Kalata Yaciwiri kwa Akorinto
1 Ine Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa cifunilo ca Mulungu, ndili limodzi ndi Timoteyo m’bale wathu, ndipo ndikulembela mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto, kuphatikizapo oyela onse okhala m’cigawo conse ca Akaya.
2 Cisomo ndi mtendele zocokela kwa Mulungu Atate wathu komanso kwa Ambuye wathu Yesu Khristu, zikhale nanu.
3 Atamandike Mulungu komanso Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Tate wacifundo cacikulu, Mulungu amene amatitonthoza pa bvuto lililonse. 4 Iye amatitonthoza* pa mayeso* athu onse, kotelo kuti ifenso tizitonthoza ena pa mayeso* alionse ndi citonthozo cocokela kwa Mulungu. 5 Pamene tikukumana ndi zowawa zoculuka cifukwa ca Khristu, timalandilanso citonthozo coculuka kudzela mwa Khristuyo. 6 Tikamakumana ndi mayeso,* timakumana ndi mayesowo kuti inuyo mutonthozedwe komanso kuti mupeze cipulumutso. Ndipo tikatonthozedwa, inunso mutonthozedwe cifukwa mumathandizika kupilila zowawa zimene ifenso tikukumana nazo. 7 Ciyembekezo cathu pa inu sicikugwedezeka, pakuti tikudziwa kuti mukukumana ndi zowawa ngati zathu, inunso mudzatonthozedwa.
8 Abale, tikufuna kuti mudziwe, za masautso amene tinakumana nao m’cigawo ca Asia. Mabvuto oposa msinkhu wathu anatipsyinja kwambili, moti tinali kukaikila ngati tipulumuke. 9 Ndipotu tinamva ngati atiweluza kuti tiphedwe. Zinatelo kuti tisadzidalile, koma tizidalila Mulungu amene amaukitsa akufa. 10 Iye anatipulumutsa ku zinthu zimene zikanatipha, ndipo adzatipulumutsanso. Sitikukaikila kuti adzapitiliza kutipulumutsa. 11 Inunso mungathandizepo mwa kutipelekela mapemphelo ocondelela, kuti pakhale anthu ambili otipelekela mapemphelo oyamikila thandizo limene Mulungu amapeleka, poyankha mapemphelo a anthu ambili.
12 Cifukwa cimene timadzitamandila ndi ici, cikumbumtima cathu cikuticitila umboni kuti m’dzikoli, tacita zinthu zoyela maka-maka kwa inuyo, mogwilizana ndi kuona mtima kocokela kwa Mulungu. Tacita izi, osati ndi nzelu za m’dzikoli, koma cifukwa ca cisomo ca Mulungu. 13 Pakuti sitikukulembelani zinthu zimene simungathe kuzimvetsa, koma zokhazo zimene mungathe kuziwelenga* ndi kuzimvetsa. Ndipo ndikhulupilila kuti zinthu zimenezi mupitiliza kuzimvetsa mokwanila.* 14 Monga mmene ena a inu mukudziwila kale, mukudzitamandila cifukwa ca ife ngati mmene ifenso tidzadzitamandile cifukwa ca inu pa tsiku la Ambuye wathu Yesu.
15 Conco ndi cidalilo cimeneci, ndinali kufuna kuti ndibwele kwa inu coyamba, kuti mudzakhalenso ndi mwai wina wosangalala.* 16 Cifukwa ndinali kufuna kuti paulendo wanga wopita ku Makedoniya ndidzadutsile kwanuko kudzakucezelani. Ndipo pocoka ku Makedoniya ndinali kufuna kuti ndidzadutsilenso kumekeko, kenako mudzandipelekeze popita ku Yudeya. 17 Pamene ndinali ndi colinga cimeneci, sindinaone nkhaniyi mopepuka. Zimene ndinali kufuna kucita sindinali kufuna kuzicita ndi colinga cadyela, kuti ndikati “Inde” nthawi yomweyo n’kusintha n’kukamba kuti “Ai.” 18 Koma khulupililani Mulungu kuti zimene tinakamba n’zoona. Sitingakuuzeni kuti “inde” kenako n’kusintha n’kunena kuti “ai.” 19 Pakuti Mwana wa Mulungu, Yesu Khristu, amene ine, Silivano,* ndi Timoteyo tinalalikila za iye, sakamba kuti “inde” kenako “ai,” koma iye akati “inde” amakhalabe “inde.” 20 Pakuti kaya malonjezo a Mulungu akhale oculuka cotani, amakhala “inde” kupitila mwa iye. Cotelo kudzela mwa iye timanena “Ameni” kwa Mulungu kuti Mulungu alandile ulemelelo kudzela mwa ife. 21 Koma Mulungu ndi amene amatitsimikizila kuti inu ndi ife tili a Khristu. Iye ndi amene anatidzoza. 22 Iye watidinda cidindo cake. Cidindo cimeneci ndi mzimu woyela umene uli m’mitima yathu, ndipo cidindico cili ngati cikole ca madalitso a m’tsogolo.
23 Mulungu ndiye mboni yanga kuti cifukwa cimene sindinabwelele ku Korinto mpaka pano, n’cakuti sindinafune kuonjezela cisoni canu. 24 Sikuti ndife olamulila cikhulupililo canu ai, koma ndife anchito anzanu kuti muzisangalala, pakuti ndinu okhazikika cifukwa ca cikhulupililo canu.