Kodi Baibo Imati Ciani pa Nkhani ya Moyo na Imfa?
Na. 4 2017
© 2017 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
Magazini ino si yogulitsa. Colinga cake ni kuthandiza pa nchito yophunzitsa Baibo imene ikucitika padziko lonse lapansi. Zopeleka zaufulu n’zimene zimathandiza kupititsa patsogolo nchito imeneyi.
Kuti mucite copeleka, yendani pa webusaiti ya www.jw.org.
Baibo imene taseŵenzetsa ni Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika kusiyapo ngati taonetsa ina.
MAGAZINI ya Nsanja ya Mlonda, imalemekeza Yehova Mulungu, amene ni Wolamulila wa cilengedwe conse. Imalimbikitsa anthu ndi uthenga wabwino wakuti posacedwa, Ufumu wa Mulungu udzacotsa zoipa zonse na kusintha dziko lapansi kukhala paradaiso. Imalimbikitsa anthu kukhulupilila Yesu Khristu amene anatifela kuti tikapeze moyo wosatha, ndipo panthawi ino iye akulamulila monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Magaziniyi yakhala ikufalitsidwa kuyambila mu 1879 ndipo si yandale. Mfundo zake zonse n’zocokela m’Baibo.