LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w15 1/1 tsa. 13
  • Kodi Mudziŵa?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mudziŵa?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Nkhani Zofanana
  • Kuthandiza Abale a Kristu Mokhulupilika
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 1/1 tsa. 13

Kodi Mudziŵa?

Malinga ndi mmene Baibulo limanenela, kodi liu lakuti “nduna” limatanthauza ciani?

Cifanizilo cogoba ca nduna ya Asuri

Cifanizilo cogoba ca ku asuri ca nduna

Nthawi zina liu limeneli linali kunena za mwamuna amene ndi wofulidwa. M’nthawi za Baibulo, amuna ena anali kufulidwa monga mbali ya cilango, ndipo ena anali kufulidwa akagwilidwa monga akapolo. Komanso amuna ofulidwa anali kuyang’anila akazi a mfumu ku nyumba zacifumu. Mwacitsanzo, Hegai ndi Sesigazi amene anali kulondela akazi ndi adzakazi a mfumu Ahasiwelo, yemwe amaganizilidwa kuti anali Sasita woyamba, anali ofulidwa.—Esitere 2:3, 14.

Komabe, sikuti onse amene amachulidwa m’Baibulo kuti nduna anali ofulidwa. Akatswili ena amanena kuti liu limeneli linali kugwilanso nchito kwa anthu a udindo waukulu m’nyumba ya mfumu. Liu lakuti nduna linagwilitsidwa nchito kwa Ebedimeleki, mnzake wa Yeremiya, ndi kwa mdindo wina wa ku Itiyopiya amene analalikidwa ndi mlaliki Filipo. Zikuoneka kuti Ebedimeleki anali ndi udindo waukulu cifukwa anali kulankhula mwacindunji ndi Mfumu Zedekiya. (Yeremiya 38:7, 8) Ndipo Mwiitiyopiya akufotokozedwa kuti anali woyang’anila cuma. Iye “anapita ku Yerusalemu kukapembedza Mulungu.”—Machitidwe 8:27.

N’cifukwa ciani abusa a m’nthawi ya Baibulo anali kulekanitsa nkhosa ndi mbuzi?

M’busa ali ndi nkhosa

Yesu pofotokoza za ciweluzo ca mtsogolo anati: “Mwana wa munthu akadzafika mu ulemelelo wake, . . . adzalekanitsa anthu mmene m’busa amalekanitsila nkhosa ndi mbuzi.” (Mateyu 25:​31, 32) N’cifukwa ciani abusa akale anali kulekanitsa nyama zimenezi?

Nthawi zonse nkhosa ndi mbuzi anali kuziŵeta ndi kuzidyetsela pamodzi nthawi ya masana. Koma usiku anali kuzitsekela m’khola pofuna kuziteteza ku zilombo zolusa, ku akawalala, ndiponso kuti zikhale mothuma. (Genesis 30:​32, 33; 31:​38-​40) Mitundu iŵiliyi ya ziweto inali kutsekeledwa m’makola osiyana ndi colinga cakuti ateteze nkhosa zofatsa, zazikazi, ndi zimene zili ndi tuŵana, kuti zisapwetekedwe ndi mbuzi zazikali. Buku lakuti All Things in the Bible linati: Abusa anali kulekanitsanso nkhosa pa nthawi ya “kubeleka, kuyamwitsa, ndi kumeta ubweya.” Yesu anagwilitsila nchito fanizo limeneli cifukwa abusa ndiponso ziweto zinali zinthu zimene anthu a ku Isiraeli wakale anali kuzidziŵa bwino.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani