MAFUNSO KWA OFUNSILA UBATIZO
Gawo 2: Umoyo Wacikhristu
Pa kuphunzila kwanu Baibo, mwadziŵa zimene Yehova amafuna kuti muzicita, na mmene mungamatsatilile miyezo yake yolungama. Cifukwa ca zimene mwaphunzila, muyenela kuti munasintha kale zinthu zambili mu umoyo wanu, komanso mmene mumaonela moyo. Popeza kuti munatsimikiza mtima kuti muziyendela miyezo ya Yehova yolungama, ndimwe woyenelela kukhala mtumiki wa uthenga wabwino.
Kukambilana mafunso otsatilawa kudzakuthandizani kukumbukila bwino miyezo ya Yehova yolungama, ndipo kudzakukumbutsani zimene mungacite kuti mukhale mtumiki wake wovomelezeka. Mudzaonanso kufunika kocita zinthu zonse na cikumbumtima cabwino polemekeza Yehova.—2 Akor. 1:12; 1 Tim. 1:19; 1 Pet. 3:16, 21.
Pamene mwafika apa lomba m’kuphunzila kwanu, mosakayikila ndimwe wofunitsitsa kugonjela ulamulilo wa Yehova, na kukhala m’gulu lake. Mafunso otsatilawa pamodzi na Malemba ake, adzakuthandizani kuona mmene mumagonjelela makonzedwe a Yehova, kaya ni mumpingo, m’banja, kapena kwa olamulila andale adziko. Ndithudi, mudzayamikila kwambili makonzedwe a Yehova ophunzitsa anthu ake na kuwalimbikitsa mwauzimu. Makonzedwe amenewa akuphatikizapo misonkhano ya mpingo imene mumapezekapo na kutengapo mbali.
Kuwonjezela apo, gawo limeneli lidzaonetsanso kufunika kotengako mbali nthawi zonse m’nchito yolalikila za Ufumu, kuthandiza anthu kuti adziŵe Yehova na zimene akucitila mtundu wa anthu. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Comalizila, mudzamvetsa bwino kufunika kwa kudzipatulila kwanu kwa Yehova Mulungu na ubatizo wanu. Dziŵani ndithu kuti Yehova ni wokondwa kwambili na mmene mwalabadilila cisomo cimene wakuonetsani.
1. Kodi Yehova amavomeleza cikwati cotani? Kodi pali maziko okha ati olola anthu kusudzulana mwa Malemba?
• “Kodi simunawelenge kuti amene analenga anthu pa ciyambi pomwe anawalenga mwamuna ndi mkazi n’kunena kuti, ‘Pa cifukwa cimeneci mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo awiliwo adzakhala thupi limodzi’? Cotelo salinso awili, koma thupi limodzi. Conco cimene Mulungu wacimanga pamodzi, munthu asacilekanitse. . . . Aliyense wosiya mkazi wake n’kukwatila wina wacita cigololo, kupatulapo ngati wamusiya cifukwa ca dama.”—Mat. 19:4-6, 9.
2. N’cifukwa ciani mwamuna na mkazi amene akukhala pamodzi afunika kukhala okwatilana mwalamulo? Ngati muli pa cikwati, kodi cikwati canu cilidi covomelezeka mwalamulo?
• “Pitiliza kuwakumbutsa kuti azigonjela ndi kumvela maboma ndiponso olamulila.”—Tito 3:1.
• “Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse, ndipo pogona pa anthu okwatilana pakhale posaipitsidwa, pakuti Mulungu adzaweluza adama ndi acigololo.”—Aheb. 13:4.
3. Kodi mbali yanu m’banja ni iti?
• “Mwana wanga, tamvela malangizo a bambo ako, ndipo usasiye malamulo a mayi ako.”—Miy. 1:8.
• “Mwamuna ndiye mutu wa mkazi wake monganso mmene Khristu alili mutu wa mpingo, . . . Amuna inu, pitilizani kukonda akazi anu monga mmene Khristu anakondela mpingo.”—Aef. 5:23, 25.
•“Abambo, musamapsetse mtima ana anu, koma muwalele m’malangizo a Yehova kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.”—Aef. 6:4.
• “Ananu, muzimvela makolo anu pa zinthu zonse, pakuti kucita zimenezi kumakondweletsa Ambuye.”—Akol. 3:20.
• “Inu akazi, muzigonjela amuna anu.”—1 Pet. 3:1.
4. N’cifukwa ciani tiyenela kulemekeza moyo?
• “Ndi iyeyo [Mulungu] amene amapatsa anthu onse moyo, mpweya, ndi zinthu zonse. . . . Cifukwa ca iye tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo.”—Mac. 17:25, 28.
5. N’cifukwa ciani kupha munthu aliyense ni chimo, ngakhale mwana ali m’mimba?
• “Amuna akamamenyana ndipo avulaza kwambili mkazi wapakati moti . . . wina wamwalila, pamenepo uzipeleka moyo kulipila moyo.”—Eks. 21:22, 23.
• “Maso anu anandiona pamene ndinali mluza, ndipo ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku lanu. M’bukumo munalembamo za masiku amene zinapangidwa koma panalibe ngakhale ciwalo cimodzi cimene cinali citapangidwa.”—Sal. 139:16.
• “Yehova amadana [ndi] . . . manja okhetsa magazi a anthu osalakwa.”—Miy. 6:16, 17.
6. Kodi lamulo la Mulungu limati ciani pa nkhani ya magazi?
• ‘Pitilizani kupewa . . . magazi [ndi] zopotola.’—Mac. 15:29.
7. N’cifukwa ciani tiyenela kuwakonda abale na alongo athu acikhristu?
• “Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mmene ine ndakukondelani, inunso muzikondana. Mwakutelo, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzila anga, ngati mukukondana.”—Yoh. 13:34, 35.
8. Pofuna kupewa kupatsila ena matenda, amene angakhale akupha: (a) N’cifukwa ciani munthu wodwala sayenela kuonetsa cikondi mwa kukumbatila anthu ena? (b) Ndipo n’cifukwa ciani sayenela kukhumudwa ngati ena samuitanila kunyumba kwawo? (c) Ngati munthu analiko paciwopsezo cotenga matenda oyambukila, n’cifukwa ciani pa iye yekha afunika kukapimitsa magazi asanayambe cibwenzi? (d) Ngati munthu ali na matenda oyambukila pamene akukonzekela ubatizo, n’cifukwa ciani ayenela kudziŵitsa mgwilizanitsi wa bungwe la akulu za matendawo asanabatizike?
• “Musamakhale ndi ngongole iliyonse kwa munthu aliyense, . . . ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.’ Cikondi sicilimbikitsa munthu kucitila zoipa mnzake.”—Aroma 13:8-10.
• “Musamaganizile zofuna zanu zokha, koma muziganizilanso zofuna za ena.”—Afil. 2:4.
9. N’cifukwa ciani Yehova amafuna kuti tizikhululukila ena?
• “Pitilizani kulolelana ndi kukhululukilana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi cifukwa codandaulila za mnzake. Monga Yehova anakukhululukilani ndi mtima wonse, inunso teloni.”—Akol. 3:13.
10. Kodi muyenela kucita ciani ngati m’bale kapena mlongo wakukambilani misece, kapena kukubelani mokugwilani m’maso, kapena kuti mwaukathyali?
• “Ngati m’bale wako wacimwa, upite kukam’fotokozela colakwaco panokha iwe ndi iyeyo. Ngati wakumvela, ndiye kuti wabweza m’bale wakoyo. Koma akapanda kukumvela, upiteko ndi munthu wina mmodzi kapena awili, kuti nkhani yonse ikatsimikizike ndi pakamwa pa mboni ziwili kapena zitatu. Akapanda kuwamvela amenewanso, uuze mpingo. Ndipo akapandanso kumvela mpingowo, kwa iwe akhale ngati munthu wocokela mu mtundu wina komanso ngati wokhometsa msonkho.”—Mat. 18:15-17.
11. Kodi Yehova amawaona bwanji macimo awa?
▪ Ciwelewele
▪ Kuseŵenzetsa zifanizo polambila
▪ Mathanyula
▪ Kuba
▪ Njuga
▪ Kuledzela
• “Kodi zoonadi inu simukudziwa kuti anthu osalungama sadzalowa mu ufumu wa Mulungu? Musasoceletsedwe. Adama, opembedza mafano, acigololo, amuna amene amagonedwa ndi amuna anzawo, amuna ogona amuna anzawo, akuba, aumbombo, zidakwa, olalata, kapena olanda, onsewo sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.”—1 Akor. 6:9, 10.
12. Pa nkhani ya ciwelewele, comwe cimaphatikizapo cigololo na macitidwe alionse akugonana kunja kwa cikwati, kodi ndimwe wokonzeka kucita ciani?
• “Thaŵani dama.”—1 Akor. 6:18.
13. N’cifukwa ciani tiyenela kupewa fodya kapena amkolabongo a mtundu uliwonse?
• “Mupeleke matupi anu ngati nsembe yamoyo, yoyela ndi yovomelezeka kwa Mulungu, ndiyo utumiki wopatulika mwa kugwilitsa nchito luntha la kuganiza. Musamatengele nzelu za nthawi ino, koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu, kuti muzindikile cimene cili cifunilo ca Mulungu, cabwino, covomelezeka ndi cangwilo.”—Aroma 12:1, 2.
14. Kodi ni macita-cita ati auciwanda amene Mulungu amaletsa?
• “Pakati panu pasapezeke munthu wotentha mwana wake pamoto, wolosela, wocita zamatsenga, woombeza, wanyanga, kapena wolodza ena, aliyense wofunsila kwa wolankhula ndi mizimu, wolosela zam’tsogolo kapena aliyense wofunsila kwa akufa.”—Deut. 18:10, 11.
15. Ngati munthu wacita chimo lalikulu koma afuna kubwelela kwa Yehova, kodi ayenela kucita ciani mwamsanga?
• “Ndinaulula chimo langa kwa inu, ndipo sindinabise colakwa canga. Ndinati: ‘Ndidzaulula kwa Yehova macimo anga.’”—Sal. 32:5.
•“Kodi pali wina amene akudwala pakati panu? Aitane akulu a mpingo, ndipo iwo amupemphelele ndi kumupaka mafuta m’dzina la Yehova. Pemphelo la cikhulupililo lidzacilitsa wodwalayo, ndipo Yehova adzamulimbitsa. Ndiponso ngati anacita macimo, adzakhululukidwa.”—Yak. 5:14, 15.
16. Mukadziŵa kuti Mkhristu mnzanu anacita chimo lalikulu, kodi muyenela kucita ciani?
• “Munthu akaona wina akucita chimo, kapena wamva kuti wina wacita chimo, munthu ameneyo ndi mboni. Akamva cilengezo kuti akacitile umboni za wocimwayo koma iye osapita kukanena, ndiye kuti wacimwa. Ayenela kuyankha mlandu wa colakwa cakeco.”—Lev. 5:1.
17. Cilengezo cikapelekedwa cakuti uje salinso Mboni ya Yehova, kodi tiyenela kucita naye motani?
• “Muleke kuyanjana ndi aliyense wochedwa m’bale, amene ndi wadama, kapena waumbombo, kapena wopembedza mafano, wolalata, cidakwa, kapena wolanda, ngakhale kudya naye munthu woteleyu ayi.”—1 Akor. 5:11.
• “Wina akabwela kwa inu ndi ciphunzitso cosiyana ndi ici, musamulandile m’nyumba zanu kapena kumupatsa moni.”—2 Yoh. 10.
18. N’cifukwa ciani mabwenzi anu abwino ayenela kukhala aja okonda Yehova?
• “Munthu woyenda ndi anthu anzelu adzakhala wanzelu, koma wocita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.”—Miy. 13:20.
•“Musasoceletsedwe. Kugwilizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.”—1 Akor. 15:33.
19. N’cifukwa ciani a Mboni za Yehova satengako mbali m’zandale?
• “Iwo sali mbali ya dziko, monganso ine [Yesu] sindili mbali ya dziko.”—Yoh. 17:16.
20. N’cifukwa ciani muyenela kumvela boma?
• “Munthu aliyense azimvela olamulila akuluakulu, cifukwa palibe ulamulilo umene ungakhalepo kupatulapo ngati Mulungu waulola. Olamulila amene alipowa ali m’malo awo osiyanasiyana mololedwa ndi Mulungu.”—Aroma 13:1.
21. Ngati lamulo la anthu lawombana na lamulo la Mulungu, kodi mungacite ciani?
• “Tiyenela kumvela Mulungu monga wolamulila, osati anthu.”—Mac. 5:29.
22. Posankha nchito, ni malemba ati angakuthandizeni kukhalabe wolekana nalo dziko?
• “Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake, ndipo anthuwo sadzaphunzilanso nkhondo.”—Mika 4:3.
• “Tulukani mwa iye [Babulo Wamkulu] anthu anga, ngati simukufuna kugawana naye macimo ake, ndiponso ngati simukufuna kulandila nawo ina ya milili yake.”—Chiv. 18:4.
23. Kodi muyenela kusankha zosangalatsa na zosangulutsa za mtundu wanji? Ndipo muyenela kupewa za mtundu uti?
•“Yehova . . . amadana kwambili ndi aliyense wokonda ciwawa.”—Sal. 11:5.
• “Nyansidwani ndi coipa, gwilitsitsani cabwino.”—Aroma 12:9.
• “Zinthu zilizonse zoona, zilizonse zofunika kwambili, zilizonse zolungama, zilizonse zoyela, zilizonse zacikondi, zilizonse zoyamikilika, khalidwe labwino lililonse, ndi ciliconse cotamandika, pitilizani kuganizila zimenezi.”—Afil. 4:8.
24. N’cifukwa ciani a Mboni za Yehova salambilako pamodzi na zipembedzo zina?
• “Sizingatheke kuti muzidya ‘patebulo la Yehova’ komanso patebulo la ziwanda.”—1 Akor. 10:21.
• “‘Tulukani pakati pawo, lekanani nawo,’ watelo Yehova. ‘Musakhudze cinthu codetsedwa,’ ‘ndipo ndidzakulandilani.’”—2 Akor. 6:17.
25. Pa nkhani ya zikondwelelo, ni mfundo ziti zingakuthandizeni kuona ngati muyenela kutengako mbali kapena ayi?
• “Iwo anayamba kusakanikilana ndi mitundu ina, ndi kuyamba kuphunzila zocita zawo. Anayamba kutumikila mafano awo, ndipo mafanowo anakhala msampha wawo.”—Sal. 106:35, 36.
• “Akufa sadziwa ciliconse.”—Mlal. 9:5.
• “Iwo sali mbali ya dziko, monganso ine sindili mbali ya dziko.”—Yoh. 17:16.
• “Pakuti nthawi imene yapitayi inali yokwanila kwa inu kucita cifunilo ca anthu a m’dzikoli pamene munali kucita zinthu zosonyeza khalidwe lotayilila, zilakolako zoipa, kumwa vinyo mopitilila muyezo, maphwando aphokoso, kumwa kwa mpikisano, ndi kupembedza mafano kosaloleka.”—1 Pet. 4:3.
26. Kodi zitsanzo za m’Baibo zimakuthandizani bwanji pa nkhani yokondwelela tsiku la kubadwa?
• “Tsiku lacitatulo linafika, ndipo linali tsiku lokumbukila kubadwa kwa Farao. Mfumuyo inakonzela phwando anchito ake onse. Pa tsikuli, Farao anatulutsa m’ndende mkulu wa opelekela cikho ndi mkulu wa ophika mkate, n’kuwaimika pamaso pa anchito ake onse. Farao anabwezeladi pa nchito mkulu wa opelekela cikho uja, . . . Koma mkulu wa ophika mkate anam’pacika.”—Gen. 40:20-22.
