Zamkati
WIKI YA OCTOBER 23-29, 2017
3 Phunzilani Kukhala Wodziletsa
Yehova wapeleka citsanzo cabwino koposa ca kudziletsa. Kodi ise anthu tingatengele bwanji citsanzo cake? Nanga n’ciani cimene tingacite kuti tikhale odziletsa kwambili?
WIKI YA OCTOBER 30, 2017–NOVEMBER 5, 2017
8 Tengelani Khalidwe la Yehova la Cifundo
Kodi kukhala wacifundo kumatanthauza ciani? Yehova na Yesu apeleka citsanzo cabwino kwambili pankhani yoonetsa khalidwe la cifundo. Koma kodi n’zinthu ziti zimene tingacite potengela citsanzo cawo? Nanga tidzapeza madalitso anji tikacita zimenezo?
13 Mbili Yanga—Nakhala na Mwayi Wotumikila Pamodzi ndi Amuna Auzimu
WIKI YA NOVEMBER 6-12, 2017
18 “Mau a Mulungu Wathu Adzakhala Mpaka Kalekale”
WIKI YA NOVEMBER 13-19, 2017
23 “Mau a Mulungu . . . Ndi Amphamvu”
N’cifukwa ciani n’zocititsa cidwi kuti Baibo ikupitiliza kupezeka m’zitundu zambili? Nanga tingaonetse bwanji kuti timayamikila kukhala na Mau a Mulungu m’citundu cimene timamvetsetsa? Nkhani ziŵilizi zidzatithandiza kuti tiziyamikila kwambili Baibo. Zidzatithandizanso kuti tizikonda kwambili Mlembi wake.
WIKI YA NOVEMBER 20-26, 2017
28 ‘Limba Mtima, Ugwile Nchito Mwamphamvu’
Kulimba mtima ndi khalidwe lofunika ngako kwa Akhristu. Kodi zitsanzo za anthu akale amene anacita zinthu molimba mtima zingatipindulitse bwanji? Kodi acicepele, makolo, alongo acikulile, ndi abale obatizika angaonetse bwanji kuti ni olimba mtima ndi kuti ni okonzeka kugwila nchito zabwino?