LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • my nkhani 25
  • Banja Lonse Lisamukila Ku Iguputo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Banja Lonse Lisamukila Ku Iguputo
  • Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Yehova Sanamuiŵale Yosefe
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Abale Ake Amuzonda Yosefe
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • ‘Tamvelani Maloto Awa’
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Kapolo Amene Anamvela Mulungu
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
Onaninso Zina
Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
my nkhani 25

Nkhani 25

Banja Lonse Lisamukila Ku Iguputo

YOSEFE alephela kupitiliza kudziletsa. Auza anchito ake onse kuti acokemo mu cipinda. Pamene atsala yekha ndi abale ake, Yosefe ayamba kulila. Ganiza cabe mmene abale ake anadabwila! Sanadziŵe cimene anali kulilila. Koma potsilizila pake awauza kuti: ‘Ine ndine Yosefe, kodi atate anga akali moyo?’

Abale ake adabwa kwambili cakuti alephela kukamba. Iwo ali ndi mantha. Koma Yosefe akuti: ‘Fendelani pafupi ndi ine.’ Pamene afendela, awauza kuti: ‘Ndine m’bale wanu Yosefe, uja amene munagulitsa ku Iguputo.’

Yosefe apitiliza kukamba nao mwacifundo kuti: ‘Musadzipatse mlandu kuti munanigulitsa kuno. Mulungu ndiye ananditumiza ku Iguputo kuno kuti ndidzapulumutse miyoyo ya anthu. Farao wandiika kukhala wolamulila wa dziko lonse. Conco bwelelani mwamsanga kwa atate, mukawauze zimene ndakuuzani. Mukawauze kuti akabwele kuti azikhala kuno.’

Ndiyeno Yosefe awakumbatila abale ake onse ndi kuwapsompsona. Pamene Farao amvela kuti abale a Yosefe abwela, auza Yosefe kuti: ‘Uwauze abale ako kuti atenge ngolo ndipo akatenge atate ao ndi mabanja ao kuti abwele nao kuno. Nidzakupatsani malo abwino koposa mu dziko lonse la Iguputo.’

Iwo anacitadi zimenezo. Amene uona pacithunzi-thunzi apa ni Yosefe akumana ndi atate ake pamene anabwela ku Iguputo ndi banja lao lonse.

Banja la Yakobo linakula kwambili. Pamene Yakobo, ana ake ndi adzukulu ake anasamukila ku Iguputo, onse pamodzi anali 70. Koma panalinso azikazi ao, ndipo mwina panalinso anchito ao ambili. Anthu onsewa anakhala mu dziko la Iguputo. Iwo anali kuchedwa kuti Aisiraeli, cifukwa Mulungu anasintha dzina lakuti Yakobo kukhala Isiraeli. Aisiraeli anakhala anthu apadela kwa Mulungu, monga mmene tidzaonela mu nkhani zina.

Genesis 45:1-28; 46:1-27.

Mafunso Ophunzilila

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani