KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO
Kodi dziko lapansi linapangidwa n’colinga canji?
Dziko lapansi linapangidwa moyenelela kuti pakhale zamoyo. Lili ndi madzi oculuka amene ndi ofunika ku moyo. Kupendekeka kwa dziko ndi kayendedwe kake zimacitika pa mlingo woyenela kuti nyanja zisazizizila kwambili kapena kuphwila. Mlengalenga ndi mphamvu yokoka ya dziko zimateteza kuti kutentha kovulaza kwa dzuŵa kusaononge dziko. Zomela ndi nyama padziko lapansi zimadalilana. Kudalilana kumeneko ndi kocititsa cidwi kwambili. Conco, anthu ambili amakhulupilila kuti dziko lathu linapangidwa ndi colinga.—Ŵelengani Yesaya 45:18.
Koma, mungadzifunse kuti, ‘Kodi kuvutika ndi cisalungamo zinali mbali ya colingaco?’—Ŵelengani Deuteronomo 32:4, 5.
Kodi colinga ca dziko lapansi cidzakwanilitsika?
Dziko lapansi linapangidwa kuti likhale malo abwino okhalamo anthu amene amalemekezana ndi kukonda Mlengi wao. Conco, anthu ndi ofunika kwambili kuposa zomela kapena nyama. Timadziŵa mmene Mlengi wathu alili, timakhudzika mtima ndi cikondi ndi cilungamo cake, ndipo timam’sanzila.—Ŵelengani Mlaliki 12:13; Mika 6:8.
Mlengi wathu adzakwanilitsa zonse zimene akufuna kucita. Conco, tili ndi cidalilo cakuti adzacotsapo kuvutika ndi cisalungamo. Ndipo adzapanga dziko lapansi kukhala malo abwino okhalamo anthu.—Ŵelengani Salimo 37:11, 29; Yesaya 55:11.