Kalata Yoyamba kwa Akorinto
5 Mbili yamveka kuti pakati panu pakucitika ciwelewele,* ndipo mtundu wa ciweleweleco* ndi woti ngakhale anthu a mitundu ina sacita. Akuti mwamuna wina anatengana ndi mkazi wa atate ake. 2 Kodi inu mukusangalala nazo zimenezi m’malo momva cisoni, kuti munthu amene anacita zimenezi acotsedwe pakati panu? 3 Ngakhale kuti thupi langa silili kumeneko, mwauzimu ndili kumeneko, ndipo ndamuweluza kale munthu amene anacita zimenezi, ngati kuti ndili nanu limodzi. 4 Mukasonkhana m’dzina la Ambuye wathu Yesu, mudziwe kuti mwamzimu komanso m’mphamvu ya Ambuye wathu Yesu ndili nanu limodzi. 5 Conco, m’pelekeni kwa Satana munthu ameneyo kuti thupilo lionongedwe, n’colinga coti mzimuwo ukapulumutsidwe m’tsiku la Ambuye.
6 Kudzitama kwanu si kwabwino. Kodi simukudziwa kuti yisiti wocepa amafufumitsa mtanda wonse? 7 Cotsani yisiti wa kaleyo kuti mukhale mtanda watsopano, popeza ndinu opanda zofufumitsa. Cifukwa Khristu wapelekedwa ngati nkhosa ya nsembe yathu ya Pasika. 8 Conco tiyeni ticite cikondwelelo ca Pasika cimeneci osati ndi yisiti wakale kapena yisiti woimila zoipa ndi ucimo, koma ndi mkate wopanda yisiti woimila kuona mtima ndi coonadi.
9 M’kalata yanga, ndinakulembelani kuti muleke kugwilizana ndi anthu aciwelewele.* 10 Sindikutanthauza kuti muzipewelatu anthu aciwelewele* a m’dzikoli kapenanso adyela, olanda ndi opembedza mafano. Zikanakhala conco ndiye kuti mukanafunika kutuluka m’dzikoli. 11 Koma tsopano ndikukulembelani kuti muleke kugwilizana ndi aliyense wochedwa m’bale amene ndi waciwelewele* kapena wadyela, wopembedza mafano, wolalata,* cidakwa kapenanso wolanda, ngakhale kudya naye munthu woteleyu n’kosayenela. 12 Nanga ndi udindo wanga ngati kuweluza anthu amene ali kunja? Kodi si paja inu mumaweluza anthu amene ali mkati, 13 pamene Mulungu amaweluza amene ali kunja? “M’cotseni munthu woipayo pakati panu.”