LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • Agalatiya 1
  • Baibo ya Cimasulilo ca Dziko Latsopano

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

Za m’Buku la Agalatiya

      • Moni (1-5)

      • Palibe uthenga wina wabwino (6-9)

      • Uthenga wabwino umene Paulo analalikila ndi wocokela kwa Mulungu (10-12)

      • Kutembenuka kwa Paulo komanso nchito zake zoyambilila (13-24)

Agalatiya 1:13

Mawu amunsi

  • *

    Kucokela ku Cigiriki, “Ndinafika pozunza mopambanitsa mpingo wa Mulungu.”

Agalatiya 1:16

Mawu amunsi

  • *

    Kucokela ku Cigiriki, “kwa anthu athupi la nyama ndi magazi.”

Agalatiya 1:18

Mawu amunsi

  • *

    Wochedwanso Petulo.

  • Baibo ya Cimasulilo ca Dziko Latsopano
  • 1
  • 2
  • 3
  • 4
  • 5
  • 6
  • 7
  • 8
  • 9
  • 10
  • 11
  • 12
  • 13
  • 14
  • 15
  • 16
  • 17
  • 18
  • 19
  • 20
  • 21
  • 22
  • 23
  • 24
Baibo ya Cimasulilo ca Dziko Latsopano
Agalatiya 1:1-24

Kwa Agalatiya

1 Ndine mtumwi Paulo. Sindine mtumwi wocokela kwa anthu kapena wotumidwa ndi munthu. Koma ndine mtumwi wosankhidwa ndi Yesu Khristu kudzela mwa Mulungu Atate amene anamuukitsa kwa akufa. 2 Ine pamodzi ndi abale onse amene ndili nao, tikupeleka moni ku mipingo ya ku Galatiya:

3 Cisomo komanso mtendele zocokela kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye wathu Yesu Khristu zikhale nanu. 4 Iye anadzipeleka kaamba ka macimo athu kuti atipulumutse ku nthawi ino yoipa, malinga ndi cifunilo ca Mulungu Atate wathu. 5 Ndipo ulemelelo upite kwa Mulunguyo mpaka muyaya. Ameni.

6 Ndikudabwa kuti mwapatuka mwamsanga kucoka kwa Mulungu amene anakuitanani mwa cisomo ca Khristu, ndipo mwakopeka ndi uthenga wabwino wa mtundu wina. 7 Sikuti palinso uthenga wina wabwino ai. Koma pali ena pakati panu amene akukusokonezani, ndipo akufuna kupotoza uthenga wabwino wonena za Khristu. 8 Ngakhale n’telo, ngati ife kapena mngelo wocokela kumwamba angalengeze uthenga wabwino wosiyana ndi uthenga wabwino umene tinaulengeza kwa inu, ameneyo akhale wotembeleledwa. 9 Ndipo monga ndakambila kale, ndibwelezanso kuti, ngati kuli aliyense amene akulengeza uthenga wabwino wosiyana ndi umene munaulandila kale, munthu ameneyo akhale wotembeleledwa.

10 Kodi ndikufuna kuti anthu azindikonda kapena kuti Mulungu azindikonda? Kapena kodi ndikuyesa kukondweletsa anthu? Ndikanafuna kupitiliza kukondweletsa anthu, sindikanakhala kapolo wa Khristu. 11 Ndikufuna kuti mudziwe abale, kuti uthenga wabwino umene ndinaulengeza kwa inu sunacokele kwa anthu. 12 Sindinaulandile kucokela kwa munthu aliyense, ndipo sindinacite kuphunzitsidwa. Koma Yesu Khristu ndiye anandiululila uthengawu.

13 Munamva zimene ndinali kucita pamene ndinali m’Ciyuda. Ndinali kuzunza mpingo wa Mulungu koopsa,* ndipo ndinali kuusakaza. 14 Ndinali kucita bwino kwambili m’Ciyuda kuposa Ayuda anzanga ambili a msinkhu wanga, cifukwa ndinali wokangalika kwambili pa miyambo ya makolo anga. 15 Koma Mulungu amene anacititsa kuti ndibadwe, komanso amene anandiitana mwa cisomo cake, anaona kuti m’poyenela kuti 16 aulule za Mwana wake kudzela mwa ine. Anatelo kuti ndilengeze uthenga wabwino wokhudza iye kwa anthu a mitundu ina. Ataulula zimenezi ine sindinapite kukafunsila kwa munthu aliyense* nthawi yomweyo. 17 Sindinapitenso ku Yerusalemu kwa amene anakhala atumwi ine ndisanakhale, koma ndinapita ku Arabiya, kenako ndinabwelelanso ku Damasiko.

18 Ndiyeno patapita zaka zitatu, ndinapita ku Yerusalemu kukaonana ndi Kefa,* ndipo ndinakhala naye masiku 15. 19 Koma sindinaonane ndi atumwi ena onse kupatulapo Yakobo, m’bale wa Ambuye. 20 Ndikukutsimikizilani pamaso pa Mulungu kuti zimene ndikukulembelanizi sindikunama.

21 Kenako ndinapita m’zigawo za Siriya ndi Kilikiya. 22 Koma mipingo ya ku Yudeya yomwe inali yogwilizana ndi Khristu, siinali kundidziwa bwino-bwino. 23 Iwo anali kungomva mbili yakuti: “Munthu uja amene anali kutizunza kale, tsopano akulengeza uthenga wabwino wonena za cikhulupililo cimene kale anali kucisakaza.” 24 Conco iwo anayamba kupeleka ulemelelo kwa Mulungu cifukwa ca ine.

Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani