Kalata Yaciwiri kwa Akorinto
11 Ndikanakonda mukanandilola kuti ndidzikweze pang’ono. Ndipo zoona zake n’zakuti, mwandilola kale. 2 Nsanje imene ndimakucitilani ndi yofanana ndi ya Mulungu. Ndinakulonjezani mwamuna mmodzi, Khristu, kuti ndidzakupelekani kwa iye monga namwali woyela. 3 Koma nkhawa yanga ndi yakuti, monga mmene njoka inapusitsila Hava mocenjela, naonso maganizo anu angapotozedwe ndipo mungasiye kukhala oona mtima komanso oyela, makhalidwe amene munthu wa Khristu ayenela kukhala nao. 4 Pakuti ngati wina wabwela kwa inu ndi uthenga wosiyana ndi umene tinaulalikila, kapena wabweletsa mzimu wosiyana ndi umene munaulandila, kapenanso uthenga wabwino wosiyana ndi umene munaubvomeleza, inu mumangomulandila munthu woteloyo. 5 Koma ndikuona kuti sindine wotsika mwa njila iliyonse poyelekezela ndi atumwi anu apamwambawo. 6 Ngati ndilibe luso la kulankhula, sikuti ndine wosadziwanso zinthu ndipo tinakuonetsani zimenezi m’njila iliyonse komanso pa zinthu zonse.
7 Kodi ndinacimwa pamene ndinadzicepetsa kuti inuyo mukwezedwe, cabe cifukwa cakuti ndinalalikila uthenga wabwino wa Mulungu kwa inu kwaulele? 8 Ndinalandila thandizo kucokela kumipingo ina, ndipo kucita zimenezo kunali ngati kuwabela kuti ndikutumikileni inuyo. 9 Pamene ndinali nanu ndipo ndinafunikila thandizo, sindinakhale mtolo kwa aliyense wa inu, popeza abale a ku Makedoniya anandipatsa zimene ndinali kufunikila. Ndithu, ndinayesetsa kuti ndisakhale mtolo mwa njila iliyonse, ndipo ndikupitilizabe kutelo. 10 Popeza ndimalankhula coonadi ca Khristu, sindidzasiya kudzitamandila m’madela a ku Akaya. 11 Kodi ndikucita zimenezi pa cifukwa citi? Cifukwa cakuti sindikukondani? Ayi ndithu. Ngakhale Mulungu adziwa kuti ndimakukondani.
12 Ndipitiliza kucita zimene ndikucita, kuti ndisapatse mpata anthu amene akuyesetsa kupeza cifukwa conenela kuti ndi ofanana ndi ife pa zinthu zimene amadzitamandila. 13 Anthu amenewa ndi atumwi onama, anchito acinyengo, ndipo amadzicititsa kuoneka* ngati atumwi a Khristu. 14 Izi n’zosadabwitsa, cifukwa ngakhale Satana amadzicititsa kuoneka* ngati mngelo wakuwala. 15 Conco, n’zosadabwitsa ngati naonso atumiki ake amadzipangitsa kukhala* ngati atumiki acilungamo. Koma mapeto ao adzakhala monga mwa nchito zao.
16 Ndikubwelezanso kunena kuti, wina aliyense asandione ngati wopanda nzelu. Koma ngati mukundionabe kuti ndine wopanda nzelu, mungobvomeleza kuti ndi mmene ndilili, kuti nanenso ndidzitame pang’ono. 17 Zimene ndikunenazi, sindikuzinena ngati munthu wotsatila citsanzo ca Ambuye. Koma ngati munthu wopusa, wodzitama, komanso wodzidalila kwambili. 18 Popeza anthu ambili akudzitama cifukwa ca zinthu za m’dzikoli, inenso ndikudzitama. 19 Popeza mumadziona “anzelu” kwambili, sizimakubvutani kucita nao zinthu anthu opanda nzelu. 20 Ndipo mumalolela aliyense, kaya akupangeni akapolo ake, akutengeleni zinthu zanu, akulandeni zimene muli nazo, adzione kuti ndi wapamwamba kuposa inuyo, ndiponso aliyense amene wakuwazani mbama.
21 Ndikunena izi modzinyoza tokha, popeza ena angaone ngati tacita zinthu mofooka.
Koma ngati anthu ena akucita zinthu molimba mtima, ndikulankhula ngati wopanda nzelu, inenso ndikucita zinthu molimba mtima. 22 Kodi iwo ndi Aheberi? Inenso cimodzi-modzi. Kodi ndi Aisiraeli? Nanenso ndine Mwisiraeli. Kapena iwo ndi mbadwa* za Abulahamu? Inenso cimodzi-modzi. 23 Kodi iwo ndi atumiki a Khristu? Ndikuyankha ngati wamisala, ine ndiye mtumiki wa Khristu woposa iwo. Ndacita nchito zambili kuposa iwo, ndinaponyedwapo m’ndende mobweleza-bweleza, ndinamenyedwa kosawelengeka, ndipo ndinatsala pafupi kufa kambili-mbili. 24 Maulendo asanu Ayuda anandikwapula zikoti 39.* 25 Katatu anandimenya ndi ndodo. Kamodzi anandiponya miyala, katatu konse ngalawa inandiswekelapo, kamodzi ndinakhala panyanja usiku ndi masana onse. 26 Ndinayenda maulendo ambili-mbili, ndinakumana ndi zoopsa pa mitsinje, zoopsa za acifwamba, zoopsa kucokela kwa anthu a mtundu wanga, zoopsa zocokela kwa anthu a mitundu ina, ndinakumana ndi zoopsa m’mizinda, m’cipululu, panyanja, ndi pakati pa abale onyenga. 27 Ndinali kugwila nchito zolemetsa komanso zotulutsa thukuta. Nthawi zambili sindinali kugona usiku, ndinali kukhala ndi njala komanso ludzu. Nthawi zambilinso ndinali kukhala wosadya, ndinali kukongwa, komanso ndinalibe zobvala zokwanila.*
28 Kuonjezela pa izi, palinso cinthu cina cimene cimandibvutitsa maganizo tsiku ndi tsiku.* Ndimadela nkhawa mipingo yonse. 29 Ndani angafooke ine osafooka? Ndani angakhumudwitsidwe ine osakwiya nazo?
30 Ngati ndiyenela kudzitama, ndidzadzitamandila pa zinthu zimene zimaonetsa kufooka kwanga. 31 Mulungu komanso Atate wa Ambuye Yesu, amene ndi woyenela kumutamanda mpaka muyaya akudziwa kuti sindikunama. 32 Ku Damasiko, bwanamkubwa wa Areta mfumu anaika alonda pamageti a mzinda wa Damasiko kuti andigwile. 33 Koma anthu anandiika m’dengu n’kunditsitsila pawindo ya mpanda wa mzindawo, ndipo ndinapulumuka m’manja mwake.