Kalata Yoyamba kwa Akorinto
4 Anthu aziona kuti ndife atumiki a Khristu komanso atumiki a zinsinsi zopatulika za Mulungu. 2 Pa nkhaniyi, cofunika kwa atumiki ndi kukhala okhulupilika. 3 Kwa ine, kuweluzidwa ndi inu kapena khoti iliyonse ya anthu ndi kosafunika kwenikweni. Ndipo ngakhale ine sindidziweluza ndekha. 4 Cikumbumtima canga sicikunditsutsa pa nkhani iliyonse. Koma izi sizitanthauza kuti ndine wolungama, cifukwa amene amandifufuza ndi Yehova. 5 Conco, musamaweluze kalikonse nthawi isanakwane mpaka Ambuye adzabwele. Iye adzacititsa kuti zinsinsi zamumdima zionekele, komanso adzaonetsa poyela zolinga zimene zili mumtima. Ndiyeno Mulungu adzayamikila aliyense payekha.
6 Tsopano abale, ndanena zimenezi zokhudza ineyo ndi Apolo kuti mumvetse mfundo yake n’colinga cakuti muphunzile kwa ife lamulo ili lakuti: “Musapitilile zinthu zolembedwa.” Sitikufuna kuti aliyense wa inu adzikuze n’kumacita zinthu mokondela. 7 Kodi akukupangitsa kukhala wosiyana ndi ena n’ndani? Uli ndi ciani cimene sunacite kulandila? Ndiye ngati unacita kulandila zinthuzo, n’cifukwa ciani ukudzitama ngati kuti siunacite kulandila?
8 Kodi mwakhutila kale? Kodi mwalemela kale? Kodi mwayamba kale kulamulila monga mafumu popanda ife? Ndikanakonda kwambili mukanayamba kulamulila ngati mafumu kuti ifenso tizilamulila nanu limodzi ngati mafumu. 9 Ndikuona monga kuti Mulungu waika atumwife kumapeto pacionetselo monga anthu okaphedwa, cifukwa zili ngati tili m’bwalo lamasewela ndipo tikuonetsedwa ku dziko, kwa angelo, ndiponso kwa anthu. 10 Takhala opusa cifukwa ca Khristu, koma inu mwakhala ocenjela mwa Khristu. Ife ndife ofooka, inu ndinu olimba. Inu mukulemekezedwa, koma ife tikunyozedwa. 11 Mpaka pano tikali anjala, aludzu komanso ausiwa.* Tikumenyedwabe, tikusowabe pokhala, 12 ndipo tikugwilabe nchito molimbika ndi manja athu. Akamatinyoza, timawadalitsa, ndipo akamatizunza timapilila moleza mtima. 13 Akamatineneza zoipa, timayankha mofatsa. Takhala monga zinyalala za dziko, ndiponso zonyansa za zinthu zonse mpaka pano.
14 Ndikulemba zinthu izi, osati kuti ndikucititseni manyazi, koma kuti ndikulangizeni monga ana anga okondedwa. 15 Ngakhale mutakhala ndi anthu 10,000 okuyang’anilani mwa Khristu, mulibe atate ambili. Ine ndine tate wanu mwa Khristu Yesu cifukwa cokubweletselani uthenga wabwino. 16 Conco, ndikukulimbikitsani kuti muzitengela citsanzo canga. 17 Ndiye cifukwa cake ndikukutumizilani Timoteyo, pakuti iye ndi mwana wanga wokondedwa, komanso wokhulupilika mwa Ambuye. Iye adzakukumbutsani mmene ndimacitila* zinthu potumikila Khristu Yesu, monga mmene ndikuphunzitsila kulikonse mumpingo uliwonse.
18 Ena akudzikuza ngati kuti sindidzabwela kwanuko. 19 Yehova akalola, ndibwela posacedwa, ndipo sindidzafuna kumva mau ao odzikuza, koma ndidzafuna ndione mphamvu zao. 20 Pakuti Ufumu wa Mulungu si nkhani ya mau, koma mphamvu. 21 Kodi mungakonde ciani? Ndibwele kwa inu ndi mkwapu, kapena ndibwele ndi cikondi komanso mzimu wofatsa?