PHUNZILO 22
Cozizwitsa pa Nyanja Yofiila
Pamene Farao anamvela kuti Aisiraeli acoka mu Iguputo, anasinthanso maganizo ake. Analamula asilikali ake kuti: ‘Konzekeletsani magaleta onse ankhondo, tiyeni tiŵakonke! Tisaŵalole kupita.’ Pamenepo iye na asilikali ake ananyamuka kuthamangila Aisiraeli.
Yehova anali kutsogolela anthu ake na mtambo masana, komanso moto usiku. Anawatsogolela ku Nyanja Yofiila, na kuwauza kuti amange msasa pamenepo.
Pambuyo pake, Aisiraeli anagoona kuti Farao watulukila na asilikali ake, akuwathamangila. Iwo anasoŵa koloŵela. Kutsogolo kunali nyanja, kumbuyo kunali asilikali a Farao. Pamenepo Aisiraeli anafuulila Mose kuti: ‘Tidzafa ise! Munaticotselanji ku Iguputo kutibweletsa kuno.’ Koma Mose anati: ‘Musacite mantha. Yembekezani muone mmene Yehova adzatipulumutsila.’ Mose anadaliladi Yehova, si conco?
Yehova anauza Aisiraeli kupasula msasa. Usikuwo, Yehova anacotsa mtambo kutsogolo na kuuika pakati pa Aiguputo na Aisiraeli. Kumbali ya Aiguputo kunali mdima, koma kumbali ya Aisiraeli kunali kowala.
Ndiyeno Yehova anauza Mose kutambasulila dzanja lake ku nyanja. Pamenepo Yehova anacititsa mphepo yamphamvu kuwomba usiku wonse. Nyanjayo inagaŵika pakati, cakuti madzi anapanga monga cipupa, cina uku cina uku, pakati panapangika njila. Aisiraeli mamiliyoni anayenda pa nthaka youma, mpaka kuwolokela ku tsidya lina.
Asilikali a Farao poona conco, nawonso analoŵa pa njila imene inapangika panyanjapo kuti alondole Aisiraeli. Koma Yehova anapangitsa asilikaliwo kusokonezeka. Mawilo a magaleta awo anayamba kuguluka. Ndipo anafuula kuti: ‘Tiyeni tithaŵemo muno! Yehova akuwamenyela nkhondo.’
Koma Yehova anauza Mose kuti: ‘Tambasulila dzanja lako ku nyanja.’ Pamenepo vimadzi vinakhuthukila asilikali aciiguputo. Farao na asilikali ake onse anafela pamenepo. Sipanapulumuke olo mmodzi.
Ku tsidya lina la nyanja, khamu la Aisiraeli linali kutamanda Mulungu pomuimbila nyimbo yakuti: “Ndiimbila Yehova, pakuti iye wakwezeka koposa. Waponyela m’nyanja mahachi ndi okwela pamahachiwo.” Pamene iwo anali kuimba conco, azimayi anali kuvina na kuliza masece. Aliyense anali wosangalala ngako cifukwa anamasukadi.
“Moti tikhale olimba mtima ndithu ndipo tinene kuti: ‘Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa. Munthu angandicite ciani?’”—Aheberi 13:6