• “Tsiku lokumbukila kubadwa kwa Herode litafika, mwana wamkazi wa Herodiya anavina pa tsikulo ndipo anasangalatsa Herode kwambili, mwakuti analonjeza molumbila kuti adzapatsa mtsikanayo ciliconse cimene angapemphe. Tsopano mtsikanayu, mayi wake atacita kum’pangila, anapempha kuti: ‘Ndipatseni mutu wa Yohane M’batizi m’mbale pompano.’ Conco anatuma munthu kukadula mutu wa Yohane m’ndende.”—Mat. 14:6-8, 10.
27. N’cifukwa ciani muyenela kumvela malangizo a akulu?
• “Muzimvela amene akutsogolela pakati panu ndipo muziwagonjela. Iwo amayang’anila miyoyo yanu monga anthu amene adzayankhe mlandu. Muziwamvela ndi kuwagonjela kuti agwile nchito yawo mwacimwemwe, osati modandaula, pakuti akatelo zingakhale zokuvulazani.”—Aheb. 13:17.
28. N’cifukwa ciani n’kofunika kwambili kuti imwe, komanso banja lanu, muzipatula nthawi yoŵelenga Baibo na kuiphunzila nthawi zonse?
• “Amakondwela ndi cilamulo ca Yehova, ndipo amawelenga ndi kusinkhasinkha cilamulo cake usana ndi usiku. Munthu ameneyo adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m’mphepete mwa mitsinje ya madzi, umene umabala zipatso m’nyengo yake, umenenso masamba ake safota, ndipo zocita zake zonse zidzamuyendela bwino.”—Sal. 1:2, 3.
29. N’cifukwa ciani mumakonda kupezeka ku misonkhano na kutengako mbali?
• “Ndidzalengeza dzina lanu kwa abale anga. Ndidzakutamandani pakati pa mpingo.”—Sal. 22:22.
• “Tiyeni tiganizilane kuti tilimbikitsane pa cikondi ndi nchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi, monga mmene ena acizolowezi cosafika pamisonkhano akucitila. Koma tiyeni tilimbikitsane, ndipo tiwonjezele kucita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikila.”—Aheb. 10:24, 25.
30. Kodi nchito yofunika kopambana imene Yesu anatipatsa kuti tiigwile ni nchito yanji?
• “Conco pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila anga. Muziwabatiza . . . , ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulilani.”—Mat. 28:19, 20.
31. Pocita zopeleka ku nchito ya Ufumu, kapena pothandiza abale na alongo athu, kodi Yehova amakondwela ngati ticita zimenezi na mtima wotani?
•“Uzilemekeza Yehova ndi zinthu zako zamtengo wapatali.”—Miy. 3:9.
• “Aliyense acite mogwilizana ndi mmene watsimikizila mumtima mwake, osati monyinyilika kapena mokakamizika, cifukwa Mulungu amakonda munthu wopeleka mokondwela.”—2 Akor. 9:7.
32. Kodi ni mavuto otani amene Akhristu amayembekezela kukumana nawo?
• “Odala ndi anthu amene akuzunzidwa cifukwa ca cilungamo, pakuti Ufumu wakumwamba ndi wawo. ‘Ndinu odala pamene anthu akukunyozani ndi kukuzunzani, komanso kukunamizilani zoipa zilizonse cifukwa ca ine. Kondwelani, dumphani ndi cimwemwe, cifukwa mphoto yanu ndi yaikulu kumwamba, pakuti umu ndi mmenenso anazunzila aneneli amene analipo inu musanakhaleko.”—Mat. 5:10-12.
33. N’cifukwa ciani ni mwayi wapadela kubatizika n’kukhala Mboni ya Yehova?
• “Mawu anu amandikondweletsa ndi kusangalatsa mtima wanga, pakuti ine ndimachedwa ndi dzina lanu, inu Yehova Mulungu.”—Yer. 15:16.