LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w13 10/1 tsa. 6
  • “Ifetu Tapeza Mesiya”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Ifetu Tapeza Mesiya”
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Yesu Kristu Ndani?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Kodi Yesu Khiristu N’ndani?
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Kodi Yesu Ndani?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
w13 10/1 tsa. 6

“Ifetu Tapeza Mesiya”

Pambuyo pa zaka 400 kucokela pamene buku lomalizila la Malemba aciheberi a m’Baibo linalembedwa, Yesu anabadwa ku Betelehemu. Izi zinakwanilitsa ulosi wa Mika wonena za Mesiya. Mu 29 C.E, patapita zaka pafupi-fupi 30 kucokela pamene Yesu anabadwa, mbali yoyamba ya ulosi wa Danieli wokamba za kubwela kwa Mesiya inakwanilitsidwa. Yesu anabatizika, ndipo Mulungu anamudzoza ndi mzimu woyela. Mesiya, amene anthu anali kumuyembekezela kwa nthawi yaitali anafika panthawi yake yoyenela. Ameneyo ndiye anali Mbeu yolonjezedwa.

Mwamsanga Yesu anayamba utumiki wake ndipo anali “kulengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu.” (Luka 8:1) Mogwilizana ndi mmene ulosi unanenela, Yesu anali wokoma mtima, wofatsa ndi woganizila ena. Zimene anali kuphunzitsa zinali zothandiza ndipo zinaonetsa kuti anali kukonda anthu. Komanso anali kucilitsa anthu amene anali ndi ‘zofooka za mtundu uliwonse,’ kuonetsa kuti Mulungu anali kumutsogolela. (Mateyu 4:23) Akulu ndi ana anakhamukila kwa Yesu. Iwo ayenela kuti anakamba monga mmene anakambila mmodzi mwa ophunzila ake kuti: “Ifetu tapeza Mesiya.”—Yohane 1:41.

Yesu anakambilatu kuti Ufumu wake ukatsala pang’ono kuyamba kulamulila, padziko padzakhala nkhondo, zivomezi, ndi mavuto ena ambili. Iye analimbikitsa onse ‘kukhala maso.’—Maliko 13:37.

Yesu anali munthu wangwilo ndi wokhulupilika kwa Mulungu, koma adani ake anamupha. Conco, imfa yake inali nsembe imene imatipatsa ciyembekezo codzakhala ndi moyo wosatha m’Paladaiso umene Adamu ndi Hava anataya.

Yesu anafa ndi kuukitsidwa ndi Mulungu pambuyo pa masiku atatu monga colengedwa cauzimu camphamvu. Izi zinakwanilitsa ulosi. Kenako Yesu anaonekela kwa ophunzila ake oposa 500. Asanapite kumwamba, Yesu analamula otsatila ake kulengeza uthenga wabwino wonena za iye ndi Ufumu wake kwa “anthu a mitundu yonse.” (Mateyu 28:19) Kodi io anagwila nchito imeneyi kufika pati?

—Yazikidwa pa Mateyu, Maliko, Luka, Yohane, 1 Akorinto.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani