LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • jl phunzilo 15
  • Kodi Akulu Amatumikila Mpingo m’Njila Ziti?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Akulu Amatumikila Mpingo m’Njila Ziti?
  • Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
  • Nkhani Zofanana
  • Dongosolo la Mpingo
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Abusa, Tsanzilani Abusa Aakulu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • Inu Akulu—Pitilizani Kutsanzila Mtumwi Paulo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
jl phunzilo 15

PHUNZILO 15

Kodi Akulu Amatumikila Mpingo m’Njila Ziti?

Mkulu akambitsana ndi anthu a mu mpingo

Ku Finland

Mkulu aphunzitsa mu mpingo

Kuphunzitsa

Akulu akulimbikitsa anthu a mu mpingo

Ubusa

Mkulu ali mu ulaliki

Kulalikila

M’gulu lathu tilibe abusa amene amalipilidwa. Koma tili ndi oyang’anila oyenelela amene amaikidwa ‘kuti aŵete mpingo wa Mulungu.’ Umu ndi mmene zinalili pamene mpingo wacikristu unayamba. (Macitidwe 20:28) Akulu amenewa ni amuna ofikapo mwauzimu ndipo amatsogolela mpingo ndi kuuŵeta, “osati mokakamizika, koma mofunitsitsa. Osatinso cifukwa cofuna kupindulapo kenakake, koma ndi mtima wonse.” (1 Petulo 5:1-3) Kodi amatithandiza m’njila ziti?

Amatisamalila ndi kutiyang’anila. Akulu amatsogolela mpingo ndipo amauteteza mwauzimu. Pozindikila kuti Mulungu wawapatsa udindo waukulu umenewu, akulu sapondeleza anthu ake, koma amawathandiza kuti akhale olimba ndi acimwemwe. (2 Akorinto 1:24) Mbusa amacita khama kusamalila nkhosa imodzi ndi imodzi. Akulu naonso amayesetsa kudziŵa bwino munthu aliyense mumpingo.—Miyambo 27:23.

Amatiphunzitsa kucita cifunilo ca Mulungu. Wiki iliyonse, akulu amacititsa misonkhano ya mpingo kuti alimbitse cikhuluplilo cathu. (Machitidwe 15:32) Ndiponso amuna odzipeleka amenewa amatsogolela pa nchito yolalikila. Iwo amagwila nafe nchito imeneyi ndi kutiphunzitsa mbali zonse za ulaliki.

Amalimbikitsa aliyense wa ife payekha-payekha. Pofuna kusamalila zosoŵa zauzimu za aliyense wa ife, akulu angatiyendele kunyumba kwathu kapena angaceze nafe pa Nyumba ya Ufumu. Pa nthawi imeneyi, io amagwilitsila nchito Malemba kupeleka thandizo ndi citonthozo.—Yakobo 5:14, 15.

Kuonjezela pa nchito yao mumpingo, akulu ambili amaseŵenza, ndipo alinso ndi udindo wosamalila mabanja ao. Zonsezi zimafuna nthawi. Abale ogwila nchito mwakhama amenewa, afunika kuwalemekeza.—1 Atesalonika 5:12, 13.

  • Kodi akulu mumpingo ali ndi udindo wanji?

  • Kodi akulu amaonetsa bwanji kuti ali ndi cidwi ndi aliyense wa ife?

DZIŴANI ZAMBILI

Kodi ni munthu wotani amene angatumikile pa udindo? Ŵelengani ziyeneletso za m’Malemba za akulu ndi atumiki othandiza pa 1 Timoteyo 3:1-10, 12 ndi Tito 1:5-9.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani