Kalata Yaciwiri kwa Akorinto
6 Pamene tikugwila nchito naye limodzi, tikukulimbikitsani kuti musalandile cisomo ca Mulungu n’kuphonya colinga ca cisomoco. 2 Cifukwa iye anati: “Pa nthawi yobvomelezeka ndinakumvela, ndipo pa tsiku la cipulumutso ndinakuthandiza.” Ndithudi, ino ndiyo nthawi yeniyeni yobvomelezeka. Lelo ndilo tsiku la cipulumutso.
3 Sitikucita ciliconse cokhumudwitsa, kuti anthu asaupeze cifukwa utumiki wathu . 4 Koma m’njila iliyonse, tikuonetsa kuti ndife atumiki a Mulungu. Tikucita zimenezi popilila mabvuto ambili, pokumana ndi masautso, pokhala opanda zinthu zofunikila, pokumana ndi zobvuta, 5 pomenyedwa, poikidwa m’ndende, pokumana ndi zipolowe, pogwila nchito mwakhama, posagona tulo, komanso posowa cakudya. 6 Tikucitanso zimenezi mwa kukhala oyela, acidziwitso , oleza mtima, okoma mtima, potsogoleledwa ndi mzimu woyela, poonetsa cikondi copanda cinyengo, 7 polankhula zoona, komanso pokhala ndi mphamvu ya Mulungu. Ndiponso tikucita zimenezi ponyamula zida zacilungamo kudzanja lamanja komanso lamanzele, 8 popatsidwa ulemelelo komanso ponyozedwa, poneneledwa zoipa komanso zabwino. Timaonedwa ngati anthu acinyengo koma ndife acilungamo, 9 ngati osadziwika koma ndife odziwika bwino, ngati kuti tikufa koma tikukhalabe ndi moyo, ngati olandila cilango koma osapita kukaphedwa, 10 ngati acisoni koma acimwemwe nthawi zonse, ngati osauka koma olemeletsa anthu oculuka, ngati anthu opanda kalikonse koma okhala ndi zinthu zonse.
11 Tatsegula pakamwa pathu kuti tilankhule ndi inu* Akorinto, ndipo tafutukula mtima wathu. 12 Ife sitimaumila pokuonetsani cikondi, koma inu mumaumila potionetsa cikondi. 13 N’cifukwa cake ndikulankhula nanu ngati ana anga, kuti inunso muzifutukula mitima yanu.*
14 Musamangidwe mu joko ndi anthu osakhulupilila, cifukwa ndinu osiyana. Kodi pali mgwilizano wanji pakati pa cilungamo ndi kuphwanya malamulo? Kapena pali kugwilizana kotani pakati pa kuwala ndi mdima? 15 Komanso pali mgwilizano wotani pakati pa Khristu ndi Beliyali?* Kapena munthu wokhulupilila* angagawane ciani ndi munthu wosakhulupilila? 16 Ndipo pali kugwilizana kotani pakati pa kacisi wa Mulungu ndi mafano? Pakuti ife ndife kacisi wa Mulungu wamoyo, monga mmene Mulungu anakambila kuti: “Ndidzakhala pakati pao komanso kuyenda pakati pao. Ndidzakhala Mulungu wao, ndipo iwo adzakhala anthu anga.” 17 “‘Conco cokani pakati pao ndipo mulekane nao,’ watelo Yehova. ‘Musakhudze cinthu codetsedwa,’” “‘ndipo ine ndidzakulandilani.’” 18 “‘Ndidzakhala atate wanu ndipo inu mudzakhala ana anga aamuna ndi aakazi,’ watelo Yehova Wamphamvuzonse.”