LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w15 8/15 masa. 31-32
  • “Yehova Wakubweletsani Kuno ku France kuti Muphunzile Coonadi”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Yehova Wakubweletsani Kuno ku France kuti Muphunzile Coonadi”
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 8/15 masa. 31-32

ZA M’NKHOKWE YATHU

“Yehova Wakubweletsani Kuno ku France kuti Muphunzile Coonadi”

PAMENE Antoine Skalecki anali wacinyamata, nthawi zambili anali kukonda kukhala ndi hachi. Iye pamodzi ndi hachiyo anali kuyenda pang’onopang’ono m’migodi yamdima atanyamula miyala ya malasha kucotsa pansi mamita 500. Atate ake a Antoine anali atavulazidwa pamene m’godi unawadilikila, conco banja silikanacitila mwina koma kuuza Antoine kukagwila nchito yakalavulagaga maola 9 pa tsiku. Patsiku lina Antoine anatsala pang’ono kufa atatsekeledwa ndi cimwala.

1. Zida zimene ogwila nchito ku migodi ya ku Poland anali kugwilitsila nchito; 2. M’godi wa Dechy, pafupi ndi Sin-le-Noble, ku France

Zida zimene ogwila nchito ku migodi ya ku Poland ndi ya ku Dechy pafupi ndi Sin-le-Noble amaseŵenzetsa, ndipo ndi kumene Antoine Skalecki anali kuseŵenza.

Antoine ndi mmodzi wa ana amene anabadwa kwa anthu a ku Poland ca m’ma 1920 ndi 1930. N’cifukwa ciani anthu a ku Poland anasamukila ku France? Pamene dziko la Poland linabwezeletsa ufulu wake pambuyo pa Nkhondo Yoyamba ya Padziko Lonse, anthu m’dzikolo anaculuka kwambili. Anthu oposa wani miliyoni anali atafa pankhondo m’dziko la France. Conco kunali kufunikila anthu ambili ogwila nchito m’migodi ya malasha. Mu September 1919, dziko la France ndi la Poland linasainilana cikalata colola anthu a ku Poland kusamukila ku France. Pofika mu 1931 ciŵelengelo ca anthu a ku Poland m’dziko la France cinali 507,800, ndipo ambili anakakhala kumalo amigodi kumpoto kwa dzikoli.

Anthu ocokela ku Poland anali kugwila nchito mwakhama. Iwo anali kutsatilabe cikhalidwe ca kwao, ngakhale pankhani ya cipembedzo. Antoine amene tsopano ali ndi zaka 90, anati: “Agogo anga a Joseph akamafotokoza Malemba Oyela, anali kuwalemekeza kwambili cifukwa ndi zimene atate ao anawaphunzitsa. Pa Sondo, anthu a ku Poland amene anali kugwila nchito kumigodi anali kuvala zovala zabwino popita ku chalichi monga mmene anali kucitila kwao. Cifukwa ca ici anthu ena a ku France anali kuwasuliza.

Kudela lina lochedwa Nord-Pas-de-Calais anthu ambili a Cipolishi anakumana koyamba ndi Ophunzila Baibulo amene anali kulalikila mwakhama kumeneko kuyambila mu 1904. Pofika mu 1915, Nsanja ya Mlonda inayamba kusindikizidwa mu Cipolishi mwezi uliwonse, ndipo The Golden Age (tsopano imachedwa Galamukani) inayamba kupezeka m’cineneloco mu 1925. Anthu ambili anacita cidwi ndi zinthu za m’Malemba zimene zinali kupezeka m’magaziniwo kuphatikizapo m’buku lochedwa Zeze wa Mulungu la m’Cipolishi.

Banja la Antoine linadziŵa za Ophunzila Baibulo kudzela mwa amalume ake amene anapezeka koyamba ku msonkhano mu 1924. M’caka cimeneci Ophunzila Baibulo anakhala ndi msonkhano wao woyamba m’Cipolishi kudela lochedwa Bruay-en-Artois. Patapita milungu yocepa, M’bale Joseph F. Rutherford woimila likulu lathu anacititsa msonkhano m’dela limenelo ndipo kunapezeka anthu 2,000. M’bale Joseph F. Rutherford ataona kuti ambili amene analipo anali anthu a ku Poland anakhudzidwa kwambili cakuti anawauza kuti: “Yehova wakubweletsani kuno ku France kuti muphunzile coonadi. Conco inu ndi ana anu muphunzitseko anthu a Cifulenci. Nchito yolalikila ndi yaikulu ndipo ifunika kucitidwabe. Yehova adzacititsa kuti pakhale ofalitsa ena kuti agwile nchitoyo.”

Ndipo Yehova Mulungu anacitadi zimenezo. Akristu acipolishi amenewa anali akhama polalikila monga mmene anali kucitila khama panchito ya ku migodi. Ena a io anabwelela kwao ku Poland kukaphunzitsako ena coonadi camtengo wapatali cimene anaphunzila. Pakati pa anthu amene anacoka ku France kupita ku Poland kukalalikila uthenga wabwino m’mizinda ikuluikulu, panali Teofil, Piaskowski, Szczepan, Kosiak, ndi Jan Zabuda.

Koma alengezi ena a ku Poland anatsala ku France ndipo anapitiliza kulalikila mwakhama pamodzi ndi abale ndiponso alongo a ku France. Pamsonkhano umene unacitika ku Sin-le-Noble mu 1926, anthu 1,000 anapezeka pa mapulogilamu a Cipolishi, ndipo 300 anapezeka pa ya Cifulenci. Buku Lapacaka yacingelezi ya mu 1929 linati: M’caka cimeneco, anthu 332 a ku Poland anaonetsa poyela kudzipeleka kwao mwa kubatizidwa.” Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse isanayambe, pa mipingo 84 imene inali ku France 32, inali ya anthu okamba Cipolishi.

Mu 1947 Mboni za Yehova zambili zinabwelela ku Poland zitapemphedwa ndi boma. Ngakhale pambuyo pakuti io abwelela, nchito yabwino imene io ndi anthu ena a Cifulenci anacita inabala zipatso zabwino. Caka cimeneco ciŵelengelo ca ofalitsa Ufumu cinaculuka ndi 10 peresenti. Ndipo kuyambila mu 1948 kufika mu 1950 ciŵelengeloco cinali kuonjezeka kufika pa 20 ndi 23, mpaka pa 40 peresenti. Pofuna kuthandiza ofalitsa atsopanowa nthambi ya ku France inasankha oyang’anila oyendela oyamba mu 1948. Oyang’anila amene anasankhidwa anali okwana 5 ndipo mmodzi wa io anali Antoine Skalecki.

Abale ndi alongo a ku Poland m’dziko la France akupita ku msonkhano

Abale ndi alongo a ku Poland m’dziko la France akupita ku msonkhano. Pa galimoto pali cikwangwani conena kuti: “Mboni za Yehova”

Mboni za Yehova zambili zimene zili ku France zikali ndi ziongo za atate ao akale amene anali kugwila nchito yolalikila ndiponso ya ku migodi mwa khama. Masiku anonso, anthu ambili amene anasamukila ku France akuphunzila coonadi. Mosasamala kanthu kuti alengezi a Ufumu amene anali ku France anabwelela kwao kapena anakhalilatu kumeneko, iwo akutsatila mwakhama citsanzo ca Olengeza Ufumu akale a ku Poland.—Za m’Nkhokwe Yathu ku France.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani