Kalata Yaciwiri kwa Akorinto
13 Ulendo uno wobwela kwa inu umene ndakonza ndi wacitatu. “Nkhani iliyonse izitsimikizika ndi umboni wa anthu awili kapena atatu.” 2 Ngakhale kuti sindili kumeneko palipano, zili ngati ndili nanu limodzi kaciwili. Ndipo ndikupelekelatu cenjezo ndisanafike kumeneko kwa amene anacimwa komanso kwa ena onse, kuti ndikadzafikanso kumeneko sindidzawacitila cifundo. 3 Ndikutelo cifukwa mukufuna umboni wakuti Khristu yemwe si wofooka kwa inu, koma ndi wamphamvu, akulankhuladi kudzela mwa ine. 4 Ndithudi iye anaphedwa pamtengo cifukwa ca kufooka, koma ali moyo cifukwa ca mphamvu ya Mulungu. Zoonadi ifenso ndife ofooka limodzi naye, koma tidzakhala naye limodzi cifukwa ca mphamvu ya Mulungu yomwe ikugwila nchito mwa inu.
5 Pitilizani kudziyesa kuti mutsimikize ngati mukali ndi cikhulupililo. Pitilizani kudzisanthula kuti mudziwe kuti ndinu munthu wotani. Kodi simukuzindikila kuti ndinu ogwilizana ndi Yesu Khristu? Muyenela kudziwa zimenezi, pokhapo ngati ndinu osabvomelezeka. 6 Ndikukhulupilila kuti mudzazindikila kuti ndife obvomelezeka.
7 Tsopano tikupemphela kwa Mulungu kuti musacite colakwa ciliconse, osati kuti tioneke ngati obvomelezeka, koma kuti mucite zoyenela ngakhale titaoneka ngati osabvomelezeka. 8 Cifukwa sitingacite ciliconse cotsutsana ndi coonadi, koma zokhazo zogwilizana ndi coonadi. 9 Timasangalala tikakhala ofooka, inu n’kukhala amphamvu. Ndipo pemphelo lathu ndi lakuti mupitilize kupanga masinthidwe oyenelela. 10 N’cifukwa cake ndikulemba zinthu zimenezi ndisanafike kwa inu, kuti ndikadzabwela kumeneko ndisadzagwilitse nchito ulamulilo wanga mwamphamvu, cifukwa Ambuye anandipatsa ulamulilowu kuti ndizikulimbikitsani osati kukufooketsani.
11 Potsiliza abale, pitilizani kukondwela, kusintha maganizo, kulimbikitsidwa, kukhala ogwilizana, ndiponso kukhala mwamtendele. Mwakutelo, Mulungu wacikondi komanso wamtendele, adzakhala nanu. 12 Patsanani moni mwa kupsompsonana kwaubale. 13 Oyela onse akupeleka moni wao.
14 Cisomo ca Ambuye Yesu Khristu, cikondi ca Mulungu, komanso madalitso a mzimu woyela, zikhale ndi inu nonse.