LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • Agalatiya 6
  • Baibo ya Cimasulilo ca Dziko Latsopano

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

Za m’Buku la Agalatiya

      • Muzinyamuzana mitolo (1-10)

        • Timakolola zimene tabzyala (7, 8)

      • Kucita mdulidwe kulibe phindu (11-16)

        • Kulengedwa mwatsopano (15)

      • Mau othela (17, 18)

Agalatiya 6:1

Amlongoza a Zofalitsa

  • Buku Lofufuzila Nkhani

    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!, phunzilo 57

Agalatiya 6:2

Amlongoza a Zofalitsa

  • Buku Lofufuzila Nkhani

    Nsanja ya Mlonda (Yophunzila),

    5/2019, masa. 2-4

    Nsanja ya Mlonda,

    3/15/2015, tsa. 29

Agalatiya 6:4

Amlongoza a Zofalitsa

  • Buku Lofufuzila Nkhani

    Nsanja ya Mlonda (Yophunzila),

    7/2021, masa. 20-25

    Nsanja ya Mlonda (Yophunzila),

    8/2020, masa. 23-24

Agalatiya 6:5

Mawu amunsi

  • *

    Kapena kuti, “ayenela kusamalila udindo wake.”

Agalatiya 6:7

Amlongoza a Zofalitsa

  • Buku Lofufuzila Nkhani

    Galamuka!,

    na. 1 2021 tsa. 11

Agalatiya 6:9

Amlongoza a Zofalitsa

  • Buku Lofufuzila Nkhani

    Nsanja ya Mlonda (Yophunzila),

    10/2021, masa. 24-28

Agalatiya 6:10

Mawu amunsi

  • *

    Kapena kuti, “ngati tili ndi mpata.”

Amlongoza a Zofalitsa

  • Buku Lofufuzila Nkhani

    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!, phunzilo 44

Agalatiya 6:12

Mawu amunsi

  • *

    Onani Matanthauzo a Mau Ena.

Agalatiya 6:17

Mawu amunsi

  • *

    Kapena kuti, “ndi cidindo coonetsa kuti ndine kapolo.”

  • Baibo ya Cimasulilo ca Dziko Latsopano
  • 1
  • 2
  • 3
  • 4
  • 5
  • 6
  • 7
  • 8
  • 9
  • 10
  • 11
  • 12
  • 13
  • 14
  • 15
  • 16
  • 17
  • 18
Baibo ya Cimasulilo ca Dziko Latsopano
Agalatiya 6:1-18

Kwa Agalatiya

6 Abale, ngati munthu wapatuka n’kuyamba kutenga njila yolakwika mosadziwa, inu oyenelela mwauzimu yesani kumuthandiza munthu woteloyo ndi mzimu wofatsa. Koma pamene mukutelo, inunso khalani maso kuopela kuti mungayesedwe. 2 Pitilizani kunyamuzana mitolo yolemela, ndipo mwa njila imeneyi mudzakhala mukukwanilitsa cilamulo ca Khristu. 3 Pakuti ngati wina akudziona kuti ndi wofunika koma sali kanthu, akudzinamiza yekha. 4 Koma aliyense asanthule nchito zake kuti aone kuti ndi zotani. Akatelo adzakhala ndi cifukwa cosangalalila, osati modziyelekezela ndi munthu wina. 5 Pakuti aliyense ayenela kunyamula katundu wake.*

6 Ndiponso aliyense amene akuphunzitsidwa zinthu zabwino, agawane zinthu zonse zabwino ndi amene akumuphunzitsayo.

7 Musanamizidwe: Mulungu sapusitsika. Zilizonse zimene munthu wabzala, adzakololanso zomwezo. 8 Pakuti amene amabzala n’colinga copindulitsa thupi lake, adzakolola cionongeko kucokela m’thupi lakelo, koma amene akubzala n’colinga copindulitsa mzimu, adzakolola moyo wosatha kucokela ku mzimuwo. 9 Conco tisaleke kucita zabwino, cifukwa panyengo yake tidzakolola tikapanda kutopa. 10 Cotelo ngati tingathe,* tiyeni ticitile anthu onse zabwino, koma maka-maka abale ndi alongo athu m’cikhulupililo.

11 Taonani zilembo zikulu-zikulu zimene ndakulembelani ndi dzanja langali.

12 Onse amene akufuna kuti azioneka ngati abwino pamaso pa anthu, ndi amene akukuumilizani kuti muzicita mdulidwe. Amatelo kuti asazunzidwe cifukwa ca mtengo wozunzikilapo* wa Khristu. 13 Pakuti ngakhale amene akudulidwawo sasunga Cilamulo, koma akufuna kuti inu muzidulidwa kuti iwo azidzitama cifukwa ca zimene zacitika pathupi lanu. 14 Koma ine sindidzadzitama pa cifukwa cina ciliconse, kupatulapo cifukwa ca mtengo wozunzikilapo wa Ambuye wathu Yesu Khristu. Kwa ine, dziko linaweluzidwa kuti liphedwe kudzela mwa iye, koma malinga ndi kuona kwa dziko, ine ndinaweluzidwa kuti ndiphedwe kudzela mwa iye. 15 Pakuti kudulidwa kapena kusadulidwa si kanthu, koma cofunika ndi kukhala wolengedwa mwatsopano. 16 Koma kwa onse amene akuyenda molongosoka motsatila lamulo limeneli, mtendele ndi cifundo zikhale nao, inde zikhale ndi Isiraeli wa Mulungu.

17 Kuyambila tsopano pasapezeke munthu wondibvutitsa, pakuti pa thupi langa ndili ndi zipsyela zoonetsa kuti ndine kapolo* wa Yesu.

18 Cisomo ca Ambuye wathu Yesu Khristu cikhale nanu abale, cifukwa ca makhalidwe abwino amene mumaonetsa. Ameni.

Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani