KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBO
Kodi n’zotheka kukhala ndi moyo wamuyaya?
Munthu woyamba, Adamu, anakhala ndi moyo kwa zaka zambili. Koma m’kupita kwa nthawi, anakalamba ndi kufa. Kuyambila nthawi imeneyo, anthu ayesa kucita zinthu zosiyana-siyana kuti asamakalambe. Komabe, palibe munthu amene anathawapo imfa. N’cifukwa ciani zili conco? Adamu anakalamba ndi kufa cifukwa cakuti anacimwa mwa kusamvela Mulungu. Ifenso timakalamba cifukwa cakuti tinatengela kwa Adamu ucimo ndi malipilo ake amene ndi imfa.—Ŵelengani Genesis 5:5; Aroma 5:12.
Kuti ife tidzakhale ndi moyo wamuyaya, tinafunikila munthu wina kutilipilila dipo. (Yobu 33:24, 25) Dipo ndi malipilo amene amalipilidwa kuti munthu amasulidwa, ndipo ife tinayenela kumasulidwa ku imfa. (Ekisodo 21:29, 30) Yesu analipila malipilo amenewo pamene anatifela.—Ŵelengani Yohane 3:16.
Kodi tiyenela kucita ciani kuti tikapeze moyo wamuyaya?
Si anthu onse amene adzaomboledwa ku ukapolo wa matenda ndi ukalamba. Anthu amene samvela Mulungu monga mmene Adamu anacitila, adzataya mwai wokhala ndi moyo. Anthu okha amene adzakhululukidwa macimo ao ndi amene adzakhala ndi moyo wamuyaya.—Ŵelengani Yesaya 33:24; 35:3-6.
Kuti tikakhululukidwe macimo, tiyenela kucitapo kanthu. Tiyenela kudziŵa Mulungu mwa kuphunzila Mau ake, Baibo. Baibo imatiphunzitsa mmene tingakhalile ndi umoyo wabwino. Imatiphunzitsanso zimene tiyenela kucita kuti tikhale paubwenzi wabwino ndi Mulungu ndi kuti tidzakhale ndi moyo wamuyaya.—Ŵelengani Yohane 17:3; Machitidwe 3:19.
Kuti mudziŵe zambili, onani nkhani 3 m’buku ili, Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova
[Cithunzi papeji 32]
Kodi ndi makonzedwe otani amene angatimasule ku imfa?