anafunikira kuika mawuwo m’chinenero chimene mudziwa. Kutembenuza kumeneku kuchokera ku chinenero chimodzi kumka ku china kwatheketsa anthu ambiri kuwerenga Mawu a Mulungu. Mwa chitsanzo, pafupifupi zaka 300 Yesu asanakhale padziko lapansi, Chigiriki chinachake chinenero chimene anthu ochuluka anayamba kulankhula. Motero Malemba Achihebri anaikidwa m’Chigiriki, kuyambira mu 280 B.C.E. Kutembenuza koyambirira kumeneku kunatchedwa “Septuagint.”

14. (a) Kodi nchifukwa ninji atsogoleri ena achipembedzo anamenya nkhondo kuchititsa Baibulo kusatembenuzidwa? (b) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti amenewa analuza nkhondoyo?

14 Pambuyo pake. Chilatini chinakhala chinenero chofala cha anthu ambiri, motero Baibulo linatembenuziridwa m’Chilatini. Koma, pamene zaka mazana ambiri zinatha, anthu ocheperachepera analankhula Chilatini. Anthu ochuluka analankhula zinenero zina, monga ngati Chiarabu, Chifrenchi, Chispanya, Chipwitikizi, Chitaliyan, Chijeremani ndi Chingelezi. Kwa nthawi yaitali atsogoleri achipembedzo Achikatolika anamenya nkhondo kuchitisa Baibulo kusaikidwa m’chinenero cha anthu wamba. Iwo anatenthadi pamtengo anthu okhala ndi Baibulo.Iwo anachita zimenezi chifukwa chakuti Baibulo linavumbula ziphunzitso zawo zonyenga ndi machitidwe oipa. Koma, m’kupita kwa nthawi, atsogoleri achipembedzo amenewa analuza nkhondoyo, ndipo Baibulo linayamba kuikidwa m’zinenero zambiri ndi kugawidwa m’ziwerengero zazikulu. Lerolino Baibulo lingawerengedwe, mu uthunthu wake kapena m’theka, m’zinenero zoposa 1,700!

15. Kodi nchifukwa ninji matembenuzidwe Abaibulo atsopano kwambiri ali abwino kukhala nawo?

15 Pamene zaka zinatha, matembenuzidwe ambiri osiyanasiyana a Baibulo anapangidwa m’chinenero chimodzimodzi. Mwa chitsanzo, m’Chingelezi chokha muli matembenuzidwe a Baibulo ambiri Chifukwa ninji? Kodi kamodzi kokha sikakanakhala kokwanira? Eya, mkati mwa zaka zambiri chinenero chimadzasintha kwambiri. Motero ngati mukanayerekezera matembenuzidwe Abaibulo akale ndi atsopano kwambiri, mukanawona masinthidwe m’chinenero. Pamene iwo pafupifupi nthawi zonse anapereka ganizo limodzimodzi, mudzawona kuti matembenuzidwe osindikizidwa m’zaka zaposachedwapa kwambiri ali kwenikweni osavuta kwambiri kumvetsetsa. Motero tingakhale othokoza kaamba ka matembenuzidwe Abaibulo atsopano, popeza kuti iwo amaika Mawu a Mulungu m’chinenero chofala ndi chosavuta kumva cha panthawiyo.

KODI BAIBULO LASINTHIDWA?

16. Kodi nchifukwa ninji anthu ena amakhulupirira kuti Baibulo lasinthidwa?

16 Koma mungafunse kuti: ‘Kodi tingatsimikizire motani kuti Mabaibulo anthu lerolino ali ndi mawu amodzimodziwo amene olemba Baibulo analandira kuchokera kwa Mulungu?’ Mwa kukopedwakopedwa kwa mabukhu Abaibulo mkati mwa zaka mazana ambiri ndipo ngakhale zikwi zambiri, kodi zolakwa sizinalowemo? Inde, koma zolakwa zimenezi zatulukiridwa ndi kukonzedwa m’matembenuzidwe amakono a Baibulo. Lerolino mawuwo ali chimodzimodzi monga pamene Mulungu anapereka kwa awo amene anawalemba poyamba. Kodi pali umboni wotani wa zimenezi?

17. Kodi pali umboni wotani wakuti Baibulo silinasinthidwe?

17 Eya, pakati pa 1947 ndi 1955 zimene zikutchedwa Dead Sea Scrolls zinapezedwa. Mipukutu yakale imeneyi imaphatikizapo makope a mabukhu a Malemba Achihebri. Iyo ikuyambira pa zaka 100 kufikira 200 Yesu asanabadwe. Umodzi wa mipukutuyo ndiwo kope la bukhu la Yesaya. Limeneli lisanapezeke kope lakale koposa la bukhu la Yesaya lopezeka m’Chihebri linali lija limene linalembedwa pafupifupi zaka 1,000 Yesu atabadwa. Pamene makope awiri a Yesaya amenewa anayerekezeredwa munali kusiyana kokha kwakung’ono kwambiri mwa iwo, kochuluka kwake kunali kusiyanasiyana kwakung’ono kwa sipelo! Zimenezi zikutanthauzakuti m’zaka zoposa 1,000 za kukopa sipadakhale kusintha kwenikweni!

18. (a) Kodi ndimotani mmene zolakwa za okopa zawongoledwera? (b) Kodi nchiyani chimene chinganenedwe ponena za kulongosoka kwa Malemba Achigiriki?

18 Pali makope akale oposa 1,700 a zigawo zosiyanasiyana za Malemba Achihebri opezeka. Mwa kuyerekezera mosamala makope ambiri akale kwambiri amenewa, ngakhale zolakwa zowerengeka zimene okopa anapanga zingapezedwe ndi kuwongoledwa. Ndiponso, pali zikwi zambiri za makope akale kwambiri a Malemba Achigiriki, ena a makopewo amachokera pafupifupi ku nthawi ya Yesu ndi atumwi ake. Motero, monga momwe Sir Frederic Kenyon ananenera: “Maziko otsiriza a chikayikoo chirichonse chakuti Malemba afika kwa ife monga mome iwo analembedwera kwenikweni tsopano achotsedwa.—The Bible and Archaeology, tsamba 288, 289.

19. (a) Kodi nchiyani chimene chiri chitsanzo cha kuyesa kuwonjezera ku Baibulo? (b) Kodi tikudziwa motani kuti 1 Yohane 5:7 sali wa m’Baibulo?

19 Zimenezi sizitanthauza ksuti sipanakhale zoyesayesa za kusintha Mawu a Mulungu. Zakhalapo. Chitsanzo chapadera ndicho 1 Yohane 5:7. Mu Authorized Version ya 1611 amati: “Pakuti pali atatu amene achitira umboni kumwamb, Atate, Mawu, ndi Mzimu Woyera: ndipo atatu amenewa ndiwo mmodzi.” Komabe mawu amenewa sakupezeka mu alionse a makope a Baibulo oyambirira kwambiri. Iwo anawonjezeredwa ndi munthu wina amene anali kuyesa kuchirikiza chiphunzitso Chautatu. Popeza kuti nkwachiwonekere kuti mawu amenewa sali kwenikweni mbali ya Mawu a Mulungu, mawongoledwe apangidwa ndipo mawuwo sakupezeka m’Mabaibulo atsopano kwambiri.

20. Kodi nchifukwa ninji tingatsimikizire kuti Baibulo lasungidwa mu mpangidwe wangwiro?

20 Motero aliyense amene amanena kuti Baibulo liribe mawu amodzimodziwo monga pamene ilo linalembedwa poyamba sakudziwa konse zenizeni. Yehova Mulungu walinganiza kuti Mawu ake atetezeredwe osati kokha ku zolakwa zimene okopa anapanga komanso ku zoyesayesa za ena za kuwawonjezera. Baibulo lenilenilo liri ndi lonjezo la Mulungu lakuti Mawu ake akasungidwe mu mpangidwe wangwiro kaamba ka ife lerolino.—Salmo 12:6, 7; Danieli 12:4; 1 Petro 1:24, 25; Chivumbulutso 22:18, 19.

KODI BAINULO NLOWONADI?

21.Kodi ndimotani mmene Yesu anawonera Mawu a Mulungu?

21 Yesu Kristu m’pemphero kwa Mulungu anati: “Mawu anu ndichowonadi.” (Yohane 17:17) Koma kodi maumboni amachirikiza zimenezi? Pamene Baibulo lipendedwa mosamala, kodi timapeza kuti ilo liridi chowonadi?Ophunzira mbiri amene apenda Baibulo kawirikawiri amadabwa ndi kulongosoka kwake. Baibulo liri ndi maina ndi zinthu zotsimikizirika zimene zingatsimikiziridwe. Lingalirani zitsanzo zina.

22-25. Kodi ndizitsanzo zowerengeka zotani zimene zimasonyeza kuti Baibulo liri ndi mbiri yowona?

22 Yang’anani zithunzithuzi ndi malembowo pakhomo la kachisi lino ku Karnak, Igupto. Izo zikusimba chipambano, pafupifupi zaka 3,000 zapitazo, cha Farao Sisaki paufumu wa Yuda mkati mwa kulamulira kwa mwana wa Solomo Rehabiamu. Baibulo limasimba chochitika chimodzimodzicho.—1 Mafumu 14:25, 26.

23 Yang’ananinso Mwala Wachimoabuwo. Weniweni ungawonenedwe mu Louvre Museum mu Paris, France. Malembowo amasimba chipanduko chochitidwa ndi Mfumu Mesa ya Moabu pa Israyeli. Chochitika chimenechi chikusimbidwanso m’Baibulo.—2 Mafumu 1:1; 3:4-27.

24 Dziwe la Siloamu ndi polowera pa mchera wamadzi wautali mapazi 1,749 (mamita 533) m’Yerusalemu zikuwoneka pano kudzanja lamanja kwenikweno. Ocheza Yerusalemu ambiri amakono ayenda kuvukuvu mumchera umenewu. Kukhalapo kwake ndiko umboni wowonjezereka wakuti Baibulo nlowona. Kodi ziri choncho motani? Chifukwa chakuti Baibulo limafotokoza kuti Mfumu Hezekiya anachititsa mchera umenewu kukumbidwa zaka zoposa 2,500 zapitazo kutetezera madzi ake kwa gulu lankhondo loukira.—2 Mafumu 20:20; 2 Mbiri 32:2-4, 30.

25 Pa British Museum wocheza angawone Mbiri ya Nabonidus, kope lake limene likuwoneka kumanja. Imafotokoza kugwa kwa Babulo wakale, monga momwedi Baibulo limachitiranso. (Danieli 5:30, 31) Koma Baibulo limanena kuti Belisazara anali pa nthawi imeneyo mfumu ya Babulo. Komabe Mbiri ya Nabonidus sikutchulankomwe dzinalo Belisazara. Kunena zowona, pa nthawi ina zolembedwa zonse zakale zodziwika zinanena kuti Nabonidus anali mfumu yotsiriza ya Babulo. Motero ena amene ananena kuti Baibulo silowona ananenakuti Belisazara sanakhaleko ndi kuti Baibulo linalakwa. Koma m’zaka zaposachedwapa zolembedwa zakale zapezedwa zimene zinadziwikitsa Belisazara kukhala mwana wa Nebonidus ndi wolamulira limodzi ndi atate wake m’Babulo pa nthawiyo! Inde, Baibulo nlowonadi, monga momwe zitsanzo zambirimbiri zimatsimikizirira.

26. Kodi pali umboni wotani wakuti Baibulo nlowona mwausayansi?

26 Komabe Baibulo siliri kokha ndi mbiri yowona. Chirichonse chimene limanena nchowona. Ngakhale pamene limakhudza pa nkhani ya sayansi, limakhala lolondola modabwitsa. Kupereka zitsanzo ziwiri chabe: M’nthawi zakale kunakhulupiriridwa mofala kuti dziko lapansi linali ndimchirikizo wowoneka, kuti linakhala pakanthu kena, monga ngati pachimphona. Komabe mogwirizana kwambiri ndi umboni wasayansi, Baibulo limasimba kuti Mulungu ‘akulenjeka dziko lapansi pachabe.’ (Yobu 26:7) Ndipo koposa ndi kunena kuti dziko lapansi nlathyathyathya, monga momwe ambiri anakhulupirira papitapo, Baibulo limanena kuti Mulungu “akukhala pamwamba pa mbulunga ya dziko lapansi.”—Yesaya 40:22, NW.

27. (a) Kodi nchiyani chimene chiri umboni wamphamvu koposa wakuti Baibulo nlochokera kwa Mulungu? (b) Kodi ndizinthu zotani zimen Malemba Achihebri ananeneratu mowona ponena za Mwana wa Mulungu?

27 Koma umboni waukulu koposa wakuti Baibulo nlochokeradi kwa Mulungu ndiwo cholembedwa chake changwiro m’kuneneratu mtsogolo. Palibe bukhu lolembedwa ndi anthu limasimba mwandendende mbiri iyo isanachitike; komabe Baibulo limatero. Ladzaza maulosi owona, inde, mbiri yolembedwadi pasadakhale. Ena apadera koposa a amenewa ngonena za kudza kudziko lapansi kwa Mwana wa Mulungu. Malemba Achihebri ananeneratu mowona zaka mazana ambiri pasadakhale kuti Wolonjezedwa ameneyu akabadwira m’Betelehemu, kuti iye akaberekedwa ndi namwali, kuti akaperekedwa kaamba ka ndalama 30 zasiliva, kuti akaphatikizidwa pamodzi ndi ochimwa, kuti nnena fupa la thupi lake nlimodzi lomwe likathyoledwa, kuti maere akachitidwira zovala zake, ndi zinthu zina zambirimbiri.—Mika 5:2; Mateyu 2:3-9; Yesaya 7:14; Mateyu 1:22, 23; Zakariya 11:12, 13; Mateyu 27:3-5; Yesaya 53:12; Luka 22:37, 52; 23:32, 33; Salmo 34:20; Yohane 19:36; Salmo 22:18; Mateyu 27:35.

28. (a) Kodi nchifukwa ninji tingakhale ndi chidaliro chakuti ngakhale maulosi Abaibulo amenewo amene sanakwaniritsidwebe adzakwaniritsidwa? (b) Kodi kuphunzira Baibulo kopitirizabe kudzakukhutiritsani maganizo za chiyani?

28 Monga momwe kunanenedwera m’chaputula choyamba cha bukhu lino, Baibulonso limaneneratu kuti dongosolo la zinthu lakale lino lidzatha posachedwapa ndipo latsopano lolungama lidzalowa m’malo mwake. (Mateyu 24:3-14’ 2 Petro 3:7, 13) Kodi tingadalire pa maulosi oti akwaniritsidwe posachedwapa oterowo? Eya, ngati munthu wina anakuuzani zowona nthawi zambirimbiri, kodi inu mwadzidzidzi mukamkayikira pamene atakuuzani kanthu kena katsopano? Ngati simunampeze kukhala wonama, kodi inu tsopano mukayamba kumkayikira? Ha, kumeneko kukhakhala kosayenera chotani nanga! Momwemonso, palibe chifukwa chakuti ife tikayikire chirichonse chimene Mulungu amalonjeza m’Baibulo. Mawu ake angakhulupiriridwe! (Tito 1:2) Mwa kupitiriza kuphunzira Baibulo, inu, nanunso, mudzakhala wokhutiritsidwa maganizo mowonjezerekawonjezereka ndi zenizeni zakuti Baibulo mowonadi nlochokera kwa Mulungu.

[Chithunzi patsamba 49]

Mulungu anagwiritsa ntchito anthu kulemba Baibulo mofanana kwambiri ndi mmene bizinesimani amagwiritsirira ntchito mlembi kulemba kalata

[Chithunzi patsamba 50]

Atsogoleri ena achipembedzo anamenya nkhondo kuchititsa Baibulo kubisidwa kwa anthu wamba, ngakhale kutentha pamtengo awo amene anali nalo

[Chithunzi pamasamba 52, 53]

Mpukutu wa Yesaya wa m’Nyanja Yamchere

[Zithunzi pamasamba 54, 55]

Khoma la kachisi ku Karnak, Igupto

Mwala Wachimoabu

Mbiri ya Nabonidus

Polowera kumchera wa Hezekiya ndi Dziwe la Siloamu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena