LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w15 11/1 tsa. 7
  • N’cifukwa ciani timalalikila?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • N’cifukwa ciani timalalikila?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Nkhani Zofanana
  • 12 Zolinga
    Galamuka!—2018
  • Tingapeze Kuti Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambili Onena za Umoyo?
    Tingapeze Kuti Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambili Onena za Umoyo?
  • Pemphani Thandizo Kuti Mumvetsetse Baibulo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
  • “Pitani Mukaphunzitse Anthu a Mitundu Yonse Kuti Akhale Ophunzila”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 11/1 tsa. 7
Mboni za Yehova ziŵili zakulalikila

N’cifukwa ciani timalalikila?

Timadziŵika ndi nchito yolalikila kunyumba ndi nyumba, pamalo amene pamapezeka anthu ambili ndi kulikonse kumene tapeza anthu. N’cifukwa ciani timagwila nchito imeneyi?

Mboni za Yehova zimalalikila n’colinga cotamanda Mulungu ndi kudziŵitsa anthu dzina lake. (Aheberi 13:15) Timafunanso kumvela lamulo la Kristu Yesu lakuti: “Conco pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse, . . . ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulilani.”—Mateyu 28:19, 20.

Kuonjezela apo, timakonda anzathu. (Mateyu 22:39) Timadziŵa kuti anthu ambili ali ndi zipembedzo zao ndipo timadziwanso kuti si anthu onse amene angalandile uthenga wathu. Ngakhale n’telo, timaona kuti ziphunzitso za m’Baibulo zimapulumutsa miyoyo ya anthu. N’cifukwa cake timapitiliza “mwakhama kuphunzitsa ndi kulengeza uthenga wabwino wonena za Kristu Yesu,” mmene anacitila Akristu oyambilila.—Machitidwe 5:41, 42.

Katswili wa cikhalidwe dzina lake Antonio Cova Maduro analemba za Mboni za Yehova kuti “pogwila nchito yolalikila zimakumana ndi mavuto ndipo zimalema kwambili. Koma zimapitiliza kugwila nchitoyi kuti uthenga wopatulika ufalikile padziko lonse lapansi.”—El Universal Nyuzipepala ya Venezuela

Anthu ambili amene amaŵelenga mabuku athu si a Mboni za Yehova. Ndipo anthu mamiliyoni amene amaphunzila nafe Baibulo ali ndi zipembedzo zao. Iwo amayamikila kuti Mboni za Yehova zimawafikila panyumba zao.

Mwina mungakhale ndi mafunso ena okhudza Mboni za Yehova. Kuti mupeze mayankho ake, tikupemphani kuti,

  • Mufunse mmodzi wa Mboni za Yehova.

  • Mupite pa webusaiti yathu ya www.jw.org.

  • Mukabwele ku misonkhano yathu, sitilipilitsa.

Yesu akutuma ophunzila ake aŵili kukalalikila
Phili lokutidwa ndi cipale cofewa

Kuti mudziŵe zambili zokhudza Mboni za Yehova, onelelani vidiyo yakuti Mboni za Yehova—Gulu limene Limalikila Uthenga Wabwino, pa www.jw.org. (Onani polemba kuti MABUKU > MAVIDIYO)

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani