LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 51 tsa. 124-tsa. 125 pala. 2
  • Kamtsikana Kathandiza Mkulu wa Asilikali

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kamtsikana Kathandiza Mkulu wa Asilikali
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Kamtsikana Kathandiza Munthu Wamphamvu Kwambili
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 51 tsa. 124-tsa. 125 pala. 2
Namani wapita kwa Elisa kuti akam’cilitse

PHUNZILO 51

Kamtsikana Kathandiza Mkulu wa Asilikali

Ku Siriya kunali kamtsikana kaciisiraeli kamene kanatengedwa kukakhala kutali na kwawo. Kanatengedwa na asilikali acisiriya kuti kaziseŵenzela mkazi wa mkulu wa asilikali, dzina lake Namani. Kamtsikanaka kanali kulambila Yehova, olo kuti onse kumeneko sanali kulambila Yehova.

Namani anali kudwala matenda oipa akhate, ndipo anali kumvela kuŵaŵa kwambili. Kamtsikanako kanafuna kwambili kum’thandiza. Conco kanauza mkazi wa Namani kuti: ‘Nidziŵa amene angaŵacilitse amuna anu. Ku Isiraeli kuli mneneli wa Yehova dzina lake Elisa. Angaŵacilitse amuna anu.’

Mkazi wa Namani anauza mwamuna wake zimene kamtsikanako kanamuuza. Namani anali wokonzeka kucita ciliconse kuti acile. Conco, anapita ku Isiraeli ku nyumba ya Elisa. Koma iye anaganiza kuti Elisa adzamulandila mwapadela monga munthu wolemekezeka. Koma m’malo mokamba naye mwacindunji, Elisa anangouza mtumiki wake kuti apite akaonane na Namani, na kumuuza kuti: ‘Pita ukasambe maulendo 7 mu Mtsinje wa Yorodano, ndipo udzacila.’

Koma Namani anakwiya kwambili. Anati: ‘Ni nali kuganiza kuti mneneliyo adzanicilitsa mwapadela, mwa kuitanila kwa Mulungu wake poniika manja. Koma akuniuza kuti nikasambe mu mtsinje wa kuno ku Isiraeli. Tili na mitsinje yabwino ku Siriya kuposa twanu. Bwanji osangoniuza kuti nikasambe mu mtsinje wakwathu?’ Namani anakwiya kwambili, cakuti anacoka pa nyumba ya Elisa.

Namani akudziyeletsa mu Mtsinje wa Yorodano, ndipo acila

Koma atumiki a Namani anam’thandiza kuti aganizepo bwino. Iwo anati: ‘Kodi simungacite ciliconse kuti mucile? Zimene mneneliyu wakuuzani kucita si zovuta. Bwanji osangocita zimene wakamba?’ Namani anamvela. Conco, anapita ku Mtsinje wa Yorodano na kumila m’madzi maulendo 7. Pamene anavuuka ka namba 7, anapolelatu! Namani anakondwela kwambili, cakuti anapitanso kwa Elisa kuti akawonge zikomo. Iye anati: ‘Lomba nadziŵa kuti Yehova ndiye Mulungu woona.’ Uganiza kuti kamtsikana kaciisiraeli kanamvela bwanji, pamene kanaona kuti Namani wabwelako atacila?

“M’kamwa mwa ana ndi mwa ana oyamwa mwaikamo mawu otamanda.”—Mateyu 21:16

Mafunso: Kodi uganiza cinali copepuka kwa kamtsikana kaciisiraeli kukamba na mkazi wa Namani? Uganiza n’ciani cinakathandiza kulimba mtima?

2 Mafumu 5:1-19; Luka 4:27

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani