NYIMBO 161
Ndimakondwera Kucita Cifuniro Canu
(Salimo 40:8)
1. Mwana wanu’a tabatizidwa,
Inu munam’limbikitsa.
Ndipo anali wokonzeka
Kuyenda m’coonadi.
Sanagonje pamayesero.
Iye analengeza
Dzina lanu kwa anthu onse.
Ndifuna kum’tsatira.
(KOLASI)
Ndimakondwera kucita
Cifuniro canu M’lungu.
Ndidzayenda m’coonadi
Ndi moyo wanga wonse.
Ndimakondwera kucita
Cifuniro canu M’lungu.
Cimwemweci ndi coona.
Ndili n’ciyembekezo.
Ndimakondwa.
2. Pamene ndinakudziwani
Ndinapezadi cimwemwe.
N’dzalengeza za dzina lanu
Inu Yehova M’lungu.
Kutumikira ndi abale,
Inde n’kosangalatsa.
Ndikupatsani zanga zonse
Pokutumikirani.
(KOLASI)
Ndimakondwera kucita
Cifuniro canu M’lungu.
Ndidzayenda m’coonadi
Ndi moyo wanga wonse.
Ndimakondwera kucita
Cifuniro canu M’lungu.
Cimwemweci ndi coona.
Ndili n’ciyembekezo.
Ndimakondwa.
Ndimasangalala.
(Onaninso Sal. 40:3, 10.)