LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp18 na. 1 tsa. 3
  • Kodi Malangizo a m’Baibo Akali Othandiza Masiku Ano?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Malangizo a m’Baibo Akali Othandiza Masiku Ano?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2018
  • Nkhani Zofanana
  • Mau oyamba
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2018
  • Baibo Ni Gwelo la Malangizo Odalilika
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila) —2024
  • Mau Oyamba
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Musaleke Kutsatila Citsogozo ca Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2018
wp18 na. 1 tsa. 3
Munthu woyenda kuthambo, ndeke, wasayansi, banja, komanso mwamuna aŵelenga Baibo

Kodi Malangizo a m’Baibo Akali Othandiza Masiku Ano?

ENA AMAKAMBA KUTI IYAYI. Dokota wina anati kuseŵenzetsa malangizo a m’Baibo kuli monga kuseŵenzetsa buku la m’ma 1920 pophunzitsa ana a sukulu za sayansi. Munthu wokaikila Baibo angakufunseni kuti, Kodi mungaseŵenzetse kabuku ka malangizo a kompyuta yacikale-kale, kuti mudziŵe moseŵenzetsela kompyuta yamakono? M’mau ena anthu ena amaona kuti Baibo inathelatu nchito.

N’cifukwa ciani munthu angaseŵenzetse malangizo akale-kale amenewo pamene kuli cidziŵitso cambili-mbili ca panthawi yake m’dziko lamakono? Pali malangizo pamawebusaiti ambili-mbili, alangizi ochuka pamapulogilamu apa TV, makambilano a akatswili odziŵa za maganizo a anthu, aphungu a zacikhalidwe, ndi akatswili olemba mabuku. M’mashopu ogulitsa mabuku mumapezeka mabuku ambili-mbili othandiza, ndipo ndalama madola ambili-mbili zimaonongedwa kupanga mabuku amenewa.

Poona malangizo onsewa a panthawi yake, kodi pangakhale cifukwa coŵelengela malangizo a m’Baibo, buku imene inalembedwa zaka pafupi-fupi 2,000 zapitazo? Malinga n’kunena kwa anthu osakhulupilila Baibo, kodi zingakhale zoona kuti kuseŵenzetsa malangizo a m’buku lakale limeneli kungakhale monga kuseŵenzetsa kabuku kacikale-kale ka malangizo pa za sayansi kapena a kompyuta? Kweni-kweni, citsanzo cimeneci n’cosayenelela. Za sayansi zimasintha mofulumila kwambili, koma kodi zofunikila za anthu pa umoyo zasintha? Anthu amafuna kukhala na umoyo waphindu, wacimwemwe ndi wotetezeka. Amafunanso kukhala ndi mabanja abwino, na mabwenzi abwino.

Ngakhale kuti Baibo ni buku lakale, imafotokoza mmene anthu angapezele zofunika zimenezi na zina pa umoyo wawo. Imakambanso kuti inauzilidwa na Mlengi wathu. Imapeleka malangizo okhudza mbali zonse za umoyo wathu na mmene tingacitile tikakumana na vuto iliyonse. (2 Timoteyo 3:16, 17) Koposa zonse Baibo ili na malangizo amene amathandiza nthawi zonse, malangizo amene sasila nchito. Baibo imati: “Mawu a Mulungu ndi amoyo.”—Aheberi 4:12.

Kodi zimene Baibo imakamba n’zoona? Kodi inasila nchito, kapena kodi ikali na malangizo othandiza kuposa mabuku ena onse? Kope ino ya magazini a Nsanja ya Mlonda, yoyamba pa makope apadela, idzakuthandizani kupeza mayankho pa mafunso amenewa.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani