LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp16 na. 1 tsa. 3
  • N’cifukwa Ciani Tifunika Kumvetsetsa Baibulo?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • N’cifukwa Ciani Tifunika Kumvetsetsa Baibulo?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
  • Nkhani Zofanana
  • Buku Losavuta Kumvetsetsa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
  • Pindulani Mokwanila ndi Cakudya Cakuuzimu Cimene Yehova Amapeleka
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibulo?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kodi Uthenga Wabwino Ni Wocokeladi kwa Mulungu?
    Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
wp16 na. 1 tsa. 3

Nkhani Ya Pacikuto

N’cifukwa Ciani Tifunika Kumvetsetsa Baibulo?

“Baibulo ndi buku la cipembedzo lodziŵika kwambili. Koma kwa anthu a Cichainizi ndi buku lacilendo ndipo n’losathandiza.”​—LIN, CHINA.

“Sindimvetsetsa mabuku oyela acipembedzo canga ca Cihindu. Ndiye ndingakwanitse bwanji kumvetsetsa Baibulo Lopatulika?”​—AMIT, INDIA.

“Ndimalemekeza Baibulo cifukwa ndi buku lakale, ndipo ndamva kuti anthu amaligula kwambili. Koma sindinalionepo.”​—YUMIKO, JAPAN.

Anthu ambili padziko lonse amalemekeza kwambili Baibulo. Ngakhale n’conco, io amadziŵa nkhani zocepa za m’Baibulo mwinanso sazidziŵa n’komwe. Mfundo imeneyi ndi yoona. Mwacitsanzo, anthu mamiliyoni a ku Asia sadziŵa zimene Baibulo limakamba. N’cimodzimodzinso ndi anthu ambili a m’maiko amene Baibulo ndi lofala kwambili.

Mkazi aŵelenga Baibulo

Mwina mungadzifunse kuti: N’cifukwa ciani ndifunika kumvetsetsa Baibulo? Kumvetsetsa buku lopatulika limeneli, kudzakuthandizani kucita zotsatilazi:

  • Kukhala wokhutila ndi wacimwemwe

  • Kulimbana ndi mavuto a m’banja

  • Kulimbana ndi nkhawa za paumoyo

  • Kukhala bwino ndi anthu ena

  • Kuseŵenzetsa ndalama mwanzelu

Mwacitsanzo, mvelani zimene Yoshiko wa ku Japan anakamba. Iye sanali kudziŵa zimene Baibulo limakamba. Conco, anaganiza zoyamba kuliŵelenga. Nanga panali zotsatilapo zotani? Iye anakamba kuti: “Baibulo landithandiza kukhala ndi umoyo waphindu ndi kukhala ndi ciyembekezo cabwino ca mtsogolo. Tsopano ndili ndi umoyo wokhutilitsa.” Amit amene tamuchula kuciyambi kwa nkhani ino, nayenso anayamba kuphunzila Baibulo payekha. Iye anati: “Ndinadabwa kwambili ndi uthenga wa m’Baibulo. M’bukuli, muli mfundo zothandiza kwa munthu aliyense.”

Baibulo lathandiza anthu ambili kusintha umoyo wao. Bwanji osaliŵelenga ndi kuona mmene lingakuthandizileni inuyo panokha?

A Satisfying Life​—How to Attain It

Kuti mudziŵe zambili za mmene Baibulo lingakuthandizileni, onani kabuku kakuti A Satisfying Life​—How to Attain It, kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Kapezekanso pa www.jw.org

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani