Wolembedwa na Maliko
16 Tsiku la Sabata litatha, Mariya Mmagadala, Mariya mayi ake a Yakobo, na Salome anagula zonunkhilitsa kuti apite ku manda kukapaka mtembo wa Yesu. 2 Ndipo m’mamaŵa pa tsiku loyamba la mlunguwo dzuŵa litatuluka, iwo anafika ku mandako.* 3 Anali kufunsana kuti: “Ndani atikunkhunizile cimwala kucicotsa pa khomo la manda?” 4 Koma atayang’ana pa khomo la mandawo, anaona kuti cimwala cija cakunkhunizidwa kale ngakhale kuti cinali cacikulu kwambili. 5 Ataloŵa m’mandamo, anaona mnyamata wovala mkanjo woyela atakhala pansi ku dzanja lamanja, ndipo iwo anadabwa kwambili. 6 Iye anawauza kuti: “Musadabwe. Nidziŵa kuti mukufuna-funa Yesu Mnazareti amene anaphedwa pa mtengo. Iye anaukitsidwa ndipo sali muno. Onani, apa m’pamene anamuika. 7 Koma pitani mukauze ophunzila ake na Petulo kuti, ‘Iye watsogola kupita ku Galileya. Mukamuona kumeneko monga anakuuzilani.’” 8 Atatuluka m’mandamo, anathaŵa akunjenjemela komanso ali odabwa kwambili. Ndipo sanauze aliyense zimene zinacitikazo cifukwa anali na mantha kwambili.*