Macitidwe a Atumwi
7 Koma mkulu wa ansembe anafunsa kuti: “Kodi zimenezi n’zoona?” 2 Sitefano anayankha kuti: “Anthu inu, abale anga ndi azibambo anga, tamvelani. Ulemelelo wa Mulungu unaonekela kwa atate wathu Abulahamu pamene anali ku Mesopotamiya asanapite kukakhala ku Harana. 3 Anamuuza kuti: ‘Tuluka m’dziko lako komanso pakati pa abale ako upite kudziko limene ndidzakuonetsa.’ 4 Cotelo iye anatuluka m’dziko la Akasidi n’kukakhala ku Harana. Ndiyeno kumeneko, atate ake atamwalila, Mulungu anamucititsa kuti akhale m’dziko lino limene inu mukukhala. 5 Koma kumeneko sanamupatse colowa ciliconse, ngakhale kamalo kakang’ono. M’malomwake, anamulonjeza kuti adzamupatsa dzikolo kuti likhale colowa cake, komanso ca mbadwa* zake, ngakhale kuti panthawiyo analibe mwana. 6 Komanso Mulungu anamuuza kuti mbadwa* zake zidzakhala alendo m’dziko la eni, ndipo anthu adzawapanga kukhala akapolo ndi kuwazunza* kwa zaka 400. 7 Mulungu anati, ‘Mtundu umene udzawasunga ngati akapolo, ine ndidzauweluza. Ndipo pambuyo pa zimenezi, iwo adzamasulidwa n’kudzanditumikila pamalo ano.’
8 “Anamupatsanso cipangano ca mdulidwe. Kenako anabeleka Isaki, ndipo anamucita mdulidwe pa tsiku la 8. Isaki nayenso anabeleka* Yakobo, ndipo Yakobo anabeleka mitu ya mabanja 12. 9 Mitu ya mabanja imeneyo inamucitila nsanje Yosefe, ndipo inamugulitsa ku Iguputo. Koma Mulungu anali naye, 10 ndipo anamupulumutsa m’masautso ake onse. Komanso anali kumukonda, ndipo anam’patsa nzelu pamaso pa Farao mfumu ya Iguputo. Farao ameneyo, anasankha Yosefe kuti aziyang’anila Iguputo ndi nyumba yake yonse. 11 Koma ku Iguputo ndi ku Kanani kunagwa njala yaikulu moti kunali mavuto aakulu. Ndipo makolo athu akale amenewo sanali kukwanitsa kupeza cakudya. 12 Koma Yakobo anamva kuti ku Iguputo kuli cakudya, ndipo anatuma makolo athu kwa nthawi yoyamba. 13 Paulendo waciwili, Yosefe anadziulula kwa abale ake, ndipo makolo ake ndi abale ake a Yosefe anadziwika kwa Farao. 14 Conco Yosefe anatumiza uthenga woitana Yakobo atate ake ndi abale ake onse. Ndipo onse pamodzi anali anthu 75. 15 Ndiyeno Yakobo anapita ku Iguputo, ndipo anafela kumeneko. Nawonso makolo athu akale anafela kumeneko. 16 Kenako, mafupa awo anatengedwa n’kupita nawo ku Sekemu kumene anaikidwa m’manda, amene Abulahamu anagula ndi ndalama zasiliva kwa ana a Hamori ku Sekemu.
17 “Pamene nthawi inali kuyandikila yakuti lonjezo limene Mulungu anauza Abulahamu likwanilitsidwe, anthuwo anaculuka kwambili ku Iguputo. 18 Kenako mfumu ina inayamba kulamulila Iguputo, mfumuyo sinali kumudziwa Yosefe. 19 Mfumu imeneyo inawacenjelela anthu a mtundu wathu, ndipo inakakamiza makolo athu amenewo kusiya makanda awo kuti asakhale ndi moyo. 20 Panthawiyo Mose anabadwa, ndipo anali wokongola m’maso mwa Mulungu. Iye analeledwa m’nyumba ya atate ake kwa miyezi itatu. 21 Koma pamene anamusiya yekha, mwana wamkazi wa Farao anamutenga n’kuyamba kumulela ngati mwana wake. 22 Conco Mose anaphunzitsidwa nzelu zonse za Aiguputo. Ndiponso anali wamphamvu m’zokamba komanso m’zocita zake.
23 “Tsopano iye atakwanitsa zaka 40, anaganiza zopita kukaona* abale ake, ana a Isiraeli. 24 Mose ataona Mwisiraeli akuzunzidwa, anamuteteza ndipo anabwezela mwa kupha Mwiguputo amene anali kuzunza Mwisiraeliyo. 25 Mose anali kuganiza kuti abale ake adzazindikila kuti Mulungu akuwapulumutsa kudzela m’dzanja lake. Koma iwo sanazindikile zimenezo. 26 Tsiku lotsatila iye anaonekela kwa iwo pamene anali kumenyana. Ndipo anayesa kuwayanjanitsa mwa mtendele n’kuwauza kuti, ‘Amuna inu m’pacibale. N’cifukwa ciyani mukuzunzana?’ 27 Koma amene anali kuzunza mnzakeyo anakankha Mose n’kunena kuti: ‘Ndani anakuika kukhala wolamulila komanso woweluza wathu? 28 Kodi ukufuna kundipha mmene unaphela Mwiguputo uja dzulo?’ 29 Iye atamva izi, anathawa n‘kupita kukakhala mlendo m’dziko la Midiyani. Kumeneko anabeleka ana aamuna awili.
30 “Patapita zaka 40, mngelo anaonekela kwa iye m’cipululu ku Phili la Sinai, m’citsamba caminga coyaka moto walawilawi. 31 Mose ataona zimenezi anadabwa kwambili. Koma pamene anali kuyandikila kuti ayang’anitsitse, pa citsambaco panamveka mawu a Yehova akuti: 32 ‘Ine ndine Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abulahamu, wa Isaki komanso wa Yakobo.’ Conco Mose anayamba kunjenjemela, ndipo sanapitilize kuyang’anitsitsa pa citsambaco. 33 Yehova anamuuza kuti: ‘Vula nsapato kumapazi ako, cifukwa malo amene waimapowa ndi oyela. 34 Ine ndaona kupondelezedwa kwa anthu anga ku Iguputo. Ndamva kubuula kwawo, ndipo ndatsika kudzawapulumutsa. Tsopano tamvela, ndikutuma ku Iguputo.’ 35 Mose ameneyo ndi uja amene iwo anamukana n’kunena kuti, ‘Ndani anakuika kukhala wolamulila komanso woweluza?’ Ameneyo ndi amene Mulungu anamutuma monga wolamulila komanso wowaombola kudzela mwa mngelo amene anaonekela kwa iye m’citsamba caminga. 36 Munthu ameneyu anawatsogolela n’kutuluka nawo, ndipo anacita zodabwitsa komanso zizindikilo ku Iguputo, pa Nyanja Yofiila ndiponso m’cipululu kwa zaka 40.
37 “Uyu ndi Mose amene anauza ana Aisiraeli kuti: ‘Mulungu adzakuutsilani mneneli ngati ine pakati pa abale anu.’ 38 Ameneyu ndi amene anali pakati pa Aisiraeli m’cipululu pamodzi ndi mngelo amene analankhula naye, komanso makolo athu pa Phili la Sinai. Iye analandila mawu a Mulungu amoyo n’kutipatsa. 39 Makolo athu anakana kumumvela. Koma anamukankhila kumbali ndipo m’mitima yawo anabwelela ku Iguputo. 40 Iwo anauza Aroni kuti: ‘Tipangile milungu ititsogolele cifukwa sitidziwa zimene zacitikila Mose amene anatitsogolela pocoka m’dziko la Iguputo.’ 41 Conco m’masiku amenewo iwo anapanga fano la mwana wa ng’ombe. Atatelo, anabweletsa nsembe n’kuzipeleka kwa fanolo, ndipo anayamba kusangalala ndi nchito ya manja awo. 42 Conco Mulungu anawasiya kuti atumikile zakumwamba* monga mmene zinalembedwela m’buku la Aneneli kuti: ‘Inu nyumba ya Isiraeli kodi munali kupeleka nsembe ndi zopeleka zina kwa ine kwa zaka 40 m’cipululu? 43 Inuyo munali kunyamula cihema ca Moloki ndi nyenyezi ya mulungu wochedwa Refani, mafano amene munapanga kuti muziwalambila. Conco ndidzakupitikitsilani kutali kupitilila ku Babulo.’
44 “Makolo athu akale anali ndi cihema ca umboni m’cipululu. Cihemaci cinali kuonetsa kuti Mulungu ali nawo. Mulungu anauza Mose kuti acipange, ndipo anacipanga mogwilizana ndi pulani imene Mulungu anamuonetsa. 45 Makolo athu analandila cihemaci kucokela kwa makolo awo, ndipo analowa naco pamodzi ndi Yoswa m’dziko limene linali la anthu a mitundu ina. Anthu amenewa Mulungu anawapitikitsa pamaso pa makolo athu. Ndipo cihemaco cinakhalapobe mpaka m’masiku a Davide. 46 Mulungu anamukomela mtima Davide, ndipo iye anapempha kuti apatsidwe mwayi wakuti amange nyumba yoti Mulungu wa Yakobo azikhalamo. 47 Koma Solomo ndi amene anamangila Mulungu nyumba. 48 Komabe, Wam’mwambamwamba sakhala m’nyumba zopangidwa ndi manja, malinga ndi mmene mneneli anakambila kuti: 49 ‘Yehova anakamba kuti, Kumwamba ndiko mpando wanga wacifumu, ndipo dziko lapansi ndi copondapo mapazi anga. Kodi nyumba imene mufuna kundimangila idzakhala yotani? Nanga malo anga opumulilako ali kuti? 50 Kodi dzanja langa si limene linapanga zinthu zonsezi?’
51 “Anthu okanga inu, komanso osacita mdulidwe wamumtima ndi wam’makutu. Nthawi zonse mumatsutsa mzimu woyela, mumacita zinthu monga mmene makolo anu anali kucitila. 52 Kodi ndi mneneli uti amene makolo anu sanazunze? Iwo anapha aja amene anali kulengezelatu za kubwela kwa wolungamayo, amene inu munamupeleka ndi kumupha. 53 Mulungu anagwilitsa nchito angelo kuti akupatseni Cilamulo, koma inu simunacitsatile.”
54 Iwo atamva zimenezi anakwiya* kwambili m’mitima yawo, ndipo anayamba kumukukutila mano. 55 Koma iye atadzazidwa ndi mzimu woyela, anayang’ana kumwamba n’kuona ulemelelo wa Mulungu, ndiponso Yesu ataimilila kudzanja lamanja la Mulungu. 56 Ndipo iye anati: “Taonani! Ndikuona kumwamba kwatseguka, ndipo Mwana wa munthu waimilila kudzanja la manja la Mulungu.” 57 Iwo atamva zimenezi anafuula kwambili, ndipo anatseka matu awo ndi manja. Kenako onse anathamangila pa iye. 58 Atamutulutsila kunja kwa mzinda anayamba kumuponya miyala. Ndipo mboni zija zinaika zovala zawo zakunja ku mapazi a mnyamata wina dzina lake Saulo. 59 Pamene anthuwo anali kumuponya miyala, Sitefano anacondelela kuti: “Ambuye Yesu, landilani mzimu wanga.” 60 Kenako anagwada n’kufuula ndi mawu amphamvu kuti: “Yehova, musawaimbe mlandu wa chimoli.” Atakamba zimenezi, anafa.*