PHUNZILO 77
Mzimayi Akumana na Yesu pa Citsime
Cikondwelelo ca Pasika citapita, Yesu na ophunzila ake ananyamuka ulendo wobwelela ku Galileya, kupitila mu Samariya. Atafika pafupi na mzinda wa Sukari, Yesu anapumula pa citsime ca Yakobo, poyembekezela ophunzila ake amene analoŵa mu mzinda kuti akagule cakudya.
Yesu ali pa citsimepo, mzimayi wina anabwela kudzatapa madzi. Yesu anati kwa mzimayiyo: “Munipatseko madzi akumwa.” Koma iye anayankha kuti: ‘N’cifukwa ciani mukamba na ine? Ndine Msamariya ine. Ayuda sakambitsana na Asamariya.’ Koma Yesu anamuuza kuti: ‘Mukanadziŵa kuti ndine ndani, sembe mwanipempha madzi. Ndipo sembe nakupatsani madzi a moyo.’ Modabwa, mzimayiyo anafunsa kuti: ‘Mutanthauza ciani? Na cotapila mulibe.’ Yesu anati: ‘Aliyense amene angamwe madzi amene nidzam’patsa, sadzamvelanso njota.’ Pamenepo mzimayiyo anati: “Bambo, nipatsenkoni madzi amenewo.”
Yesu anamuuza kuti: ‘Kaitaneni amuna anu abwele kuno ku citsime.’ Koma mayiyo anati: ‘Nilibe mwamuna.’ Yesu anati: ‘Mwakamba zoona. Cifukwa munakwatiliwapo na amuna 5, ndipo amene mukhala naye pali pano si mwamuna wanu.’ Mzimayiyo anati: ‘Naona lomba kuti ndimwe mneneli. Ife Asamariya timakhulupilila kuti tiyenela kulambila Mulungu paphili ili. Koma Ayuda amati tiyenela kulambilila ku Yerusalemu cabe. Nikhulupilila kuti Mesiya akadzabwela, adzatiphunzitsa mmene tiyenela kulambilila.’ Ndiyeno Yesu anauza mzimayiyo zimene sanauzepo munthu wina aliyense. Iye anati: ‘Mesiyayo ndine amene.’
Mzimayiyo anathamangila mu mzinda na kuuza Asamariya kuti: ‘Niona kuti napeza Mesiya. Iye adziŵa zonse zokhudza ine. Tiyeni mukamuone!’ Anamulondola ku citsime kuja, ndipo anamvetsela pamene Yesu anali kuwaphunzitsa.
Asamariya anapempha Yesu kuti akhale mu mzinda wawo. Yesu anaphunzitsa anthu kwa masiku aŵili mu mzindawo, ndipo anthu ambili anakhulupilila mwa iye. Anthuwo anauza mzimayi wacisamariyayo kuti: ‘Pamene tamvetsela kwa munthu uyu, takhulupilila manje kuti alidi mpulumutsi wa dziko.’
“‘Bwela!’ Aliyense wakumva ludzu abwele. Aliyense amene akufuna, amwe madzi a moyo kwaulele.”—Chivumbulutso 22:17