LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • my nkhani 37
  • Tenti Yolambililako

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Tenti Yolambililako
  • Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Cihema Colambililako
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Ciitano Capadela ca Yehova Cokhala Alendo Ake
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
my nkhani 37

Nkhani 37

Tenti Yolambililako

KODI ici cioneka pacithunzi-thunzi apa ucidziŵa? Ni tenti yapadela yolambililako Yehova. Dzina lina la tenti imeneyi ni cihema. Anthu anatsiliza kumanga tenti iyi patapita caka cimodzi kucokela pamene anacoka ku Iguputo. Kodi umudziŵa amene anawauza kuti aimange?

Ni Yehova. Pamene Mose anali mu phili la Sinai, Yehova anamuuza moimangila. Anamuuza kuti apange tenti imeneyi m’njila yosavuta kumasula. Conco, cinali cotheka kunyamula mbali zosiyana-siyana za tenti imeneyi ndi kukamanganso pamalo ena. N’zimene Aisiraeli anali kucita posamuka-samuka mu cipululu.

Ukayang’ana mkati mwa cipinda cing’ono kumbali ya kumapeto kwa tenti, uona kuti muli bokosi. Imeneyi ni likasa la cipangano. Pamwamba pa likasa limeneli panali angelo kapena akelubi aŵili agolide. Wina uku, wina uku. Mulungu analembanso Malamulo Khumi pamiyala ina yafulati, cifukwa Mose anaphwanya miyala yoyamba. Ndipo miyala imeneyi anaiika mkati mwa likasa la cipangano. Anaikamonso mtsuko, kapena kuti jagi, ya mana. Kodi ukumbukila kuti mana n’ciani?

Aroni mkulu wa Mose, ni amene Yehova wasankha kukhala mkulu wa ansembe. Iye ni amene anatsogolela anthu pa kulambila Yehova. Ana ake nao ni ansembe.

Waciona cipinda cacikulu ico? Saizi yake ni yaikulu cakuti cipinda cacing’onoco ciloŵamo kaŵili. Kodi waiona bokosi ing’ono imene icotsa utsi? imeneyi ndi guwa lansembe imene ansembe amatenthelapo zinthu zonunkhila. Ndiyeno muli coikapo nyale cimene cili ndi nyale 7. Cacitatu cimene cili mmenemu ni thebulo. Pathebulo imeneyi amaikapo mitanda 12 ya mkate.

Cihema cili ndi yadi, kapena kuti bwalo. Ndipo mu yadi yake muli beseni ikulu yodzala madzi. Ansembe ndi amene amasambamo. Komanso mu yadi muli guwa lansembe lalikulu. Paguwa limeneli amatenthelapo nyama zopelekela nsembe kwa Yehova. Tenti yolambilila imeneyi ili pakati pa msasa, ndipo Aisiraeli amakhala mu matenti ao mozungulila tenti imeneyi.

Ekisodo 25:8-40; 26:1-37; 27:1-8; 28:1; 30:1-10, 17-21; 34:1, 2; Aheberi 9:1-5.

Mafunso Ophunzilila

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani