Macitidwe a Atumwi
16 Kenako Paulo anafika ku Debe komanso ku Lusitara. Kumeneko kunali wophunzila wina dzina lake Timoteyo, mwana amene mayi ake anali Myuda wokhulupilila, koma atate ake anali Mgiriki. 2 Abale a ku Lusitara ndi ku Ikoniyo anamucitila umboni wabwino. 3 Paulo anaonetsa kuti akufuna kutenga Timoteyo pa ulendo wake. Conco anamutenga ndi kumucita mdulidwe cifukwa ca Ayuda amene anali kumeneko, popeza onse anali kudziwa kuti atate ake ndi Mgiriki. 4 Pamene anali kupita m’mizinda, anali kupatsa okhulupilila a kumeneko malamulo oyenela kuwatsatila, mogwilizana ndi zimene atumwi komanso akulu ku Yerusalemu anagamula. 5 Conco mipingo inapitiliza kukhala yolimba m’cikhulupililo, ndipo ciwelengelo ca ophunzila cinali kuwonjezeka tsiku lililonse.
6 Kenako iwo anadzela ku Fulugiya komanso m’dziko la Galatiya, cifukwa mzimu woyela unawaletsa kulankhula mawu a Mulungu m’cigawo ca Asia. 7 Ndiyeno atafika ku Musiya anayesetsa kuti apite ku Bituniya, koma mzimu wa Yesu sunawalole. 8 Conco anangodutsamo m’cigawo ca Musiya n’kukafika ku Torowa. 9 Ndiyeno usiku Paulo anaona masomphenya. Anaona munthu wa ku Makedoniya ataimilila akumupempha kuti: “Wolokelani kuno ku Makedoniya mudzatithandize.” 10 Iye atangoona masomphenyawo, tinaganiza zopita ku Makedoniya. Tinali otsimikiza kuti Mulungu ndiye watiitana kuti tikalengeze uthenga wabwino kwa anthu a kumeneko.
11 Conco tinanyamuka ulendo wa panyanja kucoka ku Torowa kupita ku Samatirake. Koma tsiku lotsatila tinapita ku Neapoli. 12 Titacoka kumeneko tinapita ku Filipi, mzinda wolamulidwa ndi Aroma, umenenso ndi wofunika kwambili m’cigawo ca Makedoniya. Tinakhala mumzindawu kwa masiku angapo. 13 Tsiku la Sabata tinatuluka pageti n’kupita m’mbali mwa mtsinje, kumene tinali kuganiza kuti kuli malo opemphelela. Ndipo tinakhala pansi n’kuyamba kulankhula ndi azimayi amene anasonkhana komweko. 14 Pa gulu la azimayiwo panali mayi wina dzina lake Lidiya, ndipo anali kugulitsa zovala za mtundu wapepo. Iye anali wocokela mumzinda wa Tiyatira, ndipo anali wolambila Mulungu. Pamene anali kumvetsela, Yehova anatsegula mtima wake kwambili kuti amvetse zimene Paulo anali kulankhula. 15 Iye ndi a m’banja lake atabatizika, anaticondelela kuti: “Ngati muona kuti ndine wokhulupilika kwa Yehova, tiyeni mukakhale kunyumba kwanga.” Moti anatiumiliza ndithu kuti tipite naye kwawo.
16 Tsopano pamene tinali kupita kumalo opemphelela, tinakumana ndi mtsikana wina wogwidwa ndi mzimu, womwe ndi ciwanda coloseletsa zakutsogolo. Iye anapangitsa mabwana ake kupeza phindu kwambili, cifukwa ca zolosela zake. 17 Mtsikanayu anali kungotsatila Paulo limodzi ndi ife n’kumafuula kuti: “Anthu awa ndi akapolo a Mulungu Wapamwambamwamba, ndipo akulengeza kwa inu njila ya cipulumutso.” 18 Iye anacita zimenezi kwa masiku ambili. Pothela pake Paulo anafika potopa nazo, ndipo anaceuka n’kuuza mzimuwo kuti: “Ndikukulamula m’dzina la Yesu Khristu kuti utuluke mwa mtsikanayu.” Ndipo mzimuwo unatuluka nthawi yomweyo.
19 Ndiyeno mabwana ake aja ataona kuti sadzapezanso phindu, anagwila Paulo ndi Sila ndi kuwaguzila mumsika, kubwalo la olamulila. 20 Atafika nawo kwa akuluakulu a zamalamulo, iwo ananena kuti: “Anthu awa akusokoneza kwambili mzinda wathu, ndipo ndi Ayuda. 21 Akufalitsa miyambo imene kwa ife ndi yosaloleka kuitsatila kapena kuicita, cifukwa ndife Aroma.” 22 Kenako gulu lonselo linawaukila atumwiwo. Ndipo akuluakulu a zamalamulowo, anavula atumwiwo zovala mocita kuwang’ambila n’kulamula kuti awakwapule ndi ndodo. 23 Atawakwapula zikoti zambili, anawatsekela m’ndende ndi kulamula woyang’anila ndendeyo kuti aziwalonda mokwana kuti asathawe. 24 Popeza kuti woyang’anila ndendeyo analamulidwa zimenezi, iye anakawatsekela m’cipinda camkati ca ndendeyo ndi kumanga mapazi awo m’matangadza.
25 Koma capakati pa usiku, Paulo ndi Sila anayamba kupemphela ndiponso kutamanda Mulungu mwa kuimba nyimbo, ndipo akaidi ena anali kumvetsela. 26 Mwadzidzidzi panacitika civomezi camphamvu, moti maziko a ndendeyo anagwedezeka. Nthawi yomweyo zitseko zonse zinatseguka, ndipo aliyense unyolo wake unamasuka. 27 Woyang’anila ndende uja atauka n’kuona kuti zitseko za ndende n’zotseguka, anasolola lupanga lake kuti adziphe, cifukwa anaganiza kuti akaidiwo athawa. 28 Koma Paulo anafuula kuti: “Usadzivulaze, cifukwa tonse tilipo!” 29 Iye anapempha nyale ndipo anathamangila mkatimo. Akunjenjemela ndi mantha, anagwada pamaso pa Paulo ndi Sila. 30 Kenako anawatulutsa panja n’kunena kuti: “Inu mabwana, ndiyenela kucita ciyani kuti ndipulumuke?” 31 Iwo anati: “Khulupilila Ambuye Yesu ndipo udzapulumuka, pamodzi ndi anthu a m’banja lako.” 32 Ndiyeno anamuuza mawu a Yehova pamodzi ndi onse a m’nyumba yake. 33 Kenako anawatenga usiku womwewo ndi kutsuka mabala awo. Ndiyeno posapita nthawi iye ndi onse a m’banja lake anabatizika. 34 Kenako anawalowetsa m’nyumba mwake n’kuwaikila cakudya pathebulo. Ndipo iye ndi a m’banja lake onse anakondwela kwambili cifukwa anakhulupilila Mulungu.
35 Kutaca m’mawa, akuluakulu a zamalamulo anatumiza asilikali kukauza woyang’anila ndende kuti: “Amasuleni anthu awa.” 36 Woyang’anila ndende uja anauza Paulo uthengawo kuti: “Akuluakulu a zamalamulo atumiza anthu kudzanena kuti awilinu mumasulidwe. Conco tulukani tsopano, ndipo mupite mu mtendele.” 37 Koma Paulo anawauza kuti: “Iwo anatikwapula pamaso pa anthu n’kutiponya m’ndende popanda kutiweluza,* ngakhale kuti ndife Aroma. Koma tsopano akufuna kutitulutsa mobisa? Ayi, sitilola! Auzeni iwo abwele adzatipelekeze potuluka.” 38 Ndiyeno asilikaliwo anapita kukafotokoza zimenezi kwa akuluakulu a zamalamulo aja. Akuluakulu a zamalamulowo atamva kuti anthuwo ndi Aroma anacita mantha kwambili. 39 Conco iwo anabwela n’kuwacondelela, ndipo atawapelekeza powatulutsa anawapempha kuti acoke mumzindawo. 40 Koma atatuluka m’ndendemo anapita kunyumba kwa Lidiya. Iwo ataona abale, anawalimbikitsa, kenako ananyamuka n’kumapita.