KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBO
Kodi Mulungu amamva mapemphelo onse?
Anthu a mitundu yonse akamapemphela, Mulungu amamva. (Salimo 145:18, 19) Mau ake, Baibo, amatilimbikitsa kuti tiyenela kumuuza nkhani iliyonse imene imatidetsa nkhawa. (Afilipi 4:6, 7) Komabe, Mulungu sasangalala ndi mapemphelo ena. Mwacitsanzo, iye sasangalala ndi mapemphelo obweleza-bweleza ndi oloweza pamtima.—Ŵelengani Mateyu 6:7.
Ndiponso Yehova sakondwela ndi mapemphelo a anthu amene amanyalanyaza malamulo ake mwadala. (Miyambo 28:9) Mwacitsanzo, m’nthawi za Baibo, Mulungu anakana kumvela mapemphelo a Aisiraeli amene anali ndi mlandu wakupha anthu. Zimenezi zionetsa bwino kuti pali zinthu zina zimene tiyenela kucita kuti Mulungu amve mapemphelo athu.—Ŵelengani Yesaya 1:15.
Kodi tiyenela kucita ciani kuti Mulungu amve mapemphelo athu?
N’zosatheka kufikila Mulungu m’pemphelo ngati tilibe cikhulupililo. (Yakobo 1:5, 6) Tiyenela kukhulupilila kuti iye aliko ndipo amasamala za ife. Tingalimbitse cikhulupililo cathu mwa kuphunzila Baibo. Tikutelo cifukwa cakuti munthu amafunika kukhala ndi umboni wotsimikizilika wocokela m’Mau a Mulungu kuti akhale ndi cikhululupililo ceni-ceni.—Ŵelengani Aheberi 11:1, 6.
Tiyenela kupemphela mocokela pansi pa mtima ndi modzicepetsa. Ngakhale Mwana wa Mulungu, Yesu, anali kudzicepetsa popemphela. (Luka 22:41, 42) Conco, m’malo mouza Mulungu zocita, tiyenela kuyesetsa kumvetsetsa zimene iye amafuna mwa kuphunzila Baibo. Mwakutelo tidzapemphela mogwilizana ndi cifunilo ca Mulungu.—Ŵelengani 1 Yohane 5:14.