Kalata Yaciwiri kwa Akorinto
4 Conco, popeza tili ndi utumiki umenewu mwa cifundo cimene anaticitila, sititaya mtima. 2 Koma taleka zinthu zocititsa manyazi zocitikila mseli, ndipo sitiyenda mwacinyengo kapena kuipitsa mau a Mulungu. Koma podziwikitsa coonadi, takhala citsanzo cabwino kwa munthu aliyense pamaso pa Mulungu. 3 Ndipo ngati uthenga wabwino umene tikulalikila ndi wophimbika, ndi wophimbika kwa anthu amene akupita kucionongeko. 4 Pakati pa anthu amenewa, mulungu wa nthawi ino wacititsa khungu maganizo a anthu osakhulupilila kuti asaone kuwala kwa uthenga wabwino waulemelelo wokamba za Khristu yemwe ndi cifanizilo ca Mulungu. 5 Pakuti sitikulalikila za ife koma za Yesu Khristu, kuti ndi Ambuye ndipo ife ndife akapolo anu cifukwa ca Yesu. 6 Popeza Mulungu ndiye anakamba kuti: “Kuwala kuunike kucokela mu mdima.” Iye waunika mitima yathu kuti ikhale yowala. Wacita zimenezi mwa kugwilitsa nchito cidziwitso caulemelelo ca Mulungu kudzela pa nkhope ya Khristu.
7 Koma tili ndi cuma cimeneci m’ziwiya zadothi,* kuti mphamvu yoposa yacibadwa icokele kwa Mulungu, osati kwa ife. 8 Timapanikizika m’njila zosiyana-siyana, koma osati mpaka kufika popsyinjika moti n’kulephela kusuntha. Timathedwa nzelu, koma osati mpaka kusowelatu kothawila.* 9 Timazunzidwa, koma sitisiyidwa tokha. Timagwetsedwa, koma sitiphwanyika.* 10 Nthawi zonse timapilila mazunzo amene tingafe nao ngati aja amene Yesu anapilila, ndipo timacita zimenezi kuti moyo umene Yesu anali nao uonekelenso mwa ife.* 11 Pakuti ife amene tili moyo, nthawi zonse timayang’anizana ndi imfa cifukwa ca Yesu, n’colinga cakuti moyo wa Yesu uonekelenso m’matupi athu amene angafe. 12 Conco ife tili pa ciopsezo cakuti tikhoza kufa, koma inu moyo ndi wanu.
13 Tsopano ife tili ndi cikhulupililo* mofanana ndi zimene zinalembedwa kuti: “Ndinali ndi cikhulupililo, n’cifukwa cake ndinalankhula.” Nafenso tili ndi cikhulupililo, n’cifukwa cake timalankhula, 14 podziwa kuti amene anaukitsa Yesu ifenso adzatiukitsa mmene anacitila ndi Yesu, ndipo iye adzatipeleka kwa Yesu pamodzi ndi inu. 15 Zonsezi zacitika kaamba ka ubwino wanu, kuti cisomo ca Mulungu cimene cikuonjezeka, cionjezekebe cifukwa anthu ambili akupeleka mapemphelo oyamikila, ndipo izi zikupeleka ulemelelo kwa Mulungu.
16 Conco sititaya mtima, ngakhale kuti munthu wathu wakunja akutha, mosakaika munthu wathu wamkati akukhala watsopano tsiku ndi tsiku. 17 Ndipo ngakhale kuti masautso* amene tikukumana nao ndi akanthawi komanso opepuka, amacititsa kuti tilandile ulemelelo umene ukuonjezeka-onjezekela, umenenso ndi wamuyaya. 18 Pamene tikuika maso athu pa zinthu zosaoneka, osati pa zinthu zooneka, cifukwa zooneka n’zakanthawi, koma zosaoneka n’zamuyaya.