LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 19 tsa. 50-tsa. 51 pala. 2
  • Milili Itatu Yoyambilila

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Milili Itatu Yoyambilila
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Mose Ndi Aroni Aonana Ndi Farao
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Milili 6 Yokonkhapo
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Mose Anasankha Kulambila Yehova
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Milili 10
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
Onaninso Zina
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 19 tsa. 50-tsa. 51 pala. 2
Mose na Aroni aimilila pamaso pa Farao

PHUNZILO 19

Milili Itatu Yoyambilila

Aiguputo anali kukakamiza Aisiraeli kugwila nchito ya kalavula gaga monga akapolo. Yehova anatuma Mose na Aroni kwa Farao kukamuuza kuti: ‘Lola anthu anga apite kuti akanilambile m’cipululu.’ Koma Farao anayankha mwamwano kuti: ‘Za Yehova nilibe nazo nchito. Ndipo sinidzalola Aisiraeli kucoka.’ Pamenepo Farao anawawonjezela nchito ya kalavula gaga. Apa lomba Yehova anafuna kumulanga Farao. Udziŵa zimene anacita? Anabweletsa Milili 10 m’dziko la Iguputo. Yehova anauza Mose kuti: ‘Farao sakunimvela. Mailo kuseni, adzakhala ku Mtsinje wa Nailo. Ukapite kumeneko, ukamuuze kuti madzi onse mu Mtsinje wa Nailo adzasanduka magazi, cifukwa wakana kulola anthu anga kupita.’ Mose anapitadi kwa Farao. Ndipo Farao anaona pamene Aroni anamenya ndodo yake pa Mtsinje wa Nailo, ndipo madzi onse anasanduka magazi. Mtsinje umenewo unayamba kununkha, nsomba zinafa, ndipo kunalibe madzi abwino akumwa. Koma Farao anakanabe kulola Aisiraeli kupita.

Patapita masiku 7, Yehova anatumanso Mose kwa Farao kukamuuza kuti: ‘Ngati sudzalola anthu anga kupita, m’dziko lonse la Iguputo mudzakhala acule paliponse.’ Aroni anatambasula ndodo yake, ndipo acule anali paliponse. Anthu anali kupeza acule m’nyumba, pa mabedi, olo m’mbale zawo. Farao anapempha Mose kuti apapatile Yehova kuti acotse aculewo. Ndipo Farao analonjeza kuti adzalola Aisiraeli kupita. Pamenepo Yehova analetsa mlili umenewo, ndipo Aiguputo anaunjika acule mahopo-mahopo. Dziko lonse linayamba kununkha. Koma Farao anasinthanso maganizo, sanalole Aisiraeli kupita.

Lomba Yehova anauza Mose kuti: ‘Uza Aroni kuti amenyetse ndodo yake pansi, ndipo fumbi lidzasanduka tudoyo toluma.’ Ataimenyetsa pansi, fumbilo linasanduka tudoyo twambili ndipo tunakhala paliponse. Anthu ena a Farao anamuuza kuti: ‘Mlili umenewu wacokela kwa Mulungu.’ Ngakhale n’conco, Farao analetsa kuti Aisiraeli apite.

Milili itatu pa milili 10 ya Iguputo: magazi mu Mtsinje wa Nailo, acule, na tudoyo toluma

“Ndiwaonetsa dzanja langa ndi mphamvu zanga, ndipo adziŵa kuti dzina langa ndine Yehova.”—Yeremiya 16:21

Mafunso: Kodi milili itatu yoyambilila inali iti? N’cifukwa ciani Yehova anabweletsa milili imeneyo?

Eksodo 5:1-18; 7:8–8:19; Nehemiya 9:9, 10

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani