LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp17 na. 3 tsa. 9
  • Umboni Winanso

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Umboni Winanso
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Nkhani Zofanana
  • Kudalila Thandizo La Mulungu
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
wp17 na. 3 tsa. 9
Colembepo cadothi cimene panalembedwa dzina lakuti Tattannu

Dzina lakuti “Tattannu” linalembedwa ku mbali imodzi ya colembapo ici cadothi

Umboni Winanso

Kodi pali umboni wa zinthu zakale wotsimikizila nkhani za m’Baibo? Nkhani ina m’magazini yakuti Biblical Archaeology Review ya mu 2014, inayankha funso yakuti: “Ni anthu angati ochulidwa m’Malemba Aciheberi amene umboni wa zinthu zakale watsimikizila kuti analiko?” Yankho inali yakuti: “Ni anthu pafupi-fupi 50!” Munthu mmodzi amene sanachulidwe m’nkhaniyo anali Tatenai. Kodi iye anali ndani? Tiyeni tikambilane za udindo wake wochulidwa m’Baibo.

Panthawi ina, Yerusalemu anali mbali ya Ufumu waukulu wa Perisiya. Mzindawu unali m’dela limene Aperisiya anali kulicha kuti Tsidya Lina la Mtsinje, kutanthauza kumadzulo kwa Firate. Aperisiya atagonjetsa mzinda wa Babulo, anamasula Ayuda mu ukapolo na kuwalamula kuti akamangenso kacisi wa Yehova ku Yerusalemu. (Ezara 1:1-4) Koma adani a Ayuda anafuna kulepheletsa nchito yomangayo, ndipo inakhala cifukwa cowapatsila mlandu wopandukila ufumu wa Perisiya. (Ezara 4:4-16) Mu ulamulilo wa Dariyo Woyamba (522-486 B.C.E.), nduna yaciperisiya dzina lake Tatenai, anapita kukafufuza za nkhaniyo. Baibo imamucha kuti “bwanamkubwa wa kutsidya lina la Mtsinje.”—Ezara 5:3-7.

Masiku ano, pali zolembapo zadothi zingapo zakale zimene panalembedwa dzina lakuti Tatenai. Zolembapo zimenezo ziyenela kuti zinali mbali ya mabuku ofotokoza mbili yakale yokhudza banja lake. Cimodzi mwa zolembazo, cimene papezeka dzina la munthu wochulidwa m’Baibo, ni kalata ya pangano la zamalonda imene inalembedwa mu 502 B.C.E., caka ca 20 ca ulamulilo wa Dariyo Woyamba. Kalatayi imakamba kuti amene anali mboni m’pangano la zamalonda limeneli anali mtumiki wa “Tattannu, bwanamkubwa wa Kutsidya Lina la Mtsinje.” Tattannu ndiye Tatenai wochulidwa m’buku ya m’Baibo ya Ezara.

Kodi munthu ameneyu anali na udindo wanji? Mu 535 B.C.E., Koresi Wamkulu anagaŵanso madela amene anali kulamulila kukhala zigawo-zigawo. Cimodzi mwa zigawozo cinali kuchedwa kuti “Babulo ndi Tsidya Lina la Mtsinje.” M’kupita kwa nthawi, cigawoci anacigaŵanso m’mbali ziŵili. Mbali imodzi inali kuchedwa kuti Tsidya la Mtsinje, ndipo inaphatikizapo Kole-Suriya, Foinike, Samariya, ndi Yuda. Zioneka kuti Damasiko ndiye linali likuku la cigawo cimeneci. Tatenai analamulila cigawoci kucokela ca m’ma 520 mpaka 502 B.C.E.

Pambuyo pakuti Tatenai wabwelako ku Yerusalemu kumene anakafufuza za mlandu wa Ayuda, iye anapeleka lipoti kwa Dariyo kuti Ayuda anakamba kuti Koresi ndiye anawalamula kumanganso kacisi wa Yehova. Atafufuza m’mabuku ofotokoza mbili yakale a m’nyumba yacifumu, anapeza umboni wakuti zimene Ayuda anakamba zinali zoona. (Ezara 5:6, 7, 11-13; 6:1-3) Conco, Tatenai analamulidwa kuti asawasokoneze, ndipo anamvela.—Ezara 6:6, 7, 13.

Kukamba zoona, “Tatenai bwanamkubwa wa kutsidya lina la Mtsinje,” sanacite zambili. Ngakhale n’conco, Malemba amakambako za iye, ndipo amam’chula na dzina laudindo loyenelela. Izi zimatipatsa umboni wina wakuti zinthu zakale zofukulidwa m’mabwinja zimaonetsa kuti Baibo n’lolondola ponena za mbili yakale.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